Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 15:1-21

15  Ndiyeno zimenezi zitachitika, Yehova analankhula ndi Abulamu m’masomphenya,+ kuti: “Usaope+ Abulamu. Ine ndine chishango chako.+ Mphoto yako idzakhala yaikulu kwambiri.”+  Abulamu atamva zimenezi anati: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa chiyani ine? Taonani ndilibe mwana ndipo amene adzakhale wolowa nyumba yanga ndi munthu wa ku Damasiko, Eliezere.”+  Ananenanso kuti: “Simunandipatse mbewu+ ndipo mtumiki wanga+ ndiye adzakhale wolowa nyumba yanga.”  Pamenepo Yehova anamuuza kuti: “Munthu ameneyu sadzakhala wolowa nyumba yako ayi, koma munthu amene adzatuluke mwa iwe ndi amene adzakhale wolowa nyumba yako.”+  Kenako anamutengera panja, n’kumuuza kuti: “Kweza maso ako kumwamba, uwerenge nyenyezizo ngati ungathe kuziwerenga.”+ Ndipo anamuuzanso kuti: “Umu ndi mmene mbewu yako idzakhalire.”+  Pamenepo iye anakhulupirira mwa Yehova,+ ndipo Mulunguyo anamuona Abulamu ngati wolungama.+  Anamuuzanso kuti: “Ine ndine Yehova, amene ndinakuchotsa ku Uri wa kwa Akasidi, kudzakupatsa dzikoli kuti likhale lako.”+  Ndipo iye anayankha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, nditsimikiza ndi chiyani kuti dzikoli ndidzalitengadi kukhala langa?”+  Pamenepo iye anauza Abulamu kuti: “Unditengere ng’ombe ya zaka zitatu yomwe sinaberekepo, mbuzi yaikazi ya zaka zitatu, nkhosa yamphongo ya zaka zitatu, ndiponso njiwa yaing’ono ndi mwana wa nkhunda.”+ 10  Choncho iye anatenga zonsezi n’kuzidula pakati n’kuika mbali imodzi moyang’anana ndi inzake, koma mbalamezo sanazidule.+ 11  Ndipo mbalame zodya nyama zinayamba kutera pa nyama zophedwazo.+ Koma Abulamu anali kuziingitsa. 12  Patapita nthawi, dzuwa lili pafupi kulowa, Abulamu anagona tulo tofa nato.+ Pamenepo mdima woopsa wandiweyani unayamba kufika pa iye. 13  Kenako Mulungu anauza Abulamu kuti: “Udziwe ndithu kuti mbewu yako idzakhala mlendo m’dziko la eni,+ ndipo idzatumikira eni dzikolo. Iwo adzasautsa mbewu yako kwa zaka 400.+ 14  Koma mtundu umene adzautumikirewo ndidzauweruza.+ Pambuyo pake, iwo adzachokako ndi katundu wochuluka.+ 15  Kunena za iweyo, udzatsikira kwa makolo ako mu mtendere. Udzaikidwa m’manda uli wokalamba, utakhala ndi moyo wabwino ndi wautali.+ 16  Koma m’badwo wachinayi udzabwerera kuno,+ chifukwa nthawi yoti Aamori alangidwe sinakwane.”+ 17  Tsopano dzuwa linali kulowa, ndipo kunayamba kugwa chimdima. Pamenepo, ng’anjo yofuka ndiponso muuni wamoto zinadutsa pakati pa nyama zodulidwazo.+ 18  Pa tsiku limeneli Yehova anachita pangano ndi Abulamu,+ kuti: “Dziko ili ndidzalipereka kwa mbewu yako,+ kuyambira kumtsinje wa ku Iguputo mpaka kumtsinje waukulu, mtsinje wa Firate.+ 19  Ndidzapereka kwa mbewu yako dziko la Akeni,+ Akenizi, Akadimoni, 20  Ahiti,+ Aperezi,+ Arefai,+ 21  Aamori, Akanani, Agirigasi ndi la Ayebusi.”+

Mawu a M'munsi