Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Habakuku 2:1-20

2  Ine ndidzaimabe+ pamalo a mlonda ndiponso pakhoma lachitetezo. Ndidzakhala tcheru+ kuti ndione uthenga umene iye adzalankhula kudzera mwa ine+ ndi zimene ndidzayankha pamene iye akundidzudzula.+  Pamenepo Yehova anandiyankha kuti: “Lemba masomphenyawa moonekera bwino pamiyala yosema,+ kuti wowerenga mokweza awerenge mosadodoma.+  Uchite zimenezi pakuti masomphenyawa akuyembekezera nthawi yake yoikidwiratu+ ndipo akuthamangira kumapeto kwake. Zimene zili m’masomphenyazi si zonama. Ngakhale masomphenyawa atazengereza, uziwayembekezerabe* chifukwa adzakwaniritsidwa ndithu.+ Iwo sadzachedwa.  “Taona! Iye wadzitukumula+ ndipo si wowongoka mtima. Koma wolungama adzakhalabe ndi moyo mwa chikhulupiriro chake.+  Ndiye pakuti vinyo ndi wachinyengo,+ mwamuna wamphamvu amadzimva,+ koma sadzakwaniritsa cholinga chake.+ Iye wakulitsa chilakolako chake ngati Manda* ndipo sangakhutire ngati imfa.+ Iye akupitiriza kudzisonkhanitsira mitundu yonse ya anthu ndi anthu onse pamodzi.+  Kodi anthu onsewa sadzamunenera mwambi,+ chining’a ndi mawu okuluwika? Wina adzanena kuti, “‘Kodi iye adzapitiriza kuchulukitsa zinthu zimene si zake+ kwa nthawi yaitali bwanji?+ Tsoka kwa iye pakuti akungochulukitsa ngongole yake.  Kodi amene uli nawo ngongole sadzanyamuka ndi kubwera modzidzimutsa kuti uwabwezere ngongole yawo? Kodi okugwedeza mwachiwawa sadzanyamuka ndi kubwera kudzafunkha zinthu zako zonse?+  Chifukwa chakuti iwe unafunkha mitundu yambiri ya anthu, anthu onse otsala a m’mitunduyo adzafunkha zinthu zako.+ Iwo adzateronso chifukwa unakhetsa magazi a mtundu wa anthu komanso unachitira chiwawa dziko lapansi, tauni ndi anthu onse okhala mmenemo.+  “‘Tsoka kwa munthu amene akupezera nyumba yake phindu mwachinyengo.+ Iye akuchita zimenezi kuti amange chisa chake pamalo okwezeka ndi cholinga choti tsoka lisamupeze.+ 10  Wapereka malangizo ochititsa manyazi kunyumba yako, kumene ndi kuphetsa mitundu yambiri ya anthu+ ndipo wachimwa.+ 11  Mwala wa pakhoma* udzalira mwachisoni ndipo kuchokera padenga* mtanda wa denga udzayankha.+ 12  “‘Tsoka kwa munthu amene akumanga mzinda mwa kukhetsa magazi, amenenso wakhazikitsa tauni mwa kuchita zosalungama.+ 13  Taona! Kodi si Yehova wa makamu amene adzachititsa anthu kugwira ntchito yakalavulagaga kuti moto uwononge ntchitoyo? Kodi sindiye amene wachititsa kuti mitundu ya anthu idzitopetse pachabe?+ 14  Pakuti dziko lapansi lidzadzaza ndi anthu odziwa ulemerero wa Yehova ngati mmene madzi amadzazira nyanja.+ 15  “‘Tsoka kwa amene akupatsa anzake chakumwa kuti amwe, koma atachisakaniza ndi mkwiyo ndiponso kupsa mtima kuti anzakewo aledzere+ ndipo iye aone maliseche awo.+ 16  Iwenso adzakumwetsa+ ndipo udzaonekera kuti ndiwe wosadulidwa.+ Udzakhuta zinthu zamanyazi m’malo mwa ulemerero.+ Chikho chochokera m’dzanja lamanja la Yehova chidzakupeza+ ndipo ulemerero wako udzasanduka manyazi. 17  Zidzakhala choncho chifukwa chiwawa chimene unachitira Lebanoni+ chidzafika pa iwe ndiponso chifukwa cha kuwononga kwako kwakukulu kumene unaopseza nako zilombo zakutchire, kukhetsa magazi a anthu ndi chiwawa chimene unachitira dziko lapansi,+ tauni ndi onse okhala mmenemo.+ 18  Kodi chifaniziro chosema, chifaniziro chopangidwa ndi chitsulo chosungunula ndiponso mphunzitsi wonama,+ zili ndi phindu lanji+ kuti wozipanga azizikhulupirira+ ndipo azipanga milungu yopanda pake yosalankhula?+ 19  “‘Tsoka kwa munthu amene akuuza chidutswa cha mtengo kuti: “Dzuka!” Amene amauzanso mwala wosalankhula kuti: “Dzuka! Tipatse malangizo”!+ Taona! Fanolo ndi lokutidwa ndi golide ndi siliva+ ndipo mulibe mpweya* mkati mwake.+ 20  Koma Yehova ali m’kachisi wake wopatulika.+ Inu anthu onse a padziko lapansi, khalani chete pamaso pake!’”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Ngakhale masomphenyawa ataoneka ngati akuchedwa, uziwayembekezerabe.”
Onani Zakumapeto 5.
Ena amati “chipupa” kapena “chikupa.”
Kapena kuti “patsindwi.”
Onani Zakumapeto 4.