Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Levitiko 9:1-24

9  Tsopano pa tsiku la 8,+ Mose anaitana Aroni, ana ake ndi akulu a Isiraeli.  Pamenepo anauza Aroni kuti: “Tenga ng’ombe yaing’ono kuti ikhale nsembe yamachimo,+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Nyama zonsezi zikhale zopanda chilema, ndipo uzipereke kwa Yehova.+  Koma uza ana a Isiraeli kuti, ‘Tengani mbuzi yamphongo+ kuti ikhale nsembe yamachimo. Mutengenso mwana wa ng’ombe ndi nkhosa yaing’ono yamphongo,+ zonsezi zikhale za chaka chimodzi, zopanda chilema, kuti zikhale nsembe yopsereza.  Mutengenso ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo kuti muzipereke kwa Yehova monga nsembe zachiyanjano.+ Komanso mubwere ndi nsembe yambewu+ yothira mafuta, chifukwa lero Yehova aonekera ndithu kwa inu.’”+  Choncho anthuwo anatenga zimene Mose analamula n’kupita nazo kuchihema chokumanako. Kenako khamu lonse linayandikira ndi kuima pamaso pa Yehova.+  Ndiyeno Mose anati: “Mverani zimene Yehova walamula kuti muchite, kuti ulemerero wa Yehova uonekere kwa inu.”+  Pamenepo Mose anauza Aroni kuti: “Pita kuguwa lansembe ndi kupereka nsembe yako yamachimo+ ndi nsembe yako yopsereza, kuti uphimbe machimo+ ako ndi a nyumba yako. Kenako uperekere nsembe anthuwa+ ndi kuwaphimbira machimo awo,+ monga mmene Yehova walamulira.”  Nthawi yomweyo Aroni anapita kuguwa lansembe ndi kupha ng’ombe yaing’ono kuti ikhale nsembe yake yamachimo.+  Ndiyeno ana ake anam’bweretsera magazi+ a ng’ombeyo, ndipo iye anaviika chala chake m’magaziwo+ ndi kuwapaka panyanga za guwa lansembe.+ Magazi otsala anawathira pansi pa guwa lansembelo. 10  Ndipo mafuta,+ impso ndi mafuta a pachiwindi zimene anazitenga panyama ya nsembe yamachimo anazitentha paguwa lansembe,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 11  Koma nyama ndi chikopa chake anazitentha kunja kwa msasa.+ 12  Ndiyeno Aroni anapha nyama ya nsembe yopsereza, ndipo ana ake anam’patsa magazi a nyamayo. Pamenepo iye anawaza magaziwo mozungulira paguwa lansembe.+ 13  Kenako anam’patsa ziwalo za nyama ya nsembe yopsereza pamodzi ndi mutu, ndipo anazitentha paguwa lansembe.+ 14  Atatero, anatsuka matumbo ndi ziboda, n’kuzitentha paguwa lansembe+ pamwamba pa nsembe yopsereza. 15  Ndiyeno anaperekera nsembe anthu.+ Anatenga mbuzi yoperekera anthu nsembe yamachimo, ndipo anaipha, n’kuipereka monga nsembe yamachimo, mmene anachitira ndi nyama yoyamba ija. 16  Atatero anapereka nsembe yopsereza motsatira ndondomeko yake.+ 17  Kenako anapereka nsembe yambewu.+ Anatapako nsembeyo kudzaza dzanja lake ndi kuitentha paguwa lansembe, kuwonjezera pa nsembe yopsereza ya m’mawa.+ 18  Ndiyeno Aroni anapha ng’ombe yamphongo ndi nkhosa yamphongo ya nsembe yachiyanjano yoperekera anthuwo.+ Kenako ana ake anam’patsa magazi a nyamazo ndipo iye anawaza magaziwo mozungulira paguwa lansembe.+ 19  Kunena za mafuta+ a ng’ombeyo, mchira wa mafuta+ wa nkhosa, mafuta okuta matumbo, impso ndi mafuta a pachiwindi, 20  ana a Aroni anaika zinthu za mafuta zimenezo pamwamba pa nganga+ za nyamazo. Kenako anatentha mafutawo paguwa lansembe. 21  Koma Aroni anaweyula*+ cha uku ndi uku ngangazo ndi mwendo wakumbuyo wa kudzanja lamanja pamaso pa Yehova, monga mmene Mose analamulira. 22  Kenako Aroni anakweza manja ake pa anthuwo ndi kuwadalitsa.+ Atatero, anatsika+ kuguwa lansembe kumene anali atapereka nsembe yamachimo, nsembe yopsereza ndi nsembe zachiyanjano. 23  Pamenepo Mose ndi Aroni analowa m’chihema chokumanako, kenako anatulukamo n’kudalitsa anthuwo.+ Atatero, ulemerero wa Yehova+ unaonekera kwa anthu onse, 24  ndipo moto unatsika kuchokera kwa Yehova+ n’kunyeketsa nsembe yopsereza ndiponso mafuta, zimene zinali paguwa lansembe. Anthu onse ataona zimenezi, anayamba kufuula mokondwera+ ndipo anagwada n’kuwerama mpaka nkhope zawo pansi.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 29:24.