Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Salimo 1:1-6

1  Wodala+ ndi munthu amene sayenda motsatira malangizo a anthu oipa,+ Saima m’njira ya anthu ochimwa,+ Ndipo sakhala pansi pamodzi ndi anthu onyoza.+   Koma amakondwera ndi chilamulo cha Yehova,+ Ndipo amawerenga ndi kusinkhasinkha chilamulo chake usana ndi usiku.+   Munthu ameneyo adzakhala ngati mtengo wobzalidwa m’mphepete mwa mitsinje ya madzi,+ Umene umabala zipatso m’nyengo yake,+ Umenenso masamba ake  safota,+ Ndipo zochita zake zonse zidzamuyendera bwino.+   Koma oipa sali choncho. Iwo ali ngati mankhusu* amene amauluzika ndi mphepo.+   N’chifukwa chake oipa adzatsutsidwa pa chiweruzo,+ Ndipo ochimwa sadzapezeka pagulu la olungama.+   Pakuti Yehova amadziwa njira za olungama,+ Koma oipa adzatheratu pamodzi ndi njira zawo.+

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.