Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Genesis 10:1-32

10  Tsopano nayi mbiri ya ana a Nowa,+ omwe ndi Semu, Hamu ndi Yafeti. Pambuyo pa chigumula, iwowa anayamba kubereka ana.+  Ana a Yafeti anali Gomeri,+ Magogi,+ Madai,+ Yavani,+ Tubala,+ Meseke+ ndi Tirasi.+  Ana a Gomeri anali Asikenazi,+ Rifati+ ndi Togarima.+  Ana a Yavani anali Elisaha,+ Tarisi,+ Kitimu+ ndi Dodanimu.+  Kuchokera mwa amenewa, anthu anafalikira m’zilumba* m’madera awo malinga ndi zilankhulo zawo, mabanja awo ndi mitundu yawo.  Ana a Hamu anali Kusi,+ Miziraimu,+ Puti+ ndi Kanani.+  Ana a Kusi anali Seba,+ Havila, Sabita, Raama+ ndi Sabiteka. Ana a Raama anali Sheba ndi Dedani.+  Kusi anabereka Nimurodi,+ amene anali woyamba kukhala wamphamvu padziko lapansi.  Iye anakhala mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova. N’chifukwa chake pali mawu akuti: “Monga Nimurodi mlenje wamphamvu wotsutsana ndi Yehova.”+ 10  Ufumu wake unayambira ku Babele,+ Ereke,+ Akadi mpaka ku Kaline m’dziko la Sinara.+ 11  Kuchokera m’dzikoli analowera ku Asuri+ kumene anamanga Nineve,+ Rehoboti-iri, Kala, 12  komanso Resene wa pakati pa Nineve ndi Kala. Umenewu unali mzinda waukulu. 13  Miziraimu+ anabereka Ludimu,+ Anamimu, Lehabimu, Nafituhimu,+ 14  Patirusimu+ ndi Kasiluhimu+ (Afilisiti+ anachokera mwa iyeyu), ndiponso Kafitorimu.+ 15  Kanani anabereka Sidoni+ mwana wake woyamba, kenako anabereka Heti.+ 16  Anaberekanso Ayebusi,+ Aamori,+ Agirigasi, 17  Ahivi,+ Aariki, Asini, 18  Aarivadi,+ Azemari ndi Ahamati,+ ndipo pambuyo pake, mabanja a Akanani anabalalikana. 19  Choncho malire a dziko la Akanani anachokera ku Sidoni mpaka ku Gerari+ kufupi ndi Gaza,+ n’kukafika ku Sodomu ndi Gomora+ mpakanso ku Adima+ ndi Zeboyimu,+ kufupi ndi Lasa. 20  Amenewa ndiwo anali ana a Hamu monga mwa mabanja awo, monga mwa zilankhulo zawo, m’mayiko awo, mwa mitundu yawo. 21  Nayenso Semu, kholo la ana onse a Ebere,+ anali ndi mbadwa zake. Semu anali mng’ono wake wa Yafeti, amene anali wamkulu pa onse. 22  Ana a Semu anali Elamu,+ Ashuri,+ Aripakisadi,+ Ludi ndi Aramu. 23  Ana a Aramu anali Uzi, Huli, Geteri ndi Masi.+ 24  Aripakisadi anabereka Shela+ ndipo Shela anabereka Ebere. 25  Ebere anabereka ana awiri. Wina dzina lake anali Pelegi,*+ chifukwa m’masiku ake, dziko lapansi linagawikana.+ M’bale wakeyo dzina lake anali Yokitani.+ 26  Yokitani anabereka Alamodadi, Selefi, Hazaramaveti, Yera,+ 27  Hadoramu, Uzali, Dikila,+ 28  Obali, Abimaele, Sheba,+ 29  Ofiri,+ Havila+ ndi Yobabi.+ Onsewa anali ana a Yokitani. 30  Dziko lawo limene anali kukhala linayambira ku Mesa mpaka ku Sefara, dera lamapiri la Kum’mawa. 31  Amenewa ndiwo ana a Semu monga mwa mabanja awo, zilankhulo zawo, m’mayiko awo, monga mwa mitundu yawo.+ 32  Amenewa ndiwo mabanja a ana a Nowa monga mwa mibadwo yawo, monganso mwa mitundu yawo. Ndipo kuchokera mwa iwowa, mitundu inafalikira padziko lapansi pambuyo pa chigumula.+

Mawu a M'munsi

Mawu omasuliridwa kuti “zilumba” pano kwenikweni amatanthauza madera a m’mphepete mwa nyanja.
Dzina lakuti “Pelegi” limatanthauza “Kugawika” ndiponso “Mfuleni.”