Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 11:1-32

11  Tsopano dziko lonse lapansi linali ndi chilankhulo chimodzi ndipo anthu anali kugwiritsa ntchito mawu ofanana.  Pamene anthuwo analowera chakum’mawa, anapeza chigwa m’dera la Sinara+ n’kukhazikika kumeneko.  Kenako anauzana kuti: “Tiyeni tiumbe njerwa tiziotche.” Atatero, anayamba kumanga ndi njerwa, n’kumagwiritsa ntchito phula ngati matope omangira.+  Ndiyeno anati: “Tiyeni timange mzinda wathuwathu, ndipo nsanja yake ikafike m’mwamba mwenimweni.+ Tikatero tidzipangira dzina loti titchuke nalo,+ ndipo sitibalalikana padziko lonse lapansi.”+  Kenako, Yehova anatsikirako kukaona mzinda ndi nsanja imene ana a anthu anali kumanga.+  Pamenepo Yehova anati: “Taonani! Izi n’zimene anthuwa ayamba kuchita popeza ndi amodzi ndipo onse ali ndi chilankhulo chimodzi.+ Mmene zililimu, angathe kuchita chilichonse chimene akuganiza.+  Choncho, tiyeni+ tipiteko kuti tikasokoneze+ chilankhulo chawo, kuti asamamvane polankhula.”+  Motero, Yehova anawabalalitsa pamalopo, kuti afalikire padziko lonse lapansi.+ Zitatero, iwo anasiya pang’onopang’ono kumanga mzindawo.+  Mzindawo unatchedwa Babele,+ chifukwa kumeneko, Yehova anasokoneza chilankhulo cha anthu onse, ndipo Yehova anabalalitsira+ anthuwo padziko lonse lapansi. 10  Tsopano iyi ndi mbiri ya Semu.+ Semu anali ndi zaka 100 pamene anabereka Aripakisadi,+ patapita zaka ziwiri pambuyo pa chigumula. 11  Atabereka Aripakisadi, Semu anakhalabe ndi moyo zaka zina 500. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi.+ 12  Aripakisadi atakhala ndi moyo zaka 35, anabereka Shela.+ 13  Atabereka Shela, Aripakisadi anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 14  Shela atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Ebere.+ 15  Atabereka Ebere, Shela anakhalabe ndi moyo zaka zina 403. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 16  Ebere atakhala ndi moyo zaka 34, anabereka Pelegi.+ 17  Atabereka Pelegi, Ebere anakhalabe ndi moyo zaka zina 430. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 18  Pelegi atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Reu.+ 19  Atabereka Reu, Pelegi anakhalabe ndi moyo zaka zina 209. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 20  Reu atakhala ndi moyo zaka 32, anabereka Serugi.+ 21  Atabereka Serugi, Reu anakhalabe ndi moyo zaka zina 207. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 22  Serugi atakhala ndi moyo zaka 30, anabereka Nahori.+ 23  Atabereka Nahori, Serugi anakhalabe ndi moyo zaka zina 200. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 24  Nahori atakhala ndi moyo zaka 29, anabereka Tera.+ 25  Atabereka Tera, Nahori anakhalabe ndi moyo zaka zina 119. Pa zaka zimenezi, anabereka ana aamuna ndi aakazi. 26  Tera anakhala ndi moyo zaka 70, kenako anabereka Abulamu,+ Nahori+ ndi Harana. 27  Tsopano iyi ndi mbiri ya Tera. Tera anabereka Abulamu, Nahori ndi Harana. Harana anabereka Loti.+ 28  Pambuyo pake Harana anamwalira mumzinda wa Akasidi+ wa Uri,+ kumene anabadwira. Anamwalira bambo ake Tera adakali ndi moyo. 29  Abulamu ndi Nahori anakwatira. Mkazi wa Abulamu anali Sarai,+ pamene mkazi wa Nahori anali Milika,+ mwana wa Harana. Harana ameneyu analinso bambo ake a Yisika. 30  Koma Sarai anali wosabereka,+ choncho analibe mwana. 31  Pambuyo pake Tera anatenga mwana wake Abulamu, mdzukulu wake+ Loti mwana wa Harana, Sarai+ mpongozi wake, mkazi wa mwana wake Abulamu, ndi kunyamuka kuchoka mumzinda wa Akasidi wa Uri, kupita kudziko la Kanani.+ Kenako, anafika ku Harana+ ndipo anakhala kumeneko. 32  Choncho masiku a Tera anakwana zaka 205. Kenako, iye anamwalira ku Harana.

Mawu a M'munsi