Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Maliro 3:1-66

א [ʼA′leph] 3  Ine ndine mwamuna wamphamvu amene ndaona masautso+ chifukwa cha ndodo ya ukali wa Mulungu.   Iye wanditsogolera ndi kundiyendetsa m’malo amdima, osati m’malo owala.+   Ndithudi, iye amandimenya ndi dzanja lake mobwerezabwereza tsiku lonse.+ ב [Behth]   Wafooketsa thupi langa ndipo wachititsa khungu langa kunyala.+ Iye waphwanyanso mafupa anga.+   Wandimangira mpanda+ kuti chomera chakupha+ ndi mavuto zindizungulire.   Wandichititsa kukhala m’malo amdima,+ ngati munthu woti anafa kalekale.+ ג [Gi′mel]   Wanditsekereza ngati mmene mpanda wamiyala umatsekerezera, kuti ndisatuluke.+ Wandimanga ndi maunyolo olemera amkuwa.+   Komanso ndikalira ndi kupempha thandizo mofuula, iye amatsekereza pemphero+ langa.   Watsekereza njira zanga ndi miyala yosema.+ Wachititsa njira zanga kukhala zovuta kuyendamo.+ ד [Da′leth] 10  Kwa ine, iye ali ngati chimbalangondo chimene chandibisalira,+ ndiponso ngati mkango umene wakhala pamalo obisika.+ 11  Wasokoneza njira zanga ndipo wandichititsa kukhala wopanda chochita. Wandichititsanso kukhala wosiyidwa.+ 12  Wakunga uta wake+ ndipo wandisandutsa chinthu cholasapo mivi+ yake. ה [Heʼ] 13  Walasa impso zanga ndi mivi yotuluka m’kachikwama kake.+ 14  Ndakhala chinthu choseketsa+ kwa anthu onse odana nane, ndipo amandiimba m’nyimbo yawo tsiku lonse.+ 15  Wandipatsa zinthu zowawa zokwanira.+ Wandikhutitsa chitsamba chowawa.+ ו [Waw] 16  Wachititsa kuti mano anga aguluke ndi miyala.+ Wandipondaponda m’phulusa.+ 17  Inu mwanditayira kutali, moti sindilinso pa mtendere. Sindikukumbukiranso zinthu zabwino.+ 18  Nthawi zonse ndikunena kuti: “Ulemerero wanga ndi chiyembekezo changa mwa Yehova zatha.”+ ז [Za′yin] 19  Kumbukirani kuti ndine wosautsika ndi wosowa pokhala.+ Kumbukiraninso kuti ndimadya chitsamba chowawa ndi chomera chakupha.+ 20  Ndithu mudzandikumbukira ndi kundiweramira kuti mundithandize.+ 21  Ndidzakumbukira zimenezi mumtima mwanga.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima wodikira.+ ח [Chehth] 22  Chifukwa cha kukoma mtima kosatha+ kwa Yehova, ife sitinafafanizidwe,+ ndipo chifundo chake sichidzatha.+ 23  Chifundocho chimakhala chatsopano m’mawa uliwonse,+ pakuti inu ndinu wokhulupirika kwambiri.+ 24  Ine ndanena kuti: “Yehova ndiye cholowa changa.+ Pa chifukwa chimenechi, ndidzakhala ndi mtima womudikira.”+ ט [Tehth] 25  Yehova ndi wabwino kwa munthu amene akumuyembekezera,+ kwa munthu amene akumufunafuna.+ 26  Ndi bwino kuti munthu ayembekezere+ chipulumutso cha Yehova+ moleza mtima.+ 27  Ndi bwino kuti mwamuna wamphamvu anyamule goli ali mnyamata.+ י [Yohdh] 28  Iye akhale payekha ndipo akhale chete,+ chifukwa Mulungu walola kuti zimenezi zimuchitikire.+ 29  Iye awerame mpaka pakamwa pake pafike padothi.+ Mwina angakhale ndi chiyembekezo.+ 30  Aperekere tsaya lake kwa munthu amene akumumenya.+ Alandire chitonzo chokwanira.+ כ [Kaph] 31  Pakuti Yehova sadzatitaya mpaka kalekale.*+ 32  Ngakhale kuti watichititsa kumva chisoni,+ ndithu adzatichitira chifundo chifukwa kukoma mtima kwake kosatha n’kwakukulu.+ 33  Pakuti iye sasangalala ndi kusautsa anthu kapena kuwamvetsa chisoni.+ ל [La′medh] 34  Pajatu kupondaponda+ akaidi onse a padziko lapansi,+ 35  Kukankhira pambali chilungamo cha mwamuna wamphamvu pamaso pa Wam’mwambamwamba,+ 36  Ndi kupotoza chiweruzo cha munthu pa mlandu wake, Yehova savomereza zimenezi.+ מ [Mem] 37  Tsopano ndani ananenapo kuti chinthu chichitike, chinthucho n’kuchitikadi Yehova asanalamule?+ 38  Zinthu zoipa ndi zabwino sizitulukira limodzi pakamwa pa Wam’mwambamwamba.+ 39  Kodi munthu angadandaulirenji+ chifukwa cha zotsatirapo za tchimo lake?+ נ [Nun] 40  Tiyeni tifufuze njira zathu kuti tizidziwe,+ ndipo tibwerere kwa Yehova.+ 41  Tiyeni tichonderere Mulungu kumwamba ndi mtima wonse, ndipo tikweze manja athu m’mwamba+ ndi kunena kuti: 42  “Ife taphwanya malamulo. Tachita zinthu zopanduka+ ndipo inu simunatikhululukire.+ ס [Sa′mekh] 43  Mwadzitchinga ndi mkwiyo wanu kuti tisakufikireni+ ndipo mukupitiriza kutithamangitsa.+ Mwapha anthu mopanda chisoni.+ 44  Mwadzitchinga ndi mtambo waukulu+ kuti pemphero lisadutse ndi kufika kwa inu.+ 45  Mwatisandutsa nyansi ndi zinyalala pakati pa anthu a mitundu ina.”+ פ [Peʼ] 46  Pakamwa pa adani athu onse pakutinenera zoipa.+ 47  Ife tagwidwa ndi mantha ndipo tikusowa chochita.+ Tasiyidwa ndipo tawonongedwa.+ 48  Maso anga akungotuluka misozi ngati mtsinje chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.+ ע [ʽA′yin] 49  Maso anga akungotuluka misozi mosalekeza,+ 50  Kufikira Yehova atayang’ana pansi ndi kutiona ali kumwamba.+ 51  Mtima wanga ukusautsika ndi zimene maso anga aona,+ zimene zachitikira ana onse aakazi a mzinda wanga.*+ צ [Tsa·dheh′] 52  Adani anga akundisaka ngati mbalame+ popanda chifukwa.+ 53  Anali kufuna kuchotsa moyo wanga kuti andiponye m’dzenje+ ndipo anali kundiponya miyala. 54  Madzi asefukira ndi kumiza mutu wanga,+ moti ndanena kuti: “Ndifa basi!”+ ק [Qohph] 55  Inu Yehova, ndaitana dzina lanu mofuula ndili m’dzenje lakuya kwambiri.+ 56  Mumve mawu anga.+ Musatseke khutu lanu pamene ndikupempha mpumulo ndiponso pamene ndikulirira thandizo.+ 57  Pa tsiku limene ndinakuitanani,+ munandiyandikira ndi kundiuza kuti: “Usaope.”+ ר [Rehsh] 58  Inu Yehova, mwandiweruzira milandu yanga.+ Mwawombola moyo wanga.+ 59  Inu Yehova, mwaona zoipa zimene andichitira.+ Chonde, ndiweruzireni mlandu wanga.+ 60  Mwaona mtima wawo wokonda kubwezera ndiponso ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+ ש [Sin] kapena [Shin] 61  Inu Yehova, mwamva mawu awo otonza ndipo mwaona ziwembu zawo zonse zimene andikonzera.+ 62  Mwamva mawu ochokera pakamwa pa anthu amene akundiukira.+ Mwamvanso zoipa zimene akundinenera monong’ona tsiku lonse.+ 63  Onani zochita zawo zonse.+ Iwo akundiimba m’nyimbo yawo.+ ת [Taw] 64  Inu Yehova, mudzawabwezera mogwirizana ndi ntchito za manja awo.+ 65  Mudzaumitsa mtima wawo,+ ndipo kuchita zimenezi n’kuwatemberera.+ 66  Inu Yehova, mudzawakwiyira ndi kuwathamangitsa ndipo mudzawafafaniza+ padziko lanu lapansi.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “midzi yozungulira.”