Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Maliro 4:1-22

א [ʼA′leph] 4  Golide amene anali kuwala, golide wabwino, sakuwalanso.+ Miyala yopatulika*+ aikhuthulira m’misewu yonse.+ ב [Behth]   Ana okondedwa a Ziyoni+ amene anali amtengo wapatali ngati golide woyengeka bwino, Tsopano ayamba kuonedwa ngati mitsuko ikuluikulu yadothi, ntchito ya manja a munthu woumba mbiya.+ ג [Gi′mel]   Ngakhale mimbulu imapereka bere kwa ana ake kuti ayamwe. Koma mwana wamkazi wa anthu anga wakhala wankhanza+ ngati nthiwatiwa m’chipululu.+ ד [Da′leth]   Lilime la ana oyamwa lamamatira kummero chifukwa cha ludzu.+ Ana apempha chakudya+ koma palibe amene akuwapatsa.+ ה [Heʼ]   Anthu amene anali kudya zinthu zabwino adzidzimuka ndipo agwidwa ndi mantha m’misewu.+ Anthu amene akula akuvala zovala zamtengo wapatali*+ agona pamilu ya phulusa.+ ו [Waw]   Chilango chimene mwana wamkazi wa anthu anga walandira chifukwa cha zolakwa zake, n’chachikulu kuposa chimene mzinda wa Sodomu unalandira chifukwa cha machimo ake.+ Mzinda umenewu unawonongedwa mwadzidzidzi m’kanthawi kochepa, ndipo palibe dzanja limene linauthandiza.+ ז [Za′yin]   Anaziri+ ake anali oyera kuposa chipale chofewa.+ Analinso oyera kuposa mkaka. Ndipotu anali ofiira+ kuposa miyala yamtengo wapatali ya korali. Analinso osalala ngati mwala wa safiro.+ ח [Chehth]   Tsopano ayamba kuoneka akuda kuposa makala. Anthu sakuwazindikiranso mumsewu.+ Khungu lawo lafota moti lamamatira kumafupa awo.+ Langoti gwaa ngati mtengo. ט [Tehth]   Amene anaphedwa ndi lupanga+ aliko bwino kusiyana ndi amene anafa ndi njala,+ Pakuti amene anafa ndi njala anafooka chifukwa chosowa chakudya, ndipo anakhala ngati apyozedwa ndi lupanga. י [Yohdh] 10  Ngakhale amayi, amene amakhala achifundo, afika pophika ana awo ndi manja awo.+ Anawo akhala ngati chakudya chotonthoza anthu pa nthawi ya kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+ כ [Kaph] 11  Yehova wasonyeza ukali wake wonse.+ Wakhuthula mkwiyo wake woyaka moto.+ Iye wayatsa moto m’Ziyoni, umene wanyeketsa maziko ake.+ ל [La′medh] 12  Mafumu a padziko lapansi ndiponso anthu onse okhala panthaka ya dziko lapansi,+ Sanayembekezere kuti mdani angadzalowe pazipata za Yerusalemu.+ מ [Mem] 13  Zimenezi zinachitika chifukwa cha machimo a aneneri ake ndi zolakwa za ansembe ake,+ Amene anakhetsa magazi a anthu olungama a mumzindawo.+ נ [Nun] 14  Ansembe ndi aneneriwo akungoyendayenda mumsewu ngati anthu akhungu.+ Aipitsidwa ndi magazi,+ Moti palibe amene akukhudza zovala zawo.+ ס [Sa′mekh] 15  Anthu akuwafuulira kuti: “Chokani! Ndinu odetsedwa!+ Chokani! Chokani! Musatikhudze!”+ Ansembe ndi aneneriwo alibe pokhala+ ndipo akungoyendayenda.+ Anthu a mitundu ina akunena kuti: “Amenewa sapitiriza kukhala kuno.+ פ [Peʼ] 16  Yehova wawabalalitsa+ ndipo sadzawayang’ananso.+ Anthu sadzaganiziranso ansembe.+ Sadzachitiranso chifundo amuna okalamba.”+ ע [ʽA′yin] 17  Pamene tili ndi moyo, maso athu akulefuka chifukwa choyembekezera thandizo lomwe silikubwera.+ Pofunafuna thandizo, tadalira mtundu wa anthu amene sangabweretse chipulumutso.+ צ [Tsa·dheh′] 18  Akutisakasaka kulikonse kumene tikupita,+ moti palibe amene akuyenda m’mabwalo a mizinda yathu. Mapeto athu ayandikira. Masiku athu akwanira, pakuti mapeto athu afika.+ ק [Qohph] 19  Otithamangitsawo ndi aliwiro kuposa ziwombankhanga zouluka m’mwamba.+ Iwo atithamangitsa pamapiri.+ Atibisalira m’chipululu.+ ר [Rehsh] 20  Wodzozedwa wa Yehova,+ amene ndi mpweya wotuluka mphuno mwathu,+ wagwidwa m’dzenje lawo lalikulu.+ Ponena za ameneyu, ife tinati: “Tidzakhala mumthunzi wake+ pakati pa mitundu ya anthu.”+ ש [Sin] 21  Kondwa ndipo usangalale,+ iwe mwana wamkazi wa Edomu,+ amene ukukhala m’dziko la Uzi.+ Iwenso kapuyo ikupeza.+ Udzaledzera ndipo anthu adzakuona uli maliseche.+ ת [Taw] 22  Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, chilango chimene anakupatsa chifukwa cha zolakwa zako chatha.+ Sadzakutenganso kupita nawe ku ukapolo.+ Tsopano iwe mwana wamkazi wa Edomu, Mulungu watembenukira kwa iwe kuti aone zolakwa zako. Machimo ako wawaika poyera.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “miyala ya pamalo opatulika.”
Mawu ake enieni, “zovala zofiira,” kutanthauza zovala zofiira zamtengo wapatali.