Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Hoseya 2:1-23

2  “Uzani abale anu kuti, ‘Inu ndinu anthu anga,’+ ndipo alongo anu muwauze kuti, ‘Inu ndinu akazi osonyezedwa chifundo.’+  Imbani mlandu mayi wanu.+ Muimbeni mlandu pakuti iye si mkazi wanga+ ndipo ine sindine mwamuna wake.+ Mayi wanuyo asiye dama lake ndi chigololo chake,*+  kuti ndisamuvule ndi kumukhalitsa wamaliseche+ ngati tsiku limene anabadwa,+ kutinso ndisamuchititse kukhala ngati chipululu+ ndi dziko lopanda madzi+ ndiponso kuti ndisamuphe ndi ludzu.+  Ana a mayiyo sindiwachitira chifundo,+ pakuti ndi ana obadwa chifukwa cha dama lake,+  popeza mayi wawo wachita dama.+ Mayi amene anatenga pakati kuti awabereke wachita zinthu zochititsa manyazi+ ndipo wanena kuti, ‘Ndikufuna kutsatira amene anali kundikonda kwambiri+ ndiponso amene anali kundipatsa chakudya, madzi, zovala za ubweya wa nkhosa, nsalu, mafuta ndi zakumwa.’+  “Tsopano ine ndikutsekereza njira yake ndi mpanda waminga, ndipo ndidzamumangira mpanda wamiyala+ ndi kumutsekereza kuti asapeze njira zake.+  Pamenepo iye adzathamangira amuna omukonda kwambiriwo, koma sadzawapeza.+ Adzawafunafuna koma sadzawapeza. Ndiyeno adzanena kuti, ‘Ndikufuna kubwerera kwa mwamuna wanga+ woyamba,+ pakuti zinthu zinali kundiyendera bwino nthawi imeneyo kusiyana ndi mmene zilili tsopano.’+  Koma iye sanavomereze+ kuti ndine amene ndinali kumupatsa mbewu,+ vinyo wotsekemera* ndi mafuta. Sanavomerezenso kuti ndine amene ndinamuchulukitsira siliva ndi golide amene iye anali kumugwiritsa ntchito popembedza Baala.+  “‘Chotero ndidzatembenuka ndi kumulanda mbewu zanga pa nthawi yokolola. Ndidzalanda vinyo wanga wotsekemera pa nyengo yopanga vinyo.+ Ndidzamulandanso zovala zanga za ubweya wa nkhosa ndi nsalu zanga zimene amabisa nazo maliseche ake.+ 10  Tsopano ndidzamuvula kuti amuna omukonda kwambiriwo aone maliseche ake,+ ndipo palibe mwamuna amene adzamukwatula m’dzanja langa.+ 11  Pamenepo ndidzathetsa kusangalala kwake konse.+ Ndidzathetsa zikondwerero zake,+ chikondwerero cha tsiku lokhala mwezi,+ cha sabata ndi chikondwerero china chilichonse. 12  Ndidzawononga mitengo yake ya mpesa+ ndi ya mkuyu+ imene iye anali kunena kuti: “Imeneyi ndi mphatso imene amuna ondikonda kwambiri anandipatsa.” Koma ine ndidzachititsa mitengoyo kukhala ngati nkhalango,+ ndipo zilombo zakutchire zidzaidya ndi kuiwononga. 13  Ndiyeno ndidzamuimba mlandu+ chifukwa cha masiku amene anapembedza zifaniziro za Baala+ zimene anali kuzifukizira nsembe zautsi.+ Nthawi imeneyi anali kuvala mphete* yake ndi zinthu zake zodzikongoletsera.+ Iye anali kutsatira amuna omukonda kwambiri+ ndipo ine anandiiwala,’+ watero Yehova. 14  “‘Choncho ndidzalankhula naye ndi kumukhutiritsa kuti achoke ndi kupita kuchipululu,+ ndipo ndidzalankhula naye momufika pamtima.+ 15  Kuyambira nthawi imeneyo mpaka m’tsogolo ndidzamupatsa minda yake ya mpesa.+ Ndidzamupatsanso chigwa cha Akori+ kuti chikhale ngati khomo lachiyembekezo. Pamenepo adzayankha ngati mmene anali kuyankhira ali mtsikana,+ ngatinso mmene anayankhira pa tsiku limene anatuluka m’dziko la Iguputo.’+ 16  Yehova wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo adzanditcha kuti Mwamuna wanga, ndipo sadzanditchanso kuti Mbuyanga.’*+ 17  “‘Sindidzamulola kutchulanso mayina a zifaniziro za Baala,+ ndipo iye sadzakumbukiranso mayina awo.+ 18  Pa tsiku limenelo ndidzachita pangano ndi chilombo chakuthengo,+ cholengedwa chouluka m’mlengalenga ndi cholengedwa chokwawa panthaka, kuti ndithandize anthu anga. Ndidzathyola uta ndi lupanga ndipo ndidzathetsa nkhondo padziko.+ Pamenepo ndidzawachititsa kukhala mwabata.+ 19  Ndidzalonjeza kukukwatira kuti ukhale wanga mpaka kalekale.*+ Ndidzalonjeza kukukwatira motsatira chilungamo, komanso chifukwa cha kukoma mtima kwanga kosatha ndi chifundo changa.+ 20  Ndidzalonjeza kukukwatira mokhulupirika ndipo udzadziwadi Yehova.’+ 21  “Yehova wanena kuti: ‘Pa tsiku limenelo kumwamba ndidzakuyankha zopempha zake ndipo kumwambako kudzayankha zopempha za dziko lapansi.+ 22  Ndiyeno dziko lapansi lidzayankha mbewu,+ vinyo wotsekemera ndi mafuta, ndipo zimenezi zidzayankha Yezereeli.*+ 23  Pamenepo ndidzamufesa ngati mbewu zanga padziko lapansi.+ Ndidzachitira chifundo amene sanasonyezedwe chifundo+ ndipo ndidzauza anthu amene si anthu anga kuti: “Inu ndinu anthu anga,”+ ndipo iwo adzayankha kuti: “Inu ndinu Mulungu wathu.”’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “achotse dama lake pamaso pake ndi zochita zake zachigololo pakati pa mawere ake.”
Ena amati “wonzuna.”
Kapena kuti “chipini.” Onani Miy 11:22, mawu a m’munsi.
Kapena kuti “Baala wanga,” kutanthauza “Mwiniwake wa ine.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani mawu a m’munsi pa Ho 1:11.