Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 5:1-32

5  Tsopano nayi mbiri ya Adamu. M’tsiku limene Mulungu analenga Adamu, anam’panga iye m’chifaniziro cha Mulungu.+  Anawalenga iwo mwamuna ndi mkazi.+ Kenako, anawadalitsa ndi kuwatchula dzina lakuti Anthu,+ m’tsiku limene anawalenga.+  Adamu atakhala ndi moyo zaka 130, anabereka mwana wamwamuna m’chifaniziro chake, wofanana naye. Anamutcha dzina lake Seti.+  Adamu atabereka Seti, anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.+  Chotero, masiku onse amene Adamu anakhala ndi moyo anakwana zaka 930, kenako anamwalira.+  Seti atakhala ndi moyo zaka 105, anabereka Enosi.+  Atabereka Enosi, Seti anakhalabe ndi moyo zaka zina 807. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi.  Chotero, masiku onse a Seti anakwana zaka 912, kenako anamwalira.  Enosi atakhala ndi moyo zaka 90, anabereka Kenani.+ 10  Atabereka Kenani, Enosi anakhalabe ndi moyo zaka zina 815. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 11  Chotero, masiku onse a Enosi anakwana zaka 905, kenako anamwalira. 12  Kenani atakhala ndi moyo zaka 70, anabereka Mahalalele.+ 13  Atabereka Mahalalele, Kenani anakhalabe ndi moyo zaka zina 840. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 14  Chotero, masiku onse a Kenani anakwana zaka 910, kenako anamwalira. 15  Mahalalele atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Yaredi.+ 16  Atabereka Yaredi, Mahalalele anakhalabe ndi moyo zaka zina 830. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 17  Chotero, masiku onse a Mahalalele anakwana zaka 895, kenako anamwalira. 18  Yaredi atakhala ndi moyo zaka 162, anabereka Inoki.+ 19  Atabereka Inoki, Yaredi anakhalabe ndi moyo zaka zina 800. Pazaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 20  Chotero, masiku onse a Yaredi anakwana zaka 962, kenako anamwalira. 21  Inoki atakhala ndi moyo zaka 65, anabereka Metusela.+ 22  Atabereka Metusela, Inoki anayendabe ndi Mulungu woona kwa zaka 300. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 23  Chotero, masiku onse a Inoki anakwana zaka 365. 24  Inoki anayendabe+ ndi Mulungu woona.+ Kenako iye sanaonekenso, chifukwa Mulungu anam’tenga.+ 25  Metusela atakhala ndi moyo zaka 187, anabereka Lameki.+ 26  Atabereka Lameki, Metusela anakhalabe ndi moyo zaka zina 782. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 27  Chotero, masiku onse a Metusela anakwana zaka 969, kenako anamwalira. 28  Lameki atakhala ndi moyo zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29  Mwanayo anamutcha dzina lakuti Nowa,+ ndipo anati: “Uyu ndi amene adzatibweretsere mpumulo ku ntchito yathu yopweteketsa manja, chifukwa cholima nthaka imene Yehova anaitemberera.”+ 30  Atabereka Nowa, Lameki anakhalabe ndi moyo zaka zina 595. Pa zaka zimenezi, anaberekanso ana ena aamuna ndi aakazi. 31  Chotero masiku onse a Lameki anakwana zaka 777, kenako anamwalira. 32  Nowa anakwanitsa zaka 500. Pambuyo pake iye anabereka Semu,+ Hamu+ ndi Yafeti.+

Mawu a M'munsi