Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 34:1-31

34  Dina, mwana wamkazi amene Leya+ anaberekera Yakobo, ankakonda kukacheza+ ndi ana aakazi a m’dzikolo.+  Kenako Sekemu anaona mtsikanayu. Sekemuyu anali mwana wamwamuna wa Hamori, Mhivi,+ mmodzi wa atsogoleri a m’dzikolo. Atamuona, anamutenga n’kumugwiririra.+  Atatero, nthawi zonse mtima wake unali kulakalaka Dina mwana wa Yakobo, ndipo anamukonda kwambiri m’tsikanayu, moti ankalankhula naye momunyengerera.  Potsirizira pake, Sekemu anauza bambo ake Hamori+ kuti: “Munditengere mtsikana ameneyu kuti akhale mkazi wanga.”+  Tsopano Yakobo anamva zakuti Sekemu wagwiririra mwana wake Dina. Pa nthawiyo n’kuti ana ake aamuna ali kubusa ndi ziweto zake.+ Choncho, Yakobo sananene kanthu kudikira kuti ana akewo abwere.+  Pambuyo pake, Hamori bambo ake a Sekemu, anapita kwa Yakobo kukakambirana naye.+  Koma ana a Yakobo anabwerako kubusa kuja atangomva za nkhaniyi. Nkhaniyi inawapweteketsa mtima kwambiri ndipo anakwiya koopsa,+ pakuti Sekemu anachitira Isiraeli chinthu chonyazitsa kwambiri pogona ndi mwana wa Yakobo.+ Zimenezi zinali zosayenera kuchitika m’pang’ono pomwe.+  Ndiyeno Hamori anawauza kuti: “Mwana wanga Sekemu wakonda mtsikana wanuyu ndi mtima wonse.+ Chonde, m’patseni kuti akhale mkazi wake.+  Tiyeni tichite mgwirizano wakuti tizikwatirana.+ Muzitipatsa ana anu aakazi, inunso muzitenga ana athu aakazi.+ 10  Mukhale nafe kwathu kuno, dziko lino likhalanso lanu. Mukhazikike, ndipo muzichita malonda mwaufulu.”+ 11  Pamenepo Sekemu anauza bambo ake a Dina ndi alongo ake kuti: “Ndikomereni mtima, ndikupatsani zonse zimene munganene. 12  Kwezani kwambiri ndalama za ukwati ndi mphatso zoti ndipereke,+ ndipo ndine wokonzeka kupereka zilizonse zimene munganene, malinga mundipatse mtsikanayu kuti akhale mkazi wanga.” 13  Koma ana a Yakobo anayankha Sekemu ndi bambo ake Hamori mowapita pansi. Anatero chifukwa Sekemu anali atagwiririra Dina mlongo wawo.+ 14  Kuwayankha kwake anati: “Sitingachite zimenezo. Sitingapereke mlongo wathu kwa mwamuna wosadulidwa.+ Zimenezo n’zonyazitsa kwa ife. 15  Tikulolani pokhapokha mwamuna aliyense pakati panu atadulidwa, kuti mukhale ofanana ndi ife.+ 16  Mukatero, ndithu tidzakupatsani ana athu aakazi ndipo ifenso tidzatenga ana anu aakazi. Tidzakhaladi ndi inu, ndipo tidzakhala anthu amodzi.+ 17  Koma ngati simutsatira zimene tanena zakuti mudulidwe, mwana wathu wamkaziyo tikamutenga n’kubwera naye.” 18  Mawu awowa anakondweretsa Hamori ndi mwana wake Sekemu.+ 19  Chotero mnyamatayu sanachedwe kuchita zimene anauzidwazo+ chifukwa anamukonda kwambiri mwana wa Yakobo. Sekemuyo anali wolemekezeka kwambiri+ m’nyumba yonse ya bambo ake.+ 20  Choncho Hamori ndi mwana wake Sekemu anapita kuchipata cha mzinda wawo, n’kuyamba kulankhula kwa anthu a mumzindawo+ kuti: 21  “Anthu awa n’ngofuna mtendere ndi ife.+ Ndiye aloleni akhale m’dzikoli ndi kuchitamo malonda, popeza dzikoli n’lalikulu moti atha kukhalamo.+ Tikhoza kukwatira ana awo aakazi, ndiponso tikhoza kuwapatsa ana athu aakazi.+ 22  Koma pakufunika chinthu chimodzi kuti anthuwa alole kukhala nafe limodzi n’kukhala anthu amodzi ndi ife. Akuti adzatero pokhapokha mwamuna aliyense pakati pathu atadulidwa+ ngati mmene iwonso alili. 23  Tikatero, katundu wawo, chuma chawo ndi ziweto zawo zonse sizidzakhala zathu kodi?+ Tiyeni tilolere zimene akufunazo kuti azikhala nafe.”+ 24  Chotero anthu onse otuluka pachipata cha mzindawo anamvera Hamori ndi mwana wake Sekemu, ndipo amuna onse a mumzinda wakewo anadulidwa. 25  Koma pa tsiku lachitatu, pamene anthuwo anali pa ululu,+ ana awiri a Yakobo, Simiyoni ndi Levi,+ alongo ake a Dina,+ aliyense anatenga lupanga lake n’kukalowa mumzindawo mosaonetsera cholinga chawo. Kenako anayamba kupha mwamuna aliyense.+ 26  Anaphanso Hamori ndi mwana wake Sekemu ndi lupanga.+ Kenako anatenga Dina m’nyumba ya Sekemu, n’kupita naye.+ 27  Ana ena a Yakobo anamalizitsa amuna omwe anali atapwetekedwa koopsa, n’kutenga katundu yense wa mumzindamo. Anatero chifukwa anthuwo anagwiririra mlongo wawo.+ 28  Anatenga nkhosa zawo, abulu awo ndi ziweto zina, ndi zonse zimene zinali mumzindawo, ndiponso zimene zinali kunja kwa mzindawo.+ 29  Anatenga chuma chawo chonse, ndipo ana awo onse ang’onoang’ono ndi akazi awo anawagwira ndi kupita nawo. Anatenga zonse zimene zinali m’nyumba zawo.+ 30  Yakobo ataona zimenezi anauza Simiyoni ndi Levi+ kuti: “Mwandiputira chidani, ndipo mwandinunkhitsa kwa anthu a m’dziko lino,+ Akanani ndi Aperezi. Ine ndili ndi anthu ochepa,+ ndipo iwowa ndithu asonkhana pamodzi n’kutiukira. Atithira nkhondo n’kutitha tonse, ine ndi banja langa.” 31  Koma anawo anayankha kuti: “Kodi ndi bwino kuti munthu azitenga mlongo wathu ngati hule?”+

Mawu a M'munsi