Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Luka 20:1-47

20  Tsiku lina pamene anali kuphunzitsa anthu m’kachisi ndi kulengeza uthenga wabwino, panafika ansembe aakulu, alembi pamodzi ndi akulu.+  Iwo anamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+  Poyankha Yesu anawauza kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi, ndipo mundiyankhe:+  Kodi ubatizo wa Yohane unali wochokera kumwamba kapena kwa anthu?”+  Pamenepo iwo anayamba kukambirana okhaokha kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye anena kuti, ‘Nanga n’chifukwa chiyani simunamukhulupirire?’+  Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala,+ chifukwa iwo akukhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane+ anali mneneri.”+  Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera.  Pamenepo Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.”+  Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa,+ ndipo anasiya mundawo m’manja mwa alimi n’kupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+ 10  Koma nyengo ya zipatso itakwana anatumiza kapolo+ wake kwa alimiwo,+ kuti akamupatseko zina mwa zipatso za m’munda wa mpesawo.+ Komano alimiwo anamumenya ndi kumubweza chimanjamanja.+ 11  Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya ndi kumuchitira chipongwe, ndipo anamubweza chimanjamanja.+ 12  Anatumizanso wachitatu.+ Uyunso anamuvulaza ndi kumuponya kunja. 13  Zitatero mwini munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mwana wanga yekhayu ayenera kuti akamulemekeza ndithu.’ 14  Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eya, uyu ndiye wolandira cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’+ 15  Atatero anamutulutsa+ m’munda wa mpesawo ndi kumupha.+ Pamenepa, kodi mwini munda wa mpesa uja adzachita chiyani kwa alimiwo?+ 16  Adzabwera ndi kupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.”+ Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!” 17  Koma iye anawayang’ana ndi kunena kuti: “Pajatu malemba amati, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana,+ umenewu wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? 18  Aliyense wogwera pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere,+ udzam’pereratu.”+ 19  Tsopano alembi ndi ansembe aakulu aja, pozindikira kuti iye anali kunena za iwo mufanizolo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma anaopa anthu.+ 20  Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, n’cholinga choti akamukole+ m’mawu ake, kuti akamupereke ku boma ndi kwa bwanamkubwa.+ 21  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti mumanena ndi kuphunzitsa molondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi.+ 22  Kodi n’kololeka kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”+ 23  Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti:+ 24  “Ndionetseni khobidi la dinari. Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo n’zandani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.”+ 25  Iye anawauza kuti: “Chotero perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 26  Pamenepo iwo analephera kumutapa m’kamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, mwakuti pothedwa nzeru ndi yankho lake, anangokhala chete kusowa chonena.+ 27  Koma Asaduki ena, amene amanena kuti kulibe kuuka kwa akufa anafika+ ndi kuyamba kumufunsa, 28  kuti: “Mphunzitsi, Mose+ anatilembera kuti, ‘Ngati munthu wamwalira n’kusiya mkazi amene sanabereke naye ana, m’bale wake+ atenge mkazi wamasiyeyo ndi kuberekera m’bale wake uja ana mwa mkaziyo.’+ 29  Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anatenga mkazi, koma anamwalira wopanda mwana.+ 30  Wachiwirinso chimodzimodzi. 31  Kenako wachitatu anamutenga. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja: onse anamwalira osasiya ana.+ 32  Pa mapeto pake mkazi uja nayenso anamwalira.+ 33  Kodi pamenepa, pouka kwa akufa, mkazi ameneyu adzakhala wa ndani popeza onse 7 anamukwatira?”+ 34  Yesu anawayankha kuti: “Ana a m’nthawi* ino amakwatira+ ndi kukwatiwa. 35  Koma amene ayesedwa oyenerera+ kudzapeza moyo pa nthawi* imeneyo+ ndi kudzaukitsidwa kwa akufa+ sadzakwatira kapena kukwatiwa. 36  Ndiponso iwo sadzafanso,+ chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu mwa kukhala ana a kuuka kwa akufa.+ 37  Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza m’nkhani ya chitsamba cha minga.+ M’nkhani imeneyo iye ananena kuti Yehova ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+ 38  Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, pakuti kwa iye onsewa ndi amoyo.”+ 39  Poyankha ena mwa alembiwo anati: “Mphunzitsi, mwanena bwino.” 40  Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi. 41  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “N’chifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 42  Pakuti Davide mwiniyo ananena m’buku la Masalimo kuti, ‘Yehova anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43  kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.”’+ 44  Chotero Davide anamutcha ‘Ambuye.’ Nanga akukhala bwanji mwana wake?” 45  Kenako, anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzirawo kuti:+ 46  “Chenjerani ndi alembi. Iwo amakonda kuyendayenda atavala mikanjo. Amakonda kupatsidwa moni m’misika ndi kukhala m’mipando yakutsogolo m’masunagoge. Amakondanso malo olemekezeka kwambiri pa chakudya chamadzulo.+ 47  Iwo ndi amene amadyerera nyumba za akazi amasiye,+ ndipo mwachiphamaso amapereka mapemphero ataliatali. Anthu amenewa adzalandira chiweruzo champhamvu.”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.