Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 6:1-14

6  Yehova anapitiriza kulankhula nane, kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kumapiri a Isiraeli ndipo ulosere+ kwa iwo.+  Unene kuti, ‘Inu mapiri a Isiraeli, imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa:+ Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kwa mapiri, zitunda,+ mitsinje ndi zigwa: “Ine ndidzakubweretserani lupanga ndipo ndidzawononga malo anu okwezeka.+  Maguwa anu ansembe adzasiyidwa.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzaphwanyidwa, ndipo anthu anu ophedwa ndidzawagwetsera pamaso pa mafano anu onyansa.*+  Ndidzaika mitembo ya ana a Isiraeli pamaso pa mafano awo onyansa, ndipo mafupa anu ndidzawamwaza kuzungulira maguwa anu ansembe.+  M’malo anu onse okhala,+ mizinda idzawonongedwa+ ndipo malo okwezeka adzasakazidwa kuti akhale mabwinja ndiponso kuti maguwa anu ansembe akhale osakazidwa.+ Chotero maguwa anu ansembewo adzaphwanyidwa+ ndipo mafano anu onyansa sadzakhalaponso.+ Maguwa anu ofukizirapo zonunkhira adzagwetsedwa+ ndipo ntchito za manja anu zidzafafanizidwa.  Mitembo ya anthu ophedwa a mtundu wanu idzakhala pakati panu,+ ndipo inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+  “‘“Zimenezi zikadzachitika, ndidzachititsa kuti ena a inu asaphedwe ndi lupanga pakati pa mitundu ya anthu, mukadzamwazikana kupita kumayiko osiyanasiyana.+  Opulumuka anu akadzagwidwa n’kutengedwa kukakhala pakati pa mitundu ina ya anthu, ndithu adzandikumbukira.+ Adzakumbukira mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha mtima wawo wadama umene unawachititsa kundipandukira.+ Adzakumbukiranso mmene ndinamvera kupweteka chifukwa cha maso awo othamangira mafano awo onyansa pofuna kuchita nawo zadama.+ Iwo adzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zawo, chifukwa cha zinthu zonse zoipa ndi zonyansa zimene anachita.+ 10  Ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. Sikuti ndangonena pachabe+ zoti ndidzawabweretsera tsoka limeneli.”’+ 11  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ombani m’manja+ ndipo pondani pansi mwamphamvu ndi mapazi anu. Munene kuti: “Kalanga ine!” chifukwa cha zoipa zonse zonyansa za nyumba ya Isiraeli.+ Pakuti iwo adzaphedwa ndi lupanga,+ njala+ ndi mliri.+ 12  Yemwe ali kutali+ adzaphedwa ndi mliri. Yemwe ali pafupi adzaphedwa ndi lupanga. Yemwe watsala ali wotetezeka adzafa ndi njala, ndipo ukali wanga ndidzauthetsera pa iwo.+ 13  Iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Adzadziwa zimenezi mitembo ya anthu awo ikadzakhala pakati pa mafano awo onyansa+ kuzungulira maguwa awo onse ansembe,+ paphiri lililonse lalitali,+ pansonga zonse za mapiri,+ pansi pa mtengo uliwonse waukulu wamasamba obiriwira,+ ndiponso pansi pa mtengo uliwonse waukulu wanthambi zambiri.+ Amenewa ndiwo malo amene anali kuperekerapo nsembe zafungo lokhazika mtima pansi kwa mafano awo onse onyansa.+ 14  Ndidzawatambasulira dzanja langa powalanga+ ndipo dziko lawo ndidzalisandutsa bwinja. Malo awo onse okhala adzakhala bwinja loipa kuposa chipululu cha Dibula, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Mawu amene anawagwiritsa ntchito m’mipukutu yoyambirira pa mawu akuti “onyansa” amatanthauza “ndowe.”