Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 28:1-22

28  Choncho, Isaki anaitana Yakobo ndipo anamudalitsa n’kumulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.+  Nyamuka, pita ku Padana-ramu kunyumba ya Betuele bambo a mayi ako. Kumeneko ukatenge mkazi pakati pa ana a Labani mlongo wa mayi ako.+  Mulungu Wamphamvuyonse adzakudalitsa. Adzakupatsa ana ndipo adzawachulukitsa moti adzakhala mitundu yambiri ya anthu.+  Adzakupatsa iwe ndi mbewu zako+ madalitso amene analonjeza Abulahamu,+ kuti udzakhale mwini dziko limene ukukhalamo ngati mlendo,+ limene Mulungu anapatsa Abulahamu.”+  Chotero Isaki anatumiza Yakobo, ndipo iye ananyamuka ulendo wopita ku Padana-ramu. Anapita kwa Labani mwana wa Betuele, Msiriya.+ Labaniyo anali mlongo wake wa Rabeka,+ mayi ake a Yakobo ndi Esau.+  Esau anaona kuti Isaki wadalitsa Yakobo, ndiponso kuti wam’tumiza ku Padana-ramu kukatenga mkazi kumeneko. Anaona kuti pomudalitsa anamulamula kuti: “Usatenge mkazi pakati pa ana aakazi a ku Kanani.”+  Anaonanso kuti Yakobo wamvera bambo ake ndi mayi ake ndipo wapita ku Padana-ramu.+  Pamenepo Esau anazindikira kuti, Isaki bambo ake, anali kuipidwa nawo ana aakazi a ku Kanani.+  Chotero Esau anapita kwa Isimaeli* n’kukatengako mkazi kuwonjezera pa akazi amene anali nawo.+ Mkaziyo dzina lake anali Mahalati, ndipo anali mlongo wake wa Nebayoti. Mahalati anali mwana wa Isimaeli, mwana wa Abulahamu. 10  Yakobo anapitiriza ulendo wake wochokera ku Beere-seba kupita ku Harana.+ 11  Kenako anafika pamalo ena n’kuganiza zogona, popeza dzuwa linali litalowa. Chotero, anatenga mwala umodzi pamalopo n’kuuchita mtsamiro, n’kugona pamenepo.+ 12  Kenako anayamba kulota.+ M’malotowo anaona makwerero ochokera pansi mpaka kumwamba. Angelo a Mulungu anali kukwera ndi kutsika pamakwereropo.+ 13  Pamwamba pa makwererowo anaonapo Yehova, amene anamuuza kuti:+ “Ine ndine Yehova, Mulungu wa Abulahamu kholo lako, ndi Mulungu wa Isaki.+ Dziko limene wagonapoli ndidzalipereka kwa iwe ndi kwa mbewu yako.+ 14  Mbewu yako ndithu idzachuluka ngati mchenga wa padziko lapansi,+ ndipo ana ako adzafalikira kumadzulo, kum’mawa, kumpoto ndi kum’mwera.+ Komanso kudzera mwa iwe ndi mwa mbewu yako, mabanja onse a padziko lapansi adzapeza madalitso*+ ndithu. 15  Ine ndili nawe ndipo ndikuyang’anira pa ulendo wako wonse, kufikira ndidzakubwezera kumalo ano.+ Sindidzakusiya kufikira nditachitadi zimene ndanena kwa iwe.”+ 16  Kenako Yakobo anagalamuka ku tulo take n’kunena kuti: “Ndithudi Yehova ali pamalo pano, koma ine sindinadziwe.” 17  Iye anachita mantha n’kunenanso kuti:+ “Malo ano ndi oopsa!+ Ndithu malo ano ndi nyumba ya Mulungu,+ ndiponso ndi khomo la kumwamba.” 18  Tsopano Yakobo anadzuka m’mawa kwambiri, n’kutenga mwala umene anautsamira uja, n’kuuimika monga mwala wachikumbutso. Atatero anauthira mafuta pamwamba.+ 19  Kenako, malowo anawatcha Beteli.+ Koma dzina lakale la mzindawo linali Luzi.+ 20  Yakobo analonjeza+ kuti: “Ndithu ngati Mulungu adzakhalabe nane n’kundisungabe pa ulendo wangawu, ndiponso ngati adzandipatsadi chakudya ndi zovala,+ 21  komanso ngati ndidzabwereradi mwamtendere kunyumba ya bambo anga, pamenepo Yehova adzakhala atasonyezadi kuti ndi Mulungu wanga.+ 22  Mwala wachikumbutso umene ndauimika panowu, udzakhala nyumba ya Mulungu.+ Pa chilichonse chimene mudzandipatsa, sindidzalephera kukubwezerani chakhumi chake.”+

Mawu a M'munsi

“Isimaeli” pano amatanthauza “Aisimaeli.” Pa nthawiyi Isimaeli anali atamwalira kale, ndipo Esau anali ndi zaka pafupifupi 77. Onani Ge 25:17, 26.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.