Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Hoseya 12:1-14

12  “Efuraimu akudya mphepo+ ndi kuthamangitsa mphepo ya kum’mawa tsiku lonse.+ Iye akuchulukitsa mabodza ndipo akuwononga zinthu zambiri. Wachita pangano ndi Asuri ndipo wapititsa mafuta ku Iguputo.  “Yehova ali ndi mlandu woti aimbe Yuda. Adzalanga Yakobo mogwirizana ndi njira zake+ ndipo adzamubwezera mogwirizana ndi zochita zake.+  Pamene Yakobo anali m’mimba anagwira m’bale wake chidendene. Iye analimbana ndi Mulungu ndi mphamvu zake zonse.  Anapitiriza kulimbana ndi mngelo ndipo pamapeto pake anapambana. Analira pochonderera kuti amudalitse.” Mulungu anamupeza ku Beteli ndipo kumeneko Mulungu anayamba kulankhula nafe.  Iye ndi Yehova Mulungu wa makamu. Yehova ndilo dzina lake lomukumbukira nalo.  “Koma iwe ubwerere kwa Mulungu wako.+ Usonyeze kukoma mtima kosatha+ ndi chilungamo ndipo nthawi zonse uziyembekezera Mulungu wako.+  M’manja mwa wamalonda muli sikelo yachinyengo ndipo iye amakonda kuba mwachinyengo.+  Efuraimu akupitiriza kunena kuti, ‘Inetu ndalemeradi,+ ndapeza zinthu zamtengo wapatali. Palibe amene angapeze cholakwa chachikulu pa ntchito zanga zonse.’+  “Ine ndine Yehova Mulungu wako kuchokera pamene unali ku Iguputo. Koma ndidzakuchititsa kukhala m’mahema ngati pa masiku achikondwerero. 10  Ndinalankhula ndi aneneri ndipo ndinawaonetsa masomphenya ochuluka. Kudzera mwa aneneri, ndinali kupereka mafanizo ambiri.+ 11  “Ku Giliyadi anthu akuchita zamatsenga+ ndiponso akulankhula zabodza.+ Ku Giligala akupereka nsembe ng’ombe zamphongo.+ Komanso maguwa awo ansembe ali ngati milu ya miyala m’mizere ya m’munda. 12  Yakobo anathawira kumunda wa ku Siriya ndipo Isiraeli anapitirizabe kugwira ntchito ndi kulondera nkhosa kuti apeze mkazi.+ 13  Yehova anatulutsa Isiraeli ku Iguputo pogwiritsa ntchito mneneri, ndipo mneneri analondera Isiraeli. 14  Efuraimu anakhumudwitsa kwambiri Mulungu. Magazi amene iye anakhetsa ali pa iyeyo+ ndipo Ambuye Wamkulu adzamubwezera chitonzo chake.”+

Mawu a M'munsi