Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Hoseya 13:1-16

13  “Efuraimu akalankhula, anthu anali kunjenjemera. Iye anali wolemekezeka mu Isiraeli, koma anapezeka ndi mlandu wolambira Baala ndipo anafa.  Tsopano anthu ake akuchita machimo ena ndipo akugwiritsa ntchito siliva wawo popanga zifanizo zachitsulo chosungunula.+ Zifanizo zimenezo ndi mafano opangidwa mogwirizana ndi maganizo awo,+ koma zonsezi ndi ntchito za amisiri.+ Iwo amauza mafanowo kuti, ‘Amuna opereka nsembe apsompsone mafano a ana ang’ombe.’  Chotero iwo adzakhala ngati mitambo ya m’mawa+ ndiponso ngati mame amene sachedwa kuuma. Adzakhalanso ngati mankhusu* amene amauluzika kuchokera pamalo opunthira mbewu+ ndiponso ngati utsi umene umatuluka m’chumuni kudenga.*  “Koma ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo. Panalibe Mulungu wina amene unali kumudziwa kupatulapo ine. Panalibenso mpulumutsi wina kupatulapo ine.+  Ine ndinakudziwa uli m’chipululu, m’dziko la matenda otenthetsa thupi.+  Iwe unakhuta chifukwa chakuti unali ndi zakudya zambiri. Unakhuta ndipo mtima wako unayamba kudzitukumula. N’chifukwa chake unandiiwala.  Ine ndidzakhala ngati mkango wamphamvu kwa iwo.+ Ndidzapitiriza kuwayang’ana ngati kambuku* amene wabisala m’mphepete mwa njira.+  Ndidzawaukira ngati chimbalangondo chimene ana ake asowa ndipo ndidzang’amba zifuwa zawo, mmene muli mitima yawo. Ndidzawadya kumeneko ngati mkango.+ Chilombo chakuthengo chidzawakhadzulakhadzula.+  Chifukwa chakuti zimene iwe Isiraeli unachita zinali zotsutsana ndi ine mthandizi wako,+ zimenezo zidzakuwononga.+ 10  “Tsopano mfumu yako ili kuti, kuti ikupulumutse m’mizinda yako yonse. Oweruza ako ali kuti amene unawauza kuti, ‘Ndipatseni mfumu ndi akalonga’? 11  Ndiyeno ndinakupatsa mfumu nditakwiya ndipo ndidzaichotsa nditakwiya. 12  “Zolakwa za Efuraimu zakulungidwa pamodzi, ndipo machimo ake asungidwa. 13  Zowawa ngati za mkazi amene akubereka zidzamugwera.+ Iye ndi mwana wopanda nzeru+ chifukwa nthawi yoti abadwe ikakwana, sadzadziika pamalo amene ana amatulukira pochokera m’chiberekero. 14  “Ine ndidzawawombola ku Manda*+ ndiponso ku imfa.+ Iwe Imfa amene umabweretsa ululu woopsa, kodi mphamvu yako ili kuti?+ Iwe Manda amene umawononga, kodi uli kuti?+ Koma Efuraimu sindimumverabe chisoni. 15  “Ndipo iye akayamba kubereka ndi kutulutsa ana ngati bango, mphepo ya kum’mawa, mphepo ya Yehova idzabwera.+ Mphepo yake ikuchokera kuchipululu ndipo idzaumitsa chitsime chake ndi kuphwetsa kasupe wake.+ Ameneyo adzawononga chuma chimene chikuphatikizapo zinthu zosiririka. 16  “Samariya adzaimbidwa mlandu chifukwa iye akupandukira Mulungu wake. Iwo adzagwetsedwa ndi lupanga.+ Ana awo adzaphwanyidwaphwanyidwa ndipo akazi awo amene ali ndi pakati adzatumbulidwa.”

Mawu a M'munsi

“Mankhusu” ndi makoko amene amachotsa ku mbewu ngati mpunga popuntha, ndipo amatha kuwauluza ndi mphepo.
Kapena kuti “tsindwi.”
Ena amati “nyalugwe.”
Onani Zakumapeto 5.