Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Maliro 1:1-22

א [ʼA′leph] 1  Amene anali ndi anthu ambiri+ tsopano wakhala wopanda anthu.+ Amene anali ndi anthu ambiri pakati pa mitundu ina+ wakhala ngati mkazi wamasiye.+ Amene anali wolemekezeka pakati pa zigawo zina wayamba kugwira ntchito yaukapolo.+ ב [Behth]   Iye akulira kwambiri usiku,+ ndipo misozi ikutsika pamasaya ake.+ Pakati pa onse amene anali kumukonda, palibe amene akumutonthoza.+ Anthu onse amene anali anzake amuchitira zachinyengo+ ndipo akhala adani ake.+ ג [Gi′mel]   Yuda wakhala kapolo chifukwa cha nsautso+ ndiponso chifukwa cha kukula kwa ntchito yaukapolo imene akugwira.+ Iye wakhala pakati pa mitundu ina ya anthu,+ ndipo sanapeze malo ampumulo. Onse amene anali kumuzunza amupeza pa nthawi ya mavuto ake.+ ד [Da′leth]   Njira zopita ku Ziyoni zikulira, chifukwa palibe amene akupita kuchikondwerero.+ Zipata zake zonse zasiyidwa.+ Ansembe+ ake akuusa moyo.* Anamwali ake agwidwa ndi chisoni,+ ndipo iyeyo akumva kuwawa mumtima. ה [Heʼ]   Adani ake akumulamulira.+ Anthu odana naye sakuda nkhawa.+ Yehova wamuchititsa kukhala wachisoni chifukwa cha kuchuluka kwa machimo+ ake, Ndipo ana ake ayenda patsogolo pa adani awo atagwidwa ukapolo.+ ו [Waw]   Ulemerero+ wonse wamuchokera mwana wamkazi wa Ziyoni. Akalonga ake akhala ngati mbawala zamphongo zimene zikusowa msipu.+ Iwo akuyenda mofooka+ pamaso pa wowazunza.* ז [Za′yin]   Yerusalemu anakumbukira zinthu zake zonse zabwino+ zimene anali nazo kuyambira kalekale. Anazikumbukira m’masiku a masautso ake ndi a anthu ake osowa pokhala. Anthu ake atagwidwa ndi adani, pamene iye analibe munthu womuthandiza,+ Adani akewo anamuona, ndipo anamuseka+ chifukwa chakuti wagwa. ח [Chehth]   Yerusalemu wachita tchimo+ lalikulu. N’chifukwa chake wakhala chinthu chonyansa.+ Onse amene anali kumulemekeza ayamba kumuona ngati chinthu chachabechabe,+ chifukwa aona maliseche+ ake. Iyenso akuusa moyo+ ndipo watembenukira kwina chifukwa cha manyazi. ט [Tehth]   Zovala+ zake ndi zodetsedwa. Iye sanaganizire za tsogolo+ lake. Wagwa modabwitsa ndipo alibe womutonthoza.+ Inu Yehova, onani kusautsika+ kwanga, pakuti mdani wanga akudzitukumula.+ י [Yohdh] 10  Mdani watambasula dzanja lake n’kutenga zinthu+ zake zonse zabwino. Yerusalemu waona mitundu ina itabwera ndi kulowa m’malo ake opatulika,+ Mitundu imene munalamula kuti isalowe mumpingo wanu. כ [Kaph] 11  Anthu ake onse akuusa moyo. Iwo akufunafuna chakudya.+ Asinthanitsa zinthu zawo zabwino ndi chakudya kuti adzitsitsimutse.+ Inu Yehova ndiyang’aneni. Onani kuti ndakhala ngati mkazi wachabechabe.+ ל [La′medh] 12  Inu nonse amene mukudutsa m’njira, kodi mukuona ngati imeneyi ndi nkhani yaing’ono? Ndiyang’aneni kuti muone.+ Kodi palinso ululu wina woposa ululu umene ineyo ndalangidwa nawo,+ Ululu umene Yehova wandibweretsera nawo chisoni m’tsiku la mkwiyo+ wake woyaka moto? מ [Mem] 13  Iye watumiza moto m’mafupa+ mwanga kuchokera kumwamba, ndipo wafooketsa fupa lililonse. Watchera ukonde+ kuti ukole mapazi anga. Wandibweza kumbuyo. Wandisandutsa mkazi wosiyidwa popanda thandizo. Ndikudwala tsiku lonse.+ נ [Nun] 14  Iye wakhala tcheru kuti aone machimo+ anga. Machimowo alukanalukana m’dzanja lake. Amangidwa m’khosi+ mwanga, moti mphamvu zanga zatha. Yehova wandipereka m’manja mwa anthu amene sindingathe kulimbana nawo.+ ס [Sa′mekh] 15  Yehova wandichotsera  anthu anga onse  amphamvu+ ndi kuwakankhira pambali. Wandiitanitsira msonkhano kuti athyolethyole anyamata anga.+ Yehova wapondaponda moponderamo mphesa+ mwa namwali, mwana wamkazi wa Yuda.+ ע [ʽA′yin] 16  Ndikulirira zinthu zimenezi ngati mkazi.+ Maso anga ine! Maso anga akutuluka misozi.+ Pakuti wonditonthoza, munthu woti anditsitsimule, ali kutali ndi ine. Ana anga asiyidwa+ popanda thandizo, pakuti mdani wanga wadzitukumula.+ פ [Peʼ] 17  Ziyoni watambasula manja ake.+ Iye alibe womutonthoza.+ Yehova walamula onse ozungulira Yakobo kuti akhale adani ake.+ Yerusalemu wakhala chinthu chonyansa pakati pawo.+ צ [Tsa·dheh′] 18  Yehova ndi wolungama,+ koma ine ndapandukira+ mawu a pakamwa pake. Anthu nonsenu, tamverani mawu anga, ndipo muone ululu umene ndikumva. Anamwali anga ndi anyamata anga atengedwa kupita ku ukapolo.+ ק [Qohph] 19  Ndaitana anthu ondikonda kwambiri,+ koma anthuwo andichitira zachinyengo. Ansembe anga ndiponso akuluakulu atha+ mumzinda. Atha pamene anali kufunafuna chakudya choti adye kuti adzitsitsimutse.+ ר [Rehsh] 20  Taonani, inu Yehova. Inetu zandivuta. M’mimba mwanga mukubwadamuka.+ Mtima wanga wasweka,+ pakuti ndapanduka kwambiri.+ Panja, lupanga lapha+ ana. M’nyumba, anthu akufanso.+ ש [Shin] 21  Anthu amva mmene ndikuusira moyo ngati mkazi,+ koma palibe wonditonthoza.+ Adani anga onse amva za tsoka+ langa. Iwo akondwera,+ chifukwa ndinu mwachititsa zimenezi. Inu mubweretsadi tsiku limene mwanena,+ kuti iwo akhale ngati ine.+ ת [Taw] 22  Kuipa kwawo konse kuonekere pamaso panu, ndipo muwalange+ koopsa. Muwalange koopsa monga mmene mwandilangira ine chifukwa cha machimo+ anga onse. Pakuti ndikuusa+ moyo kwambiri ndipo mtima wanga ukudwala.+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti “wowathamangitsa.”