Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Luka 4:1-44

4  Tsopano Yesu anachoka ku Yorodano atadzazidwa ndi mzimu woyera. Ndipo mzimuwo unamutenga ndi kumuyendetsa uku ndi uku m’chipululu+  kwa masiku 40, kumene anali kuyesedwa+ ndi Mdyerekezi. Komanso m’masiku amenewo sanali kudya chilichonse, choncho masikuwo atatha, anamva njala.  Mdyerekezi ataona zimenezi anamuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani mwala uwu kuti usanduke mkate.”  Koma Yesu anamuyankha kuti: “Malemba amati, ‘Munthu sangakhale ndi moyo ndi chakudya chokha.’”  Choncho anakwera naye pamwamba ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko lapansi m’kanthawi kochepa.  Ndiyeno Mdyerekezi anamuuza kuti: “Ndikupatsani ulamuliro+ pa maufumu onsewa ndi ulemerero wawo wonse, chifukwa unaperekedwa kwa ine. Ndikhoza kuupereka kwa aliyense amene ndakonda kum’patsa.+  Chotero ngati inuyo mungandiweramireko+ kamodzi kokha, ulamuliro wonsewu udzakhala wanu.”  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Malemba amati, ‘Yehova* Mulungu wako ndi amene uyenera kumulambira, ndipo uyenera kutumikira iye yekha basi.’”  Kenako anamutengera ku Yerusalemu, ndipo anamukweza pamwamba pa khoma+ la mpanda wa kachisi n’kumuuza kuti: “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, mudziponye pansi kuchokera pano.+ 10  Pajatu Malemba amati, ‘Iye adzalamula angelo ake za inu, kuti akutetezeni.’+ 11  Choncho, ‘Adzakunyamulani m’manja mwawo, kuti phazi lanu lisawombe mwala uliwonse.’”+ 12  Poyankha Yesu anamuuza kuti: “Pajatu Malemba amati, ‘Usamuyese, Yehova Mulungu wako.’” 13  Choncho Mdyerekeziyo atamaliza mayesero onsewo, anamusiya kufikira nthawi ina yabwino.+ 14  Tsopano Yesu anabwerera ku Galileya+ atadzazidwa ndi mphamvu ya mzimu. Ndipo mbiri yake yabwino inamveka ponseponse m’madera onse ozungulira.+ 15  Komanso, anayamba kuphunzitsa m’masunagoge awo, ndipo anthu onse anali kumulemekeza.+ 16  Kenako anabwera ku Nazareti,+ kumene analeredwa. Malinga ndi chizolowezi chake pa tsiku la sabata, analowa m’sunagoge,+ ndi kuimirira kuti awerenge Malemba. 17  Pamenepo anamupatsa mpukutu wa mneneri Yesaya. Iye anafunyulula mpukutuwo ndi kupeza pamene panalembedwa mawu akuti: 18  “Mzimu wa Yehova+ uli pa ine, chifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka. Anandituma kudzalalikira za kumasulidwa kwa ogwidwa ukapolo, ndi zoti akhungu ayambe kuona. Anandituma kudzamasula oponderezedwa kuti akhale mfulu,+ 19  ndi kudzalalikira chaka chovomerezeka kwa Yehova.”+ 20  Atatero anapinda mpukutuwo, n’kuubwezera kwa wotumikira mmenemo ndi kukhala pansi. Maso onse m’sunagogemo anali pa iye kumuyang’anitsitsa. 21  Ndiyeno anayamba kuwauza kuti: “Lero lemba ili, limene mwangolimva kumeneli lakwaniritsidwa.”+ 22  Pamenepo onse anayamba kumutamanda ndi kudabwa ndi mawu ogwira mtima+ otuluka pakamwa pake, mwakuti anali kunena kuti: “Kodi iyeyu si mwana wa Yosefe?”+ 23  Zitatero iye anawauza kuti: “Mosakayikira mawu akuti, ‘Wochiritsa+ iwe, dzichiritse wekha,’ mudzawagwiritsa ntchito pa ine. Mudzanena kuti: ‘Tinamva kuti unachita zinthu zambiri ku Kaperenao.+ Zinthu zimenezo+ uzichitenso kwanu kuno.’”+ 24  Iye ananenanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani, palibe mneneri amene amalandiridwa kwawo. 25  Mwachitsanzo, ndikukuuzani ndithu kuti, Munali akazi ambiri amasiye mu Isiraeli m’masiku a Eliya, pamene kumwamba kunatsekedwa zaka zitatu ndi miyezi 6, mwakuti m’dziko lonse munagwa njala yaikulu. 26  Koma Eliya sanatumizidwe kwa aliyense wa akazi amenewo. M’malomwake anatumizidwa kwa mkazi wamasiye ku Zarefati m’dziko la Sidoni. 27  Ndiponso, munali akhate ambiri mu Isiraeli m’nthawi ya mneneri Elisa. Komabe palibe aliyense wa iwo amene anayeretsedwa, koma Namani, mwamuna wa ku Siriya.” 28  Tsopano onse amene anali kumvetsera mawu amenewa m’sunagogemo anakwiya kwambiri.+ 29  Iwo ananyamuka ndipo mwamsangamsanga anamutulutsira kunja kwa mzinda. Kenako anapita naye pamwamba pa phiri limene anamangapo mzinda wawo, kuti akam’ponye kuphedi.+ 30  Koma iye anangodutsa pakati pawo n’kumapita.+ 31  Choncho anapita ku Kaperenao,+ mzinda wa ku Galileya. Ndipo anali kuwaphunzitsa pa sabata. 32  Kumeneko anthu anadabwa kwambiri ndi kaphunzitsidwe kake,+ chifukwa anali kulankhula ndi mphamvu za ulamuliro.+ 33  Tsopano m’sunagogemo munali munthu wogwidwa ndi mzimu,+ chiwanda chonyansa, ndipo anafuula ndi mawu amphamvu kuti: 34  “Tili nanu chiyani,+ Yesu Mnazareti?+ Kodi mwabwera kudzatiwononga? Inetu ndikukudziwani+ bwino kwambiri, ndinu Woyera wa Mulungu.”+ 35  Koma Yesu anadzudzula mzimuwo kuti: “Khala chete, ndipo tuluka mwa iye.” Choncho chiwandacho chinagwetsa munthuyo pansi pakati pawo, kenako chinatuluka mwa iye osamuvulaza.+ 36  Ataona zimenezi, onse anadabwa kwambiri, ndipo anayamba kukambirana kuti: “Kulankhula kumeneku ndi kwa mtundu wanji anthuni? Taonani! Akutha kudzudzula mizimu yonyansa mwa ulamuliro ndi mphamvu, ndipo mizimuyo ikutulukadi.”+ 37  Choncho mbiri yake inapitiriza kufalikira ponseponse m’midzi yonse yozungulira.+ 38  Atatuluka m’sunagogemo, anakalowa m’nyumba ya Simoni. Kumeneko apongozi aakazi a Simoni anali kudwala malungo* aakulu, choncho anam’pempha kuti apite kumeneko chifukwa cha mayiwo.+ 39  Chotero anaima pamene mayiwo anagona ndi kuwachiritsa,+ ndipo malungowo anatheratu. Nthawi yomweyo mayiwo anadzuka n’kuyamba kuwatumikira.+ 40  Koma pamene dzuwa linali kulowa, onse amene anali ndi anthu odwala matenda osiyanasiyana anawabweretsa kwa iye. Ndipo iye anawachiritsa mwa kuika manja ake pa aliyense.+ 41  Ziwanda nazonso zinatuluka mwa anthu ambiri.+ Zinali kufuula kuti: “Inu ndinu Mwana+ wa Mulungu.” Koma iye anali kudzudzula ziwandazo, ndipo sanali kuzilola kuti zilankhule,+ chifukwa zinali kudziwa kuti iye+ ndi Khristu.+ 42  Kutacha, anatuluka ndi kupita kumalo kopanda anthu.+ Koma khamu la anthu linayamba kumufunafuna mpaka linafika kumene iye anali, ndipo anthuwo anayesa kumuletsa kuti asawasiye. 43  Koma iye anawauza kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, chifukwa ndi zimene anandituma kudzachita.”+ 44  Choncho anapita n’kumalalikira m’masunagoge a mu Yudeya.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 2.
Mawu ake enieni, “kutentha thupi.”