Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Machitidwe 4:1-37

4  Pamene Petulo ndi Yohane anali kulankhula ndi anthuwo, ansembe aakulu, woyang’anira kachisi+ ndi Asaduki+ anafika kwa iwo.  Iwo anali okwiya chifukwa atumwiwo anali kuphunzitsa anthu ndi kulalikira mosapita m’mbali za kuuka kwa akufa pogwiritsa ntchito chitsanzo cha Yesu.+  Choncho anawagwira ndi kuwasunga m’ndende mpaka tsiku lotsatira,+ chifukwa anali kale madzulo.  Koma anthu ambiri amene anamvetsera mawu awo anakhulupirira,+ ndipo chiwerengero cha amuna chinakwana pafupifupi 5,000.+  Tsiku lotsatira, olamulira ndi akulu ndiponso alembi anasonkhana pamodzi mu Yerusalemu.+  (Pamenepo panalinso Anasi+ wansembe wamkulu, Kayafa,+ Yohane, Alekizanda, ndi achibale ambiri a wansembe wamkuluyo.)  Ndiyeno anaimika atumwiwo pakati pawo n’kuyamba kuwafunsa kuti: “Kodi mwachita zimenezi ndi ulamuliro uti kapena m’dzina la ndani?”+  Pamenepo Petulo, atadzazidwa ndi mzimu woyera,+ anawayankha kuti: “Olamulira anthu ndiponso akulu inu,  ngati pa ntchito yabwino imene tachita kwa wodwalayu,+ lero tikufunsidwa kuti tamuchiritsa m’dzina la ndani, 10  dziwani nonsenu ndi Aisiraeli onse, kuti m’dzina la Yesu Khristu Mnazareti+ uja, amene inu munamupachika pamtengo,+ koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa,+ kudzera mwa iyeyo, munthu uyu waimirira pamaso panu atachira bwinobwino. 11  Yesu ameneyu ndiye ‘mwala umene inu omanga nyumba munauona ngati wopanda pake, umene tsopano wakhala mwala wofunika kwambiri wapakona.’+ 12  Ndiponso chipulumutso sichipezeka mwa munthu wina aliyense, pakuti palibe dzina lina+ pansi pa thambo, limene laperekedwa kwa anthu, limene tiyenera kupulumutsidwa nalo.”+ 13  Tsopano ataona mmene Petulo ndi Yohane anali kulankhulira molimba mtima, komanso atazindikira kuti anali anthu osaphunzira ndiponso anthu wamba,+ anadabwa kwambiri. Ndipo anayamba kuwazindikira kuti anali kuyenda ndi Yesu.+ 14  Ndiyeno poona munthu wochiritsidwa uja ataimirira nawo limodzi,+ analibe chonena kuti awatsutse.+ 15  Choncho anawalamula kuti atuluke muholo ya Khoti Lalikulu la Ayuda,* ndipo anayamba kufunsana, 16  kuti: “Tichite nawo chiyani amuna amenewa?+ Chifukwa kunena zoona, iwo achitadi chizindikiro chachikulu, chimene chaonekera kwa onse okhala mu Yerusalemu.+ Ndipo ife sitingatsutse zimenezi. 17  Komabe, kuti nkhaniyi isapitirire kufalikira kwa anthu ena, tiyeni tiwaopseze kuti asalankhulenso m’dzina limeneli kwa munthu wina aliyense.”+ 18  Atatero anawaitana ndi kuwalamula kuti asalankhulenso kapena kuphunzitsa m’dzina la Yesu kwina kulikonse. 19  Koma poyankha, Petulo ndi Yohane anawauza kuti: “Weruzani nokha, ngati n’koyenera pamaso pa Mulungu kumvera inu koposa Mulungu. 20  Koma ife sitingaleke kulankhula zinthu zimene tinaziona ndi kuzimva.”+ 21  Choncho atawonjezera kuwaopseza, anawamasula, pakuti sanapeze chifukwa chilichonse chowapatsira chilango. Komanso anaopa anthu,+ pakuti onse anali kutamanda Mulungu chifukwa cha zimene zinachitikazo. 22  Ndipotu chizindikiro cha machiritsochi chinachitika kwa munthu amene anali ndi zaka zopitirira 40. 23  Atawamasula anapita kwa okhulupirira anzawo,+ ndipo anawafotokozera zonse zimene ansembe aakulu, ndi akulu anawauza. 24  Atamva zimenezi, onse pamodzi anafuula kwa Mulungu+ mokweza mawu kuti: “Ambuye Wamkulu Koposa,+ Inu ndi amene munapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zokhala mmenemo. 25  Ndinu amene mwa mzimu woyera, munanena kudzera pakamwa pa kholo lathu Davide, mtumiki wanu kuti, ‘N’chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita chipolowe, ndiponso n’chifukwa chiyani mitundu ya anthu ikusinkhasinkha zinthu zopanda pake?+ 26  Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo, ndipo olamulira asonkhana pamodzi mogwirizana, kuti alimbane ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.’+ 27  Zimenezi zinachitikadi pamene Herode,* Pontiyo Pilato,+ pamodzi ndi anthu a mitundu ina komanso anthu a mu Isiraeli, anasonkhana mumzinda uno ndi kuukira Yesu, mtumiki wanu woyera,+ amene inu munamudzoza.+ 28  Iwo anasonkhana pamodzi kuti achite zimene inu munaneneratu. Zimenezi zinachitika chifukwa inu muli ndi mphamvu komanso chifukwa chakuti zinali zogwirizana ndi chifuniro chanu.+ 29  Koma tsopano Yehova, imvani mmene akutiopsezera,+ ndipo lolani kuti akapolo anu apitirize kulankhula mawu anu molimba mtima.+ 30  Pitirizani kutambasula dzanja lanu ndi kupereka machiritso, komanso kuti zizindikiro ndi zodabwitsa+ zipitirize kuchitika m’dzina+ la Yesu, mtumiki wanu woyera.”+ 31  Atatha kupembedzera, malo amene anasonkhanawo anagwedezeka.+ Pamenepo aliyense wa iwo anadzazidwa ndi mzimu woyera,+ ndipo anayamba kulankhula mawu a Mulungu molimba mtima.+ 32  Ndipo onse amene anakhulupirira anakhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.+ Panalibe ngakhale mmodzi wonena kuti zinthu zimene anali nazo zinali zayekha. Zonse zimene anali nazo zinali za onse.+ 33  Komanso, atumwiwo anapitiriza kuchitira umboni mwamphamvu kwambiri za kuuka kwa Ambuye Yesu.+ Ndipo kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu kunali pa onsewo. 34  Ndithudi, panalibe ngakhale mmodzi wosowa kanthu pakati pawo. Onse amene anali ndi minda kapena nyumba, anali kuzigulitsa ndi kubweretsa ndalamazo, 35  kudzazipereka kwa atumwi.+ Ndiyeno ndalamazo anali kuzigawa+ kwa aliyense malinga ndi zosowa zake. 36  Choncho Yosefe, amene atumwiwo anamutchanso Baranaba,+ dzina limene polimasulira limatanthauza, Mwana wa Chitonthozo, amene anali Mlevi, komanso mbadwa ya ku Kupuro, 37  anali ndi munda. Iye anagulitsa mundawo ndi kubweretsa ndalamazo kudzazipereka kwa atumwi.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Sanihedirini.”
Onani mawu a m’munsi pa Mt 14:1.