Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 48:1-22

48  Ndiyeno patapita nthawi Yosefe anauzidwa kuti: “Bambo anutu afooka.” Pamenepo, Yosefe anatenga ana ake awiri, Manase ndi Efuraimu,+ n’kupita kwa bambo akewo.  Ndiyeno Yakobo anauzidwa kuti: “Mwana wanu Yosefe wabwera.” Choncho Isiraeli anadzuka modzilimbitsa n’kukhala tsonga pabedi.  Tsopano Yakobo anauza Yosefe kuti: “Mulungu Wamphamvuyonse anaonekera kwa ine ku Luzi+ m’dziko la Kanani kuti andidalitse.+  Ndipo anandiuza kuti, ‘Ndidzakupatsa ana,+ ndipo mwa iwe mudzatuluka mitundu yambiri ya anthu.+ Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako kuti lidzakhale dziko lawo mpaka kalekale.’+  Tsopano ana awiri amene unabereka ku Iguputo kuno ine ndisanabwere, ndi ana anga.+ Efuraimu ndi Manase akhala ana anga monga alili Rubeni ndi Simiyoni.+  Koma ana amene udzabereke pambuyo pa anawa, amenewo adzakhala ako. Iwo adzalandira mbali ya malo amene abale awo adzalandire ngati cholowa.+  Kunena za ine, pamene ndinali kuchokera ku Padani,+ mayi ako Rakele anandifera+ panjira m’dziko la Kanani, patatsala mtunda ndithu kuti tifike ku Efurata. Zitatero, ndinawaika m’manda panjira yopita ku Efurata,+ kapena kuti Betelehemu.”+  Tsopano Isiraeli anaona ana a Yosefe, ndipo anafunsa kuti: “Kodi awa ndani?”+  Yosefe anayankha bambo akewo kuti: “Ndi ana anga amene Mulungu wandipatsa kunoko.”+ Ndiyeno bambo akewo anati: “Chonde, tawabweretsa kuno ndiwadalitse.”+ 10  Maso a Isiraeli anali atafooka chifukwa chokalamba,+ moti sankatha kuona. Yosefe anabweretsa anawo pafupi ndi bambo ake, ndipo bambo akewo anawapsompsona anawo n’kuwakumbatira.+ 11  Ndiyeno Isiraeli anauza Yosefe kuti: “Ndinalibiretu chiyembekezo choti ndidzaonanso nkhope yako,+ koma tsopano Mulungu wandilola kuona iwe limodzi ndi ana ako omwe.” 12  Atatero, Yosefe anachotsa anawo pambali pa mawondo a bambo ake. Kenako, anagwada n’kuwerama mpaka nkhope yake pansi.+ 13  Tsopano Yosefe anatenga ana ake awiriwo. Efuraimu anamuika kudzanja lake lamanja, kumanzere kwa Isiraeli.+ Ndipo Manase anamuika kudzanja lake lamanzere, kudzanja lamanja la Isiraeli.+ Atatero, anawabweretsa pafupi ndi bambo ake. 14  Koma Isiraeli anatambasula dzanja lake lamanja n’kuliika pamutu pa Efuraimu,+ ngakhale kuti ndiye anali wamng’ono.+ Anatambasulanso dzanja lake lamanzere n’kuliika pamutu pa Manase.+ Anasemphanitsa dala choncho manja ake chifukwa Manase ndiye anali mwana woyamba.+ 15  Pamenepo anadalitsa Yosefe,+ kuti: “Mulungu woona amene makolo anga Abulahamu ndi Isaki anayenda pamaso pake,+ Mulungu woona amene wakhala m’busa wanga moyo wanga wonse mpaka lero,+ 16  Mngelo amene wakhala akundiwombola ku masoka anga onse,+ adalitse anyamatawa.+ Dzina langa ndi mayina a makolo anga, Abulahamu ndi Isaki, apitirize kutchulidwa kudzela mwa anawa,+ Komanso, anawa adzachulukane, adzakhale khamu la anthu padziko lapansi.”+ 17  Yosefe ataona kuti bambo ake aika dzanja lawo lamanja pamutu pa Efuraimu, sizinamusangalatse.+ Choncho, anagwira dzanja la bambo ake kuti alichotse pamutu pa Efuraimu, n’kuliika pamutu pa Manase.+ 18  Yosefe anauza bambo ake kuti: “Ayi bambo, musatero ayi. Mwana woyamba ndi uyu.+ Ikani dzanja lanu lamanja pamutu pake.” 19  Koma bambo akewo anakanabe, kuti: “Ndikudziwa mwana wanga, ndikudziwa zimenezo. Uyunso adzakhala mtundu wa anthu, ndipo adzakhala wamkulu.+ Koma mng’ono wakeyu adzakhala wamkulu kuposa iyeyu,+ ndipo mbadwa zake zidzachuluka kwambiri n’kupanga mitundu ya anthu.”+ 20  Iye anapitiriza kuwadalitsa pa tsikulo.+ Anati: “Pogwiritsa ntchito dzina lako, Aisiraeli azidzadalitsana kuti, ‘Mulungu akudalitse monga anadalitsira Efuraimu ndi Manase.’”+ Choncho Isiraeli anaikabe Efuraimu patsogolo pa Manase.+ 21  Isiraeli atatero, anauza Yosefe kuti: “Taona, inetu ndikufa.+ Koma Mulungu adzakhalabe nanu ndithu anthu inu, ndipo adzakubwezerani kudziko la makolo anu.+ 22  Koma ine ndikukuwonjezera gawo limodzi la dziko kuposa abale ako,+ limene ndinalanda Aamori ndi lupanga langa ndi uta wanga.”

Mawu a M'munsi