Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Hagai 2:1-23

2  M’mwezi wa 7,+ pa tsiku la 21 la mweziwo, Yehova analankhula ndi mneneri Hagai+ kuti:  “Chonde, kauze Zerubabele,+ mwana wa Salatiyeli+ bwanamkubwa wa Yuda,+ Yoswa+ mwana wa Yehozadaki+ mkulu wa ansembe ndi anthu ena onse kuti,  ‘Kodi pakati panu pali wotsala aliyense amene anaona ulemerero umene nyumbayi inali nawo poyamba?+ Kodi panopa mukuiona bwanji? Kodi simukuona kuti ilibe ulemerero poyerekeza ndi ulemerero umene inali nawo poyamba?’+  “‘Koma tsopano limba mtima iwe Zerubabele. Limba mtima+ iwe Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe,’ watero Yehova. “‘Limbani mtima anthu nonse a m’dzikoli ndipo gwirani ntchito,’+ watero Yehova. “‘Pakuti ine ndili ndi inu,’+ watero Yehova wa makamu.  ‘Kumbukirani pangano limene ndinapangana nanu pamene munali kutuluka m’dziko la Iguputo.+ Pa nthawi imeneyo ndinakutumizirani mzimu+ wanga kuti ukutsogolereni. Choncho musachite mantha.’”+  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Posachedwapa+ ndigwedezanso kumwamba, dziko lapansi, nyanja ndi mtunda.’+  “‘Ndigwedeza mitundu yonse ya anthu, ndipo zinthu zamtengo wapatali zochokera ku mitundu yonse ya anthu zidzalowa m’nyumba imeneyi.+ Ine ndidzadzaza nyumbayi ndi ulemerero,’+ watero Yehova wa makamu.  “‘Siliva ndi wanga, ndipo golide ndi wanganso,’+ watero Yehova wa makamu.  “‘Ulemerero wa nyumba yatsopanoyi udzakhala waukulu kuposa wa nyumba yoyamba ija,’+ watero Yehova wa makamu. “‘Ndipo ndidzakhazikitsa mtendere pamalo awa,’+ watero Yehova wa makamu.” 10  Pa tsiku la 24 la mwezi wa 9, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Dariyo, Yehova analankhula ndi mneneri Hagai+ kuti: 11  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Funsa ansembe zokhudza chilamulo.+ Uwafunse kuti: 12  “Ngati munthu atanyamula nyama yopatulika pachovala chake, ndiyeno chovalacho n’kukhudza mkate, kapena msuzi, kapena vinyo, kapena mafuta, kapena chakudya chamtundu uliwonse, kodi chinthu chokhudzidwacho chingakhale chopatulika?”’”+ Pamenepo ansembe anayankha kuti: “Ayi!” 13  Ndiyeno Hagai anafunsanso kuti: “Ngati munthu amene wadetsedwa chifukwa chokhudza mtembo atakhudza chilichonse mwa zinthu zimenezi, kodi chingakhale chodetsedwa?”+ Ansembewo anayankha kuti: “Inde, chingakhale chodetsedwa.” 14  Choncho Hagai anati: “‘Umutu ndi mmene anthu awa alili, ndipo ndi mmene mtundu uwu wa anthu ulili pamaso panga.+ Ndi mmenenso ntchito yonse ya manja awo ndi chilichonse chimene amapereka nsembe chilili. Ndi zodetsedwa,’+ watero Yehova. 15  “‘Koma tsopano, chonde ganizirani zimenezi mofatsa+ kuyambira lero mpaka m’tsogolo. Ganizirani mmene zinthu zinalili asanasanjikize mwala pamwala unzake m’kachisi wa Yehova.+ 16  Pa nthawi imeneyo zomwe zinali kuchitika n’zakuti, munthu anali kupita pamulu umene ukanakwana miyezo 20, koma anali kupeza kuti ndi wokwana miyezo 10. Munthu anali kupita moponderamo mphesa kuti akatunge miyezo 50 ya vinyo, koma anali kupeza kuti muli wongokwana miyezo 20 yokha.+ 17  Anthu inu, ine ndinawononga mbewu zanu ndi mphepo yotentha,+ matenda a chuku+ ndi matalala.+ Zimenezi zinawononganso ntchito zonse za manja anu.+ Koma panalibe aliyense wa inu amene anabwerera kwa ine,’+ watero Yehova. 18  “‘Ganizirani mofatsa+ zimene zichitike kuyambira lero mpaka m’tsogolo. Muganizire mofatsa zimene zinachitika kuyambira pa tsiku la 24 la mwezi wa 9, pamene maziko a kachisi wa Yehova anayalidwa.+ Ganizirani izi mofatsa: 19  Kodi mbewu zilipobe m’dzenje losungiramo mbewu?+ Kodi mitengo ya mpesa, mitengo ya mkuyu, mitengo ya makangaza* ndi mitengo ya maolivi ikuberekabe zipatso? Kuyambira lero ndikupatsani madalitso.’”+ 20  Yehova analankhula ndi Hagai+ kachiwiri pa tsiku la 24 la mweziwo+ kuti: 21  “Uza Zerubabele bwanamkubwa wa Yuda kuti,+ ‘Ine ndigwedeza kumwamba ndi dziko lapansi.+ 22  Ndithu ndidzagonjetsa maufumu ndi kuchotsa mphamvu za maufumu a anthu a mitundu ina.+ Ndiwononga magaleta* ndi okwera pamagaletawo. Mahatchi* ndi okwera mahatchiwo adzaphedwa.+ Aliyense adzapha m’bale wake ndi lupanga.’”+ 23  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Pa tsiku limenelo ndidzakutenga iwe Zerubabele+ mwana wa Salatiyeli,+ mtumiki wanga,’ watero Yehova. ‘Ndipo ndidzakusunga ngati mphete yodindira,+ chifukwa iwe ndi amene ndakusankha,’+ watero Yehova wa makamu.”+

Mawu a M'munsi

“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu, mwina chifukwa choti njere zake zimaoneka ngati chimanga.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ena amati “mahosi,” kapena “akavalo.”