Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Maliko 7:1-37

7  Tsopano Afarisi ndi alembi ena ochokera ku Yerusalemu anasonkhana kwa Yesu.+  Ndipo pamene anaona ena mwa ophunzira ake akudya chakudya ndi manja oipitsidwa, kapena kuti, m’manja mosasamba*+  . . .    pakuti Afarisi ndi Ayuda onse sadya osasamba m’manja mpaka m’zigongono, posunga mwambo wa makolo.  Akabwera kuchokera kumsika, sadya mpaka atadziyeretsa mwa kudziwaza madzi. Palinso miyambo ina yambiri+ imene anailandira ndipo akuisunga, monga kuviika makapu, mitsuko ndi ziwiya zamkuwa m’madzi+ . . .  choncho Afarisi ndi alembi amenewa anam’funsa iye kuti: “N’chifukwa chiyani ophunzira anu satsatira miyambo ya makolo, koma amadya chakudya ndi manja oipitsidwa?”+  Iye anawayankha kuti: “Yesaya analosera moyenera za anthu onyenga inu, monga mmene Malemba amanenera kuti,+ ‘Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yawo ili kutali ndi ine.+  Amandipembedza pachabe, chifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.’+  Mumanyalanyaza malamulo a Mulungu, ndi kuumirira mwambo wa anthu.”+  Pamenepo anapitiriza kuwauza kuti: “Mochenjera, mumakankhira pambali malamulo+ a Mulungu kuti musunge mwambo wanu. 10  Mwachitsanzo, Mose ananena kuti, ‘Uzilemekeza bambo ako ndi mayi ako,’+ komanso anati, ‘Aliyense wonenera bambo ake kapena mayi ake zachipongwe afe ndithu.’+ 11  Koma anthu inu mumanena kuti, ‘Munthu akauza bambo ake kapena mayi ake kuti: “Chilichonse chimene ine ndili nacho, chimene mukanatha kupindula nacho, ndi khobani,+ (kutanthauza kuti, mphatso yoperekedwa+ kwa Mulungu,)”’ . . . 12  anthu inu simulolanso munthuyo kuchitira bambo ake kapena mayi ake chinthu chilichonse.+ 13  Mwa kuchita zimenezi, mumapangitsa mawu a Mulungu+ kukhala opanda pake chifukwa cha mwambo wanu umene munaupereka kwa anthu. Ndipo mumachita zinthu zambiri+ zofanana ndi zimenezi.” 14  Atatero, anaitananso khamu la anthuwo kuti abwere kwa iye, ndipo anayamba kulankhula nawo kuti: “Mverani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.+ 15  Palibe chilichonse chochokera kunja kwa munthu ndi kulowa m’thupi mwake chimene chingaipitse munthu, koma zotuluka mwa munthu ndi zimene zimaipitsa munthu.”+ 16*  —— 17  Tsopano atalowa m’nyumba ina kutali ndi khamu la anthulo, ophunzira ake anayamba kumufunsa za fanizo lija.+ 18  Chotero iye anawafunsa kuti: “Kodi nanunso ndinu osazindikira ngati iwo aja?+ Kodi inunso simudziwa kuti palibe chochokera kunja kwa thupi n’kudutsa m’thupi mwa munthu chimene chingamuipitse, 19  popeza sichidutsa mumtima mwake, koma m’matumbo mwake, ndipo chimakatuluka kuchimbudzi?”+ Pamenepo anagamula kuti zakudya zonse n’zoyera.+ 20  Kenako anafotokozanso kuti: “Chotuluka mwa munthu n’chimene chimaipitsa munthu.+ 21  Pakuti mkatimo, mumtima mwa munthu,+ mumatuluka maganizo oipa. Mumatuluka zadama,*+ zakuba, zaumbanda,+ 22  zachigololo, kusirira kwa nsanje,+ kuchita zoipa, chinyengo, khalidwe lotayirira,+ diso la kaduka, mnyozo, kudzikweza, ndiponso kuchita zinthu mosaganizira ena. 23  Zoipa zonsezi zimatuluka mkatimo ndipo zimaipitsa munthu.”+ 24  Atanyamuka kumeneko, analowera kumadera a Turo ndi Sidoni.+ Kumeneko anakalowa m’nyumba ina, ndipo sanafune kuti aliyense adziwe kuti ali kumeneko. Koma anthu anadziwabe.+ 25  Nthawi yomweyo, mayi wina amene anali ndi mwana wamkazi wogwidwa ndi mzimu wonyansa anamva za iye ndipo anabwera ndi kugwada, n’kumuweramira mpaka nkhope yake pansi.+ 26  Mayiyu anali Mgiriki, wachisurofoinike. Iye anapempha Yesu kuti atulutse chiwanda mwa mwana wakeyo.+ 27  Koma Yesu anayamba n’kunena kuti: “Choyamba, zimafunika kuti ana akhute kaye, chifukwa si bwino kutenga chakudya cha ana+ ndi kuponyera tiagalu.”+ 28  Koma poyankha mayiyo ananena kuti: “Inde mbuyanga, komabe tiagalu timadya nyenyeswa+ za anawo pansi pa tebulo.”+ 29  Yesu atamva mawuwo anauza mayiyo kuti: “Chifukwa wanena zimenezi, pita, chiwandacho chatuluka mwa mwana wakoyo.”+ 30  Choncho anapita kunyumba kwake ndipo anakapeza+ mwanayo atagona pabedi chiwandacho chitatuluka. 31  Tsopano pobwerera kuchoka m’madera a Turo, anadutsa ku Sidoni ndi kufika kunyanja ya Galileya mpaka kukadutsa mkati mwa zigawo za Dekapole.+ 32  Kumeneko anthu anam’bweretsera munthu wogontha komanso wovutika kulankhula. Iwo anamupempha kuti aike dzanja lake pa munthuyo.+ 33  Koma iye anatenga munthuyo ndi kuchoka naye pakhamu la anthulo kupita naye pambali. Kumeneko anapisa zala zake m’makutu a munthuyo, ndipo analavula ndi kukhudza lilime lake.+ 34  Pamenepo anayang’ana kumwamba,+ kenako anausa moyo*+ ndi kumuuza kuti: “Efata,” kutanthauza kuti, “Tseguka.” 35  Atatero, makutu ake anatseguka,+ lilime lake lomangikalo linamasuka, moti anayamba kulankhula bwinobwino. 36  Ndiyeno anawalamula kuti asauze aliyense zimenezo.+ Koma ankati akawaletsa mwamphamvu kuti asauze aliyense, m’pamenenso iwo anali kuzifalitsa kwambiri.+ 37  Inde, iwo anali kudabwa kwambiri+ ndipo anali kunena kuti: “Wachita zinthu zonse bwinobwino ndithu. Ngakhale ogontha akumva ndipo osalankhula akuwalankhulitsa.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Mt 15:2.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.
Onani Zakumapeto 7.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.