Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Maliro 2:1-22

א [ʼAʹleph] 2  Chifukwa chokwiya, Yehova waphimba mwana wamkazi wa Ziyoni ndi mtambo+ wakuda. Iye waponya pansi chokongoletsera+ Isiraeli kuchokera kumwamba.+ Sanakumbukire chopondapo mapazi+ ake pa tsiku la mkwiyo wake. ב [Behth]   Yehova wameza malo okhala a Yakobo. Sanamvere chisoni malo ake alionse.+ Mu ukali wake, iye wagwetsa mipanda yolimba kwambiri+ ya mwana wamkazi wa Yuda. Waipitsa ufumu+ ndi akalonga+ ake ndipo wawagwetsera pansi.+ ג [Giʹmel]   Mu mkwiyo wake wathyola nyanga* iliyonse ya Isiraeli.+ Adani athu atatiukira, iye sanatithandize.+ Mkwiyo wake ukuyakirabe Yakobo ngati moto umene wawononga ponseponse.+ ד [Daʹleth]   Wakunga uta wake ngati mdani.+ Dzanja lake lamanja+ lakonzeka ngati la mdani,+ Ndipo wapitiriza kupha+ anthu onse ofunika kwambiri. Ukali wake waukhuthula ngati moto+ m’hema+ wa mwana wamkazi wa Ziyoni. ה [Heʼ]   Yehova wakhala ngati mdani.+ Wameza Isiraeli.+ Iye wameza nsanja zonse za Isiraeli zokhalamo.+ Wawononga malo ake otetezedwa ndiponso mipanda yolimba kwambiri.+ Wachititsa kuti kulira ndi maliro+ zimveke mumzinda wa mwana wamkazi wa Yuda. ו [Waw]   Iye wapasula chisimba*+ chake ngati chisimba cha m’munda+ ndipo wathetsa zikondwerero zake. Yehova wachititsa kuti zikondwerero+ ndi sabata ziiwalike mu Ziyoni, Ndipo mu mkwiyo wake waukulu wakana mfumu ndi wansembe.+ ז [Zaʹyin]   Yehova wataya guwa lake lansembe.+ Iye wanyoza malo ake opatulika.+ Wapereka m’manja mwa adani makoma* a nsanja zake zokhalamo.+ Iwo afuula m’nyumba ya Yehova ngati pa tsiku lachikondwerero.+ ח [Chehth]   Yehova waganiza zogwetsa mpanda+ wa mwana wamkazi wa Ziyoni. Watambasula chingwe choyezera.+ Sanabweze dzanja lake kuti lisabweretse chiwonongeko.+ Walilitsa+ chiunda chomenyerapo nkhondo ndi mpanda. Zonsezi zatha mphamvu. ט [Tehth]   Zipata+ zake zamira munthaka. Wawononga mipiringidzo yake ndipo waithyolathyola. Mfumu yake ndi akalonga ake ali pakati pa mitundu ina.+ Malamulo sakutsatiridwa.+ Aneneri ake sakuonanso masomphenya ochokera kwa Yehova.+ י [Yohdh] 10  Akuluakulu a mwana wamkazi wa Ziyoni akhala pansi ndipo akhala chete.+ Iwo athira fumbi pamitu+ yawo ndipo avala ziguduli.*+ Anamwali a Yerusalemu aweramitsa mitu yawo mpaka padothi.+ כ [Kaph] 11  Maso anga atopa ndi kulira.+ M’mimba mwanga mukubwadamuka.+ Chiwindi changa chakhuthulidwa+ pansi chifukwa cha kuwonongedwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga,+ Ndiponso chifukwa chakuti ana ndi makanda oyamwa akukomoka+ m’mabwalo a mzinda. ל [Laʹmedh] 12  Iwo anali kufunsa amayi awo kuti: “Kodi chakudya ndi vinyo zili kuti?”+ Anali kufunsa chifukwa anali kukomoka m’mabwalo a mzinda ndi kugona pansi ngati anthu ophedwa, Ndiponso chifukwa moyo wawo unali kukhuthukira pachifuwa cha amayi awo. מ [Mem] 13  Kodi ndikusonyeze umboni wotani? Kodi ndingakuyerekezere ndi chiyani, iwe mwana wamkazi wa Yerusalemu?+ Kodi ndikufananitse ndi chiyani kuti ndikutonthoze, namwali iwe, mwana wamkazi wa Ziyoni?+ Pakuti kuwonongeka+ kwako kwafalikira ngati kukula kwa nyanja. Ndani angakuchiritse?+ נ [Nun] 14  Aneneri ako aona masomphenya achabechabe ndi opanda pake+ onena za iwe. Iwo sanaulule zolakwa zako kuti akuteteze n’cholinga choti usatengedwe kupita ku ukapolo,+ Koma anali kuona masomphenya achabechabe ndi osocheretsa+ onena za iwe. ס [Saʹmekh] 15  Anthu onse odutsa mumsewu akakuona, akuwomba m’manja+ monyodola. Akuimba mluzu+ ndi kupukusa mitu+ yawo poona mwana wamkazi wa Yerusalemu. Iwo akunena kuti: “Kodi uwu ndi mzinda umene anali kunena kuti, ‘Ndi wokongola kwambiri, wotamandika padziko lonse lapansi’?”+ פ [Peʼ] 16  Adani ako onse akukutsegulira pakamwa.+ Akuimba mluzu ndi kukukukutira mano.+ Iwo akunena kuti: “Ameneyu timumeza.+ Ndithu, lero ndi tsiku limene takhala tikuyembekezera.+ Lafikadi! Taliona!”+ ע [ʽAʹyin] 17  Yehova wachita zimene anali kuganiza.+ Wakwaniritsa zimene ananena,+ Zimene analamula kalekale.+ Wapasula zinthu ndipo sanamve chisoni.+ Wachititsa adani ako kusangalala+ chifukwa cha zimene zakuchitikira. Wakweza nyanga ya adani+ ako. צ [Tsa·dhehʹ] 18  Mtima wa anthuwo wafuulira Yehova,+ iwe mpanda wa mwana wamkazi wa Ziyoni.+ Gwetsa misozi ngati mtsinje usana ndi usiku.+ Usapume. Mwana wa diso lako asaleke kulira. ק [Qohph] 19  Nyamuka! Lira mofuula usiku, pa nthawi yoyamba ulonda+ wam’mawa. Khuthula+ mtima wako pamaso+ pa Yehova ngati madzi. Pemphera utakweza manja+ ako kwa iye chifukwa cha ana ako, Amene akukomoka ndi njala m’misewu.+ ר [Rehsh] 20  Inu Yehova, yang’anani kuti muone+ yemwe mwamulanga chotere. Kodi amayi azidya zipatso za mimba yawo, ana awo athanzi?+ Kapena kodi wansembe ndi mneneri aziphedwa m’malo opatulika a Yehova?+ ש [Shin] 21  Anyamata ndi amuna okalamba+ agona pansi m’misewu.+ Anamwali anga ndi anyamata anga aphedwa ndi lupanga.+ Mwapha anthu pa tsiku la mkwiyo+ wanu. Onsewo mwawaphadi+ mopanda chisoni.+ ת [Taw] 22  Munaitana+ anthu kuchokera kumalo onse ozungulira, kumene akukhala monga alendo. Pa tsiku la mkwiyo wa Yehova panalibe wothawa kapena wopulumuka.+ Ana onse athanzi amene ndinabereka ndi kuwalera, mdani wanga anawapha.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa 1Sa 2:1.
Ena amati “khumbi,” kapena “chitala.”
Ena amati “zipupa,” kapena “zikupa.”
Ena amati “masaka.”