Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 5:1-17

5  “Iwe mwana wa munthu, tenga lupanga lakuthwa. Likhale ngati lezala lako lometela ndipo umetele tsitsi lako ndi ndevu zako. Kenako utenge sikelo yoyezera ndipo ugawe tsitsilo m’magawo atatu.  Gawo limodzi la magawo atatu a tsitsilo ulitenthe pamoto pakati pa mzindawo masiku ozungulira mzindawo akatha.+ Kenako utenge gawo lina la magawo atatuwo. Gawo limeneli uzilimenya ndi lupanga ukuzungulira mzinda wonsewo.+ Gawo lomaliza la magawo atatuwo uliuluze ndi mphepo ndipo ine ndidzalitsatira nditasolola lupanga.  “Pagawo lachitatuli utengepo tsitsi lochepa n’kulikulunga m’zovala zako.+  Utengeponso tsitsi lina n’kuliponya pamoto kuti linyeke. Kuchokera pamoto umenewu, padzabuka moto umene udzafalikire kunyumba yonse ya Isiraeli.+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Uyu ndi Yerusalemu. Ndamuika pakati pa mitundu ya anthu ndipo wazunguliridwa ndi mayiko ena.  Iye anapandukira zigamulo zanga pochita zoipa zoposa za mitundu ya anthuwo. Anapandukiranso malamulo anga kuposa mayiko amene amuzungulira, pakuti iye anakana zigamulo zanga ndipo sanayende m’malamulo anga.’  “Chotero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti anthu inu munali ovuta kuposa mitundu imene yakuzungulirani, ndipo simunayende m’malamulo anga, komanso simunatsatire zigamulo zanga,+ koma munatsatira zigamulo za mitundu imene yakuzungulirani,  izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena: “Ine ndithana nawe mzinda iwe,+ ndipo ndidzapereka zigamulo pakati pako pamaso pa mitundu ya anthu.  Chifukwa cha zonyansa zako zonse, ndidzakuchita zimene sindinachitepo ndiponso zimene sindidzachitanso.+ 10  “‘“Choncho pakati pako, abambo adzadya ana awo ndipo ana adzadya abambo awo. Ine ndidzakulanga ndipo anthu ako onse otsala ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi.”’ 11  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pali ine Mulungu wamoyo, chifukwa chakuti iwe unaipitsa malo anga opatulika ndi mafano ako onse onyansa ndi zinthu zako zonse zonyansa, ndithu ineyo ndidzakuchepetsa.+ Diso langa silidzakumvera chisoni ndipo sindidzakuchitira chifundo.+ 12  Gawo limodzi la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzafa ndi mliri+ ndipo adzatha ndi njala pakati pako.+ Gawo lina la magawo atatu a anthu a mtundu wako adzaphedwa ndi lupanga mokuzungulira. Gawo lomaliza la magawo atatu a anthu a mtundu wako ndidzawabalalitsira kumphepo zonse zinayi,+ ndipo ndidzawatsatira nditasolola lupanga. 13  Ndiyeno mkwiyo wanga udzatha+ ndipo ukali wanga ndidzauthetsera pa iwo.+ Kenako mtima wanga udzakhala pansi. Ndikadzathetsera ukali wanga pa iwo, pamenepo iwo adzadziwa kuti ine Yehova ndalankhula chifukwa ndimafuna kuti anthu azidzipereka kwa ine ndekha basi. 14  “‘Iweyo ndidzakusandutsa malo abwinja. Ndidzakusandutsanso chitonzo pakati pa mitundu yokuzungulira ndi pamaso pa munthu aliyense wodutsa. 15  Udzakhala chitonzo+ ndi chinthu chochilankhulira mawu onyoza.+ Udzakhalanso chenjezo+ ndi choopsezera mitundu yokuzungulira ndikadzakuweruza mokwiya komanso mwaukali, ndiponso ndikadzakulanga mokwiya.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi. 16  “‘Ndikadzakutumizirani mivi yakupha yobweretsa njala+ imene idzakuwonongeni, ndidzachititsa kuti njala ikule pakati panu, ndipo ndidzathyola ndodo zimene mumakolowekapo mikate yozungulira yoboola pakati. 17  Ndidzakutumizirani njala ndi zilombo zakupha ndipo zidzakupherani ana anu. Mliri+ ndi magazi+ zidzadutsa pakati panu ndipo ine ndidzakubweretserani lupanga.+ Ineyo Yehova ndi amene ndanena zimenezi.’”

Mawu a M'munsi