Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Machitidwe 15:1-41

15  Ndiyeno amuna ena ochokera ku Yudeya+ anapita kumeneko ndi kuyamba kuphunzitsa abale kuti: “Mukapanda kudulidwa+ malinga ndi mwambo wa Mose,+ simungapulumuke.”  Koma Paulo ndi Baranaba sanamvane nawo ndipo anatsutsana nawo kwambiri. Choncho iwo anasankha Paulo ndi Baranaba, pamodzi ndi ena mwa iwo, kuti apite kwa atumwi ndi akulu ku Yerusalemu,+ kuti akawauze za kutsutsanako.  Tsopano mpingo utawaperekeza,+ amuna amenewa anapitiriza ulendo wawo kudzera ku Foinike ndi ku Samariya. Kumeneko anali kufotokoza mwatsatanetsatane za kutembenuka kwa anthu a mitundu ina,+ ndipo iwo anasangalatsa kwambiri abale onse.+  Atafika ku Yerusalemu analandiridwa ndi manja awiri+ ndi mpingo, atumwi, komanso akulu. Kumeneko anafotokoza zinthu zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo.+  Koma okhulupirira ena, amene kale anali m’gulu lampatuko la Afarisi anaimirira m’mipando yawo n’kunena kuti: “M’pofunika kuwadula+ ndi kuwalamula kuti azisunga chilamulo cha Mose.”+  Ndiyeno atumwi ndi akulu anasonkhana pamodzi kuti akambirane nkhani imeneyi.+  Tsopano atatsutsana kwambiri,+ Petulo anaimirira, ndi kuwauza kuti: “Amuna inu, abale anga, mukudziwa bwino kuti m’masiku oyambirira Mulungu anandisankha ine pakati panu, kuti kudzera pakamwa panga, anthu a mitundu ina amve mawu a uthenga wabwino ndi kukhulupirira.+  Ndipo Mulungu, amene amadziwa zamumtima,+ anachitira umboni mwa kuwapatsa mzimu woyera,+ monga anachitiranso kwa ife.  Ndipo iye sanasiyanitse m’pang’ono pomwe pakati pa ife ndi iwo.+ Koma anayeretsa mitima yawo chifukwa cha chikhulupiriro chawo.+ 10  Nanga tsopano n’chifukwa chiyani inu mukumuyesa Mulungu mwa kukanikizira goli pakhosi la ophunzira, goli+ limene makolo athu ngakhalenso ife sitinathe kulisenza?+ 11  Koma tsopano timakhulupirira kuti ife tidzapulumuka mwa kukoma mtima kwakukulu+ kwa Ambuye Yesu, mofanananso ndi anthu amenewa.”+ 12  Pamenepo gulu lonselo linakhala chete, ndipo linayamba kumvetsera Baranaba ndi Paulo pamene anali kufotokoza zizindikiro ndi zodabwitsa zambiri zimene Mulungu anachita kudzera mwa iwo pakati pa anthu a mitundu ina.+ 13  Ataleka kulankhula, Yakobo anayankha kuti: “Amuna inu, abale anga, ndimvetsereni.+ 14  Sumeoni+ wafotokoza bwino mmene Mulungu anacheukira anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa iwo atengemo anthu odziwika ndi dzina lake.+ 15  Ndipo zimenezi zikugwirizana ndi mawu a m’Zolemba za aneneri. Mawuwo amati, 16  ‘Zimenezi zikadzatha ndidzabwerera ndi kumanganso nyumba ya Davide imene inagwa. Ndidzamanganso malo ogumuka a nyumbayo ndi kuiimikanso.+ 17  Ndidzachita zimenezi kuti anthu otsalirawo afunefune Yehova ndi mtima wonse. Amufunefune pamodzi ndi mitundu yonse ya anthu, anthu otchedwa ndi dzina langa, watero Yehova amene akuchita zinthu zimenezi,+ 18  zimene anatsimikiza kalekale kuti adzazichita.’+ 19  Choncho chigamulo changa n’chakuti, anthu amene akuchokera m’mitundu ina ndi kutembenukira kwa Mulungu, tisawavutitse.+ 20  Koma tiyeni tiwalembere kuti apewe zinthu zoipitsidwa ndi mafano,+ dama,*+ zopotola,+ ndi magazi.+ 21  Pakuti kuyambira kalekale, anthu akhala akulalikira mumzinda ndi mzinda mawu ochokera m’mabuku a Mose, chifukwa mabuku amenewa amawerengedwa mokweza m’masunagoge sabata lililonse.”+ 22  Pamenepo atumwi ndi akulu pamodzi ndi mpingo wonse, anagwirizana zosankha amuna pakati pawo, kuti awatumize ku Antiokeya limodzi ndi Paulo ndi Baranaba. Choncho anasankha Yudasi wotchedwa Barasaba,+ ndi Sila, amuna otsogolera pakati pa abale. 23  Chotero ndi manja awo analemba kuti: “Ife abale anu atumwi pamodzi ndi akulu, tikulembera inu abale athu ochokera mwa anthu a mitundu ina, okhala ku Antiokeya,+ ku Siriya ndi ku Kilikiya:+ Landirani moni! 24  Tamva kuti ena ochokera pakati pathu akhala akulankhula mawu okusautsani,+ pofuna kupotoza maganizo anu, ngakhale kuti ife sitinawapatse malangizo aliwonse.+ 25  Pa chifukwa chimenechi, tonse tagwirizana chimodzi,+ ndipo tavomerezana kuti tisankhe amuna oti tiwatumize kwa inu limodzi ndi okondedwa athu, Baranaba ndi Paulo.+ 26  Amenewa ndi amuna omwe apereka miyoyo yawo chifukwa cha dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu.+ 27  Chotero tikutumiza Yudasi ndi Sila,+ kuti iwonso adzakufotokozereni zinthu zomwezi mwa mawu apakamwa.+ 28  Pakuti mzimu woyera+ pamodzi ndi ife taona kuti ndi bwino kuti tisakusenzetseni mtolo wolemera,+ kupatula zinthu zofunika zokhazi zomwe ndi 29  kupitiriza kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano,+ magazi,+ zopotola,+ ndi dama.+ Mukamapewa zinthu zimenezi mosamala kwambiri,+ zinthu zidzakuyenderani bwino. Tikukufunirani zabwino zonse!” 30  Amuna amenewa atanyamuka, analowera ku Antiokeya. Kumeneko anasonkhanitsa khamu lonse la anthu ndi kuwapatsa kalatayo.+ 31  Ataiwerenga, anakondwera chifukwa cha mawu olimbikitsawo.+ 32  Ndiponso popeza kuti Yudasi ndi Sila anali aneneri,+ analimbikitsa abalewo ndi mawu ambiri ndipo anawapatsa mphamvu.+ 33  Atakhala kumeneko kanthawi, abalewo anawalola kubwerera mumtendere+ kwa amene anawatuma. 34*  —— 35  Koma Paulo ndi Baranaba anatsalira ku Antiokeya.+ Ndipo iwo pamodzi ndi enanso ambiri anali kuphunzitsa ndi kulengeza uthenga wabwino wa mawu a Yehova.+ 36  Patapita masiku, Paulo anauza Baranaba kuti: “Tsopano, tiyeni tibwerere kumizinda yonse kumene tinafalitsa mawu a Yehova kuti tikachezere abale ndi kuwaona kuti ali bwanji.”+ 37  Chotero Baranaba anafunitsitsa kutenga Yohane, wotchedwa Maliko.+ 38  Koma Paulo anaona kuti n’kosayenera kumutenga kuti apite nawo. Anaona kuti n’kosayenera chifukwa ulendo wapita Yohane anawasiya ku Pamfuliya+ ndipo sanapite nawo ku ntchitoyi. 39  Pamenepo panabuka mkangano woopsa mpaka anapatukana. Baranaba+ anatenga Maliko ndipo anayenda ulendo wa pamadzi kulowera ku Kupuro.+ 40  Koma Paulo anasankha Sila,+ ndipo abale atamuikiza m’manja mwa Yehova kuti amusonyeze kukoma mtima kwakukulu, ananyamuka.+ 41  Iye anadzera ku Siriya ndi ku Kilikiya, ndipo anali kulimbitsa mipingo.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 7.
Za mawu amene palibe, onani mawu a m’munsi pa Mt 17:21.