Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 18:1-33

18  Kenako Yehova anaonekera+ kwa Abulahamu pakati pa mitengo ikuluikulu ya ku Mamure.+ Pa nthawiyi n’kuti Abulahamu atakhala pansi pakhomo la hema wake masana dzuwa likutentha.+  Atakweza maso,+ anaona amuna atatu ataima chapatali ndi iye. Atawaona, ananyamuka pakhomo la hemayo n’kuthamanga kukakumana nawo. Atafika, anagwada n’kuwaweramira mpaka nkhope yake pansi.+  Ndiyeno anati: “Yehova, ngati mungandikomere mtima, chonde, musangondipitirira ine kapolo wanu.+  Mumweko madzi pang’ono, ndiponso tikusambitseni mapazi.+ Kenako, mupumeko pansi pa mtengo.+  Popeza mwadzera njira yodutsa kwa kapolo wanu, mundilole ndikukonzereni kachakudya kuti mutsitsimutse mitima yanu.+ Mukatero mukhoza kupitiriza ulendo wanu.” Pamenepo iwo anati: “Chabwino, chita mmene waneneramo.”  Chotero Abulahamu anathamangira kwa Sara n’kumuuza kuti: “Fulumira! Tenga ufa wosalala wokwana miyezo itatu ya seya,* uukande, ndipo upange makeke ozungulira.”+  Kenako, Abulahamu anathamangira kumene kunali ziweto, n’kutengako ng’ombe yaing’ono yamphongo yonona. Atatero, anaipereka kwa wantchito wake, ndipo iye anaikonza mwamsanga.+  Ndiyeno Abulahamu anatenga mafuta a mkaka, mkaka, ndi ng’ombe yaing’ono yamphongo imene anakonza ija, n’kukaziika pamene panali alendowo.+ Pamene iwo anali kudya atakhala pansi pa mtengo, iye anaimirira chapafupi.+  Tsopano alendowo anati: “Kodi mkazi wako Sara ali kuti?”+ Iye anayankha kuti: “Ali m’hemamu!”+ 10  Ndiyeno mmodzi wa iwo anapitiriza kuti: “Ndidzabweranso kwa iwe ndithu chaka chamawa nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara mkazi wako adzakhala ndi mwana wamwamuna.”+ Pa nthawiyi n’kuti Sara akumvetsera, ali pakhomo la hemayo. Ndipo mlendoyo anali atafulatira hemayo. 11  Abulahamu ndi Sara anali okalamba ndipo anali ndi zaka zambiri.+ Sara anali atasiya kusamba.+ 12  Chotero Sara anayamba kuseka mumtima mwake+ kwinaku akunena kuti: “Kodi mmene ndatheramu, zoona ndingakhaledi ndi chisangalalo chimenechi, komanso ndi mmene mbuyanga wakalambiramu?”+ 13  Ndiyeno Yehova anafunsa Abulahamu kuti: “N’chifukwa chiyani Sara waseka, kuti, ‘Kodi n’zoona kuti ineyo, mmene ndakalambiramu, ndingaberekedi mwana?’+ 14  Kodi pali chosatheka ndi Yehova?+ Pa nthawi yoikidwiratu ndidzabweranso kwa iwe chaka chamawa. Ndidzabweranso nthawi ngati yomwe ino, ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 15  Koma Sara pochita mantha anakana kuti: “Sindinaseketu ine ayi!” Koma mlendoyo anati: “Ayi! Unaseka iwe.”+ 16  Pambuyo pake amunawo anaimirira ndi kuyang’ana ku Sodomu,+ ndipo Abulahamu ananyamuka nawo n’kuwaperekeza.+ 17  Kenako Yehova anati: “Kodi ndingamubisire Abulahamu zimene ndikufuna kuchita?+ 18  Iyetu adzakhala mtundu waukulu ndi wamphamvu, ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzapeza madalitso* kudzera mwa iye.+ 19  Ndapalana ubwenzi ndi Abulahamu kuti aphunzitse ana ake ndi mbadwa zake kuyenda m’njira ya Yehova ndi kuchita chilungamo.+ Awaphunzitse kutero, kuti Yehova adzakwaniritse kwa Abulahamu zimene ananena zokhudza iye.”+ 20  Chotero Yehova anati: “Kudandaula kokhumudwa chifukwa cha Sodomu ndi Gomora+ kwamveka kwambiri, ndipo tchimo lawo n’lalikulu kwambiri.+ 21  Ndiye nditsikirako kuti ndikaone ngati akuchitadi monga mwa kudandaula kumene ndamva ndiponso ngati zochita zawo zilidi zoipa choncho. Ndikufuna ndidziwe zimenezi.”+ 22  Pamenepo, amunawo anatembenuka kulowera ku Sodomu, koma Yehova+ anatsala ataima ndi Abulahamu.+ 23  Ndiyeno Abulahamu anamuyandikira n’kuyamba kumufunsa kuti: “Kodi zoona mungawononge olungama pamodzi ndi oipa?+ 24  Bwanji ngati mumzindamo mutapezeka anthu olungama 50, kodi muwawonongabe? Kodi simukhululukira mzindawo chifukwa cha olungama 50 amenewo?+ 25  Simungachite zimenezo, kupha munthu wolungama limodzi ndi woipa. Sizingatheke kuti wolungama aone zofanana ndi woipa.+ Simungachite zimenezo ayi.+ Kodi Woweruza wa dziko lonse lapansi sadzachita cholungama?”+ 26  Pamenepo Yehova anayankha kuti: “Ngati ndingapeze anthu olungama 50 mu Sodomu, ndikhululukira mzinda wonsewo chifukwa cha iwo.”+ 27  Koma Abulahamu anapitiriza kuti: “Pepanitu, musaone ngati ndatha mantha kulankhula kwa Yehova pamene ndine fumbi ndi phulusa.+ 28  Nanga ngati pa olungama 50 aja pataperewera asanu, kodi muwononga mzinda wonsewo chifukwa choti paperewera anthu asanu?” Pamenepo iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo ndikapezamo olungama 45.”+ 29  Koma iye anafunsabe kuti: “Nanga mutapezeka 40?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga chifukwa cha 40 amenewo.” 30  Koma iye anapitiriza kuti: “Chonde Yehova, musandipsere mtima,+ koma ndiloleni ndilankhulebe.+ Nanga atapezeka 30?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga ndikapezamo 30.” 31  Iye anapitirizabe kuti: “Chonde, pepani musaone ngati ndatha mantha kulankhula kwa Yehova.+ Nanga mutapezeka 20?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 20 amenewo.”+ 32  Potsirizira pake anati: “Chonde Yehova, pepani, musandipsere mtima,+ tandilolani ndilankhule komaliza kokhaka.+ Nanga mutapezeka 10?” Iye anayankha kuti: “Sindiwononga mzindawo chifukwa cha 10 amenewo.”+ 33  Ndiyeno Yehova+ atamaliza kulankhula ndi Abulahamu, ananyamuka n’kumapita, ndipo Abulahamu anabwerera kunyumba kwake.

Mawu a M'munsi

Muyezo umodzi wa seya unali wokwana malita pafupifupi 8.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 12:3.