Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Maliko 13:1-37

13  Pamene Yesu anali kutuluka m’kachisi, mmodzi wa ophunzira ake anamuuza kuti: “Mphunzitsi, taonani mmene miyala ndi nyumbazi zikuonekera!”+  Koma Yesu ananena kuti: “Kodi waziona nyumba zapamwamba zimenezi?+ Pano sipadzatsala mwala+ uliwonse pamwamba pa unzake umene sudzagwetsedwa.”+  Tsopano atakhala pansi m’phiri la Maolivi, kachisi akuonekera bwino, Petulo,+ Yakobo, Yohane ndi Andireya anayamba kumufunsa kumbaliko kuti:+  “Tiuzeni, Kodi zinthu zimenezi zidzachitika liti, ndipo chizindikiro chosonyeza kuti zinthu zonsezi zili m’nthawi yake yamapeto n’chiyani?”+  Choncho Yesu anayamba kuwauza kuti: “Samalani kuti munthu asakusocheretseni.+  Ambiri adzabwera m’dzina langa, ndi kunena kuti, ‘Khristu uja ndine,’ ndipo adzasocheretsa anthu ambiri.+  Komanso, mukadzamva phokoso la nkhondo ndi mbiri za nkhondo, musadzachite mantha. Zimenezi ziyenera kuchitika ndithu, koma mapeto adzakhala asanafikebe.+  “Pakuti mtundu udzaukirana ndi mtundu wina, ndiponso ufumu ndi ufumu wina.+ Kudzakhala zivomezi+ m’malo osiyanasiyana ndiponso kudzakhala njala.+ Zimenezi ndi chiyambi cha masautso, ngati mmene zimayambira zowawa za pobereka.+  “Koma inu khalani wochenjera. Anthu adzakuperekani kumakhoti aang’ono,+ ndipo adzakukwapulani m’masunagoge+ ndi kukuimikani pamaso pa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo.+ 10  Komanso, m’mitundu yonse uthenga wabwino+ uyenera ulalikidwe choyamba.+ 11  Koma pamene akupita nanu kukakuperekani, musafulumire kuda nkhawa kuti mukanena chiyani.+ Zimene mukapatsidwe mu ola lomwelo, mukanene zimenezo, pakuti wolankhula si inu, koma mzimu woyera.+ 12  Komanso, munthu adzapereka m’bale wake ku imfa, ndipo bambo adzapereka mwana wake,+ ndi ana adzaukira makolo awo ndi kuwaphetsa.+ 13  Ndipo anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa.+ Koma amene adzapirire mpaka pa mapeto,+ ndiye amene adzapulumuke.+ 14  “Koma mukadzaona chinthu chonyansa+ chosakaza+ chitaimirira pamene sichiyenera kuima (wowerenga adzazindikire),+ pamenepo amene ali mu Yudeya adzayambe kuthawira kumapiri.+   15  Munthu amene ali padenga la nyumba asadzatsike, kapena kulowa mkati kukatenga chilichonse m’nyumba mwakemo.+ 16  Ndipo munthu amene ali m’munda, asadzabwerere ku zinthu zimene wazisiya, kukatenga malaya ake akunja.+ 17  Tsoka kwa akazi apakati ndi oyamwitsa ana m’masiku amenewo!+ 18  Pitirizani kupemphera kuti zisadzachitike mu nyengo yachisanu.+ 19  Pakuti masiku amenewo adzakhala masiku a chisautso+ chimene sichinachitikepo kuchokera pa chiyambi cha chilengedwe chimene Mulungu analenga kudzafika nthawi imeneyo, ndipo sichidzachitikanso.+ 20  Kunena zoona, Yehova akanapanda+ kufupikitsa masikuwo, palibe amene akanapulumuka. Koma chifukwa cha osankhidwawo,+ amene iye anawasankha,+ wafupikitsa masikuwo.+ 21  “Komanso pa nthawiyo, munthu akadzakuuzani kuti, ‘Onani! Khristu uja ali kuno,’+ ‘Onani! Ali uko,’ musadzakhulupirire zimenezo.+ 22  Pakuti kudzafika onamizira kukhala Khristu ndiponso aneneri onyenga,+ ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa+ kuti ngati n’kotheka, adzasocheretse osankhidwawo.+ 23  Choncho inuyo khalani ochenjera.+ Ine ndakuuziranitu zinthu zonse.+ 24  “Koma m’masiku amenewo, chisautso chimenecho chikadzatha, dzuwa lidzachita mdima, ndipo mwezi sudzapereka kuwala kwake. 25  Nyenyezi zidzagwa kuchokera kumwamba, ndipo mphamvu zimene zili kumwamba zidzagwedezeka.+ 26  Kenako adzaona Mwana wa munthu+ akubwera m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemerero.+ 27  Ndiyeno adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa+ ake kuchokera kumphepo zinayi, kuchokera kumalekezero ake a dziko lapansi kukafika kumalekezero a m’mlengalenga.+ 28  “Tsopano phunzirani pa fanizo ili la mkuyu: Pamene nthambi yake yanthete yaphuka ndi kuchita masamba, mumadziwa kuti dzinja lili pafupi.+ 29  Chimodzimodzi inunso, mukadzaona zinthu izi zikuchitika, dziwani kuti iye ali pafupi. Dziwani kuti ali pakhomo penipeni.+ 30  Ndithu ndikukuuzani kuti m’badwo uwu sudzatha konse, kufikira zinthu zonsezi zitachitika.+ 31  Kumwamba+ ndi dziko lapansi zidzachoka, koma mawu+ anga sadzachoka ayi.+ 32  “Kunena za tsikulo kapena ola lake, palibe amene akudziwa, ngakhale angelo kumwamba kapenanso Mwana, koma Atate okha.+ 33  Khalani maso, khalani tcheru,+ pakuti simukudziwa pamene nthawi yoikidwiratu idzafika.+ 34  Zili ngati munthu amene anali kupita kutali kudziko lina,+ amene anasiya nyumba m’manja mwa akapolo ake, aliyense pa ntchito yake, ndi kulamula mlonda wa pachipata kuti azikhala maso. 35  Choncho khalani maso,+ pakuti simukudziwa nthawi yobwera mwininyumba. Simukudziwa ngati adzabwere madzulo, pakati pa usiku, atambala akulira, kapena m’mawa,*+ 36  kuti akadzafika mwadzidzidzi, asadzakupezeni mukugona.+ 37  Koma zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.”+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:25.