Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Hagai 1:1-15

1  M’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo, m’mwezi wa 6, pa tsiku loyamba la mweziwo, mawu a Yehova anafika kwa Zerubabele mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda, ndi kwa Yoswa+ mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe. Mawuwa anafika kwa anthu amenewa kudzera mwa mneneri Hagai kuti:  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Anthu awa akunena kuti: “Nthawi yomanga nyumba ya Yehova sinakwane.”’”  Yehova anapitiriza kulankhula kudzera mwa mneneri Hagai kuti:  “Kodi ino ndi nthawi yoti inu muzikhala m’nyumba zokongoletsedwa ndi matabwa, nyumba iyi ili bwinja?+  Tsopano Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.  Mwafesa mbewu zambiri koma zokolola zanu n’zochepa.+ Mukudya koma simukukhuta. Mukumwa koma simukukhutira.* Mukuvala zovala koma simukumva kutentha. Amene akugwira ganyu akulandirira ndalama zake m’matumba obowoka.’”+  “Yehova wa makamu wanena kuti, ‘Ganizirani mofatsa zimene mukuchita.’+  “‘Pitani kuphiri ndipo mukabweretse mitengo yomangira nyumba. Mumange nyumbayi kuti ndisangalale nayo komanso nditamandidwe,’ watero Yehova.”  “‘Munali kufunafuna zinthu zambiri, koma mwapeza zochepa.+ Mwabweretsa zinthuzo m’nyumba zanu ndipo ine ndaziuzira n’kuzimwaza.+ N’chifukwa chiyani ndachita zimenezi?+ Chifukwa chakuti simunamalize kumanga nyumba yanga. Koma aliyense wa inu akuthamangathamanga kuti asamalirire nyumba yake,’ watero Yehova wa makamu. 10  ‘N’chifukwa chake kumwamba sikunakugwetsereni mame, ndipo dziko lapansi silinakupatseni zipatso zake. 11  Ndinalamula kuti chilala chigwe padziko lapansi, pamapiri, pambewu, pavinyo watsopano,+ pamafuta, pazinthu zonse zochokera munthaka, pa anthu, paziweto ndi pa ntchito iliyonse ya manja anu.’”+ 12  Ndiyeno Zerubabele mwana wa Salatiyeli ndi Yoswa mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe, ndiponso anthu ena onse anayamba kumvetsera mawu a Yehova Mulungu wawo+ ndi a mneneri Hagai, chifukwa Yehova Mulungu wawo anamutuma. Pamenepo anthuwo anayamba kuchita mantha chifukwa cha Yehova.+ 13  Hagai mthenga wa Yehova analankhula kwa anthuwo malinga ndi ntchito imene Yehova anam’patsa.+ Iye anati: “‘Ine ndili ndi inu,’ watero Yehova.” 14  Yehova analimbikitsa Zerubabele mwana wa Salatiyeli bwanamkubwa wa Yuda, Yoswa+ mwana wa Yehozadaki mkulu wa ansembe ndi anthu ena onse. Choncho iwo anapita kukagwira ntchito panyumba ya Yehova wa makamu, Mulungu wawo. 15  Zimenezi zinachitika pa tsiku la 24 la mwezi wa 6, m’chaka chachiwiri cha ulamuliro wa Mfumu Dariyo.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “simukuledzera.”