Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Hoseya 10:1-15

10  “Isiraeli ndi mtengo wa mpesa umene ukuwonongeka.+ Iye akupitiriza kubereka zipatso+ ndipo wachulukitsa maguwa ansembe mogwirizana ndi kuchuluka kwa zipatso zake.+ Pamene dzikolo likutukuka kwambiri m’pamenenso Aisiraeli akumanga zipilala zopatulika zokongola kwambiri.  Mtima wawo wakhala wachinyengo. Tsopano iwo adzapezeka ndi mlandu. “Pali wina amene adzathyola maguwa awo ansembe ndipo adzasakaza zipilala zawo zopatulika.+  Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Tilibe mfumu+ pakuti sitinaope Yehova. Ngakhale tikanakhala ndi mfumu, kodi ikanatichitira chiyani?’  “Iwo amalankhula mawu opanda pake, amachita malumbiro abodza, amachita mapangano+ ndipo kusalungama kwafalikira ngati zomera zakupha m’mizere ya m’munda.  Anthu okhala ku Samariya adzachita mantha ndi fano la ku Beti-aveni la mwana wa ng’ombe. Pakuti anthuwo pamodzi ndi ansembe a mulungu wachilendo, amene anali kusangalala ndi fanolo chifukwa cha ulemerero wake, adzalilirira. Adzalirira fanolo chifukwa ulemerero wake udzachoka likadzatengedwa kupita kudziko lina.  Wina adzapititsa fanolo kudziko la Asuri ndi kukalipereka monga mphatso kwa mfumu yaikulu. Efuraimu adzachita manyazi+ ndipo Isiraeli adzachita manyazi ndi zoipa zimene anali kufuna kuchita.+  Samariya pamodzi ndi mfumu yake adzakhalitsidwa chete, ngati kanthambi kothyoledwa mumtengo kamene kakuyandama pamadzi.  Malo okwezeka a ku Beti-aveni,+ omwe ndi tchimo la Isiraeli, adzawonongedwa. Minga ndi zitsamba zobaya*+ zidzamera pamaguwa awo ansembe. Anthu adzauza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza zitunda kuti, ‘Tikwirireni!’+  “Inu ana a Isiraeli, mwakhala mukuchimwa kuyambira m’masiku a Gibeya ndipo anthu anapitirizabe kuchita machimo kumeneko. Nkhondo ya ku Gibeya yomenyana ndi anthu osalungama sinawawononge onse. 10  Ndidzawalanga mtima wanga ukadzafuna.+ Anthu a mitundu ina adzasonkhana kuti alimbane nawo pa nthawi imene iwo adzamangidwe kugoli la zolakwa zawo ziwiri. 11  “Efuraimu anali ng’ombe yaikazi yosaberekapo yophunzitsidwa bwino yokonda kupuntha mbewu,+ ndipo ine ndinapitirira khosi lake lokongola. Koma tsopano ndichititsa wina kukwera pamsana pa Efuraimu. Yuda akulima,+ Yakobo akumusalazira zibuma za dothi.+ 12  Bzalani mbewu za chilungamo+ ndipo kololani zipatso za kukoma mtima kosatha.+ Limani munda panthaka yabwino+ pamene muli ndi nthawi yofunafuna Yehova, kufikira iye atabwera+ ndi kukupatsani malangizo onena za chilungamo. 13  “Anthu inu mwalima zoipa+ ndipo mwakolola kusalungama.+ Mwadya zipatso za zochita zanu zachinyengo,+ pakuti munali kudalira njira zanu+ ndi kuchuluka kwa anthu anu amphamvu.+ 14  Pakati pa anthu a mtundu wanu pachitika chisokonezo+ ndipo mizinda yanu yonse yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri idzawonongedwa, ngati mmene Salimani anawonongera Beti-aribeli. Iye anachita zimenezi pa tsiku lankhondo, pamene amayi anaphwanyidwaphwanyidwa pamodzi ndi ana awo.+ 15  Inu anthu a ku Beteli, wina adzakuchitaninso zimenezi chifukwa ndinu anthu oipitsitsa.+ Ndithu, mfumu ya Isiraeli adzaikhalitsa chete m’bandakucha.”

Mawu a M'munsi

Ena amati “kulasa.”