Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 30:1-26

30  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, losera kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Fuulani anthu inu kuti, ‘Kalanga ine! Tsiku lija layandikira.’+  Tsikulo lili pafupi. Inde tsiku la Yehova lili pafupi.+ Limeneli lidzakhala tsiku la mitambo,+ ndiponso nthawi yoikidwiratu yoti mitundu ya anthu iweruzidwe.+  Lupanga lidzafikadi mu Iguputo,+ ndipo ku Itiyopiya anthu adzamva ululu waukulu. Izi zidzachitika anthu akadzaphedwa mu Iguputo, chuma cha dzikolo chikadzalandidwa komanso maziko ake akadzagwetsedwa.+  Itiyopiya,+ Puti,+ Ludi, anthu onse ochokera ku mitundu ina,+ Kubi ndi anthu ochokera m’dziko la Isiraeli amene ali m’pangano, onsewa adzaphedwa ndi lupanga pamodzi ndi Aiguputo.”’+  “Yehova wanena kuti, ‘Nawonso othandiza Iguputo adzaphedwa, ndipo mphamvu zimene amazinyadira zidzatha.’+ “‘Kuchokera ku Migidoli mpaka ku Seyene,+ anthu adzaphedwa ndi lupanga m’dzikolo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  ‘Onsewo adzakhala mabwinja pakati pa mayiko omwe simukukhalanso anthu ndipo mizinda yake idzakhala pakati pa mizinda yowonongedwa.+  Ndikadzayatsa moto mu Iguputo, ndipo onse omuthandiza akadzawonongedwa, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.+  Pa tsikulo, amithenga ochokera kwa ine adzakwera zombo kuti akaopseze Itiyopiya yemwe ndi wodzidalira.+ Itiyopiya adzamva ululu woopsa pa tsiku limene Iguputo adzawonongedwe, pakuti tsikulo lidzafika ndithu.’+ 10  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononga khamu la ku Iguputo pogwiritsa ntchito dzanja la Nebukadirezara, mfumu ya Babulo.+ 11  Mfumuyo ndi anthu ake, olamulira ankhanza a mitundu ina ya anthu,+ akubwera kudzawononga dzikolo kuti likhale bwinja. Iwo adzasolola malupanga awo kumenyana ndi Iguputo ndipo adzadzaza dzikolo ndi anthu ophedwa.+ 12  Ndidzaumitsa ngalande zotuluka mumtsinje wa Nailo+ ndi kugulitsa dzikolo kwa anthu oipa.+ Ndidzachititsa kuti dzikolo ndi zonse zimene zili mmenemo ziwonongedwe ndi anthu achilendo.+ Ine Yehova, ndanena zimenezi.’+ 13  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndidzawononganso mafano onyansa+ ndi kuthetsa milungu yopanda pake ku Nofi.+ Sipadzapezekanso mtsogoleri wochokera m’dziko la Iguputo, ndipo ndidzachititsa anthu a m’dzikolo kukhala mwamantha.+ 14  Mzinda wa Patirosi ndidzausandutsa bwinja. Mzinda wa Zowani ndidzautentha ndi moto ndipo ndidzapereka ziweruzo mumzinda wa No.+ 15  Ndidzatsanulira mkwiyo wanga+ pa Sini, malo otetezedwa kwambiri a Iguputo, ndipo ndidzapha khamu la anthu a ku No.+ 16  Ndidzayatsa moto mu Iguputo. Sini adzamva ululu waukulu, No adzalandidwa ndi adani amene adzagumule mpanda wake. Adani adzalowa mumzinda wa Nofi masanasana. 17  Anyamata a ku Oni+ ndi ku Pibeseti adzaphedwa ndi lupanga. Anthu a m’mizinda imeneyi adzatengedwa kupita ku ukapolo. 18  Mumzinda wa Tahapanesi+ mudzagwa mdima masana ndikadzathyola magoli a Iguputo kumeneko.+ Mphamvu zimene amazinyadira zidzathetsedwa.+ Iye adzakutidwa ndi mitambo+ ndipo anthu a m’mizinda yake yozungulira adzatengedwa kupita ku ukapolo.+ 19  Ndidzapereka ziweruzo mu Iguputo+ ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’” 20  Ndiyeno m’chaka cha 11, m’mwezi woyamba, pa tsiku la 7 la mweziwo, Yehova analankhulanso ndi ine kuti: 21  “Iwe mwana wa munthu, ine ndidzathyola dzanja la Farao mfumu ya Iguputo.+ Dzanjalo silidzamangidwa ndi nsalu zomangira pachilonda+ kuti lichire n’kukhalanso lamphamvu kuti lizidzatha kugwira lupanga.” 22  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndithana ndi Farao mfumu ya Iguputo.+ Ndidzathyola manja ake onse,+ dzanja lamphamvu ndi lothyoka lija, ndipo ndidzachititsa kuti lupanga ligwe m’dzanja lake.+ 23  Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu ndi kuwamwazira kumayiko ena.+ 24  Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo+ ndipo ndidzaipatsa lupanga langa. Ndidzathyola manja a Farao ndipo adzabuula kwambiri pamaso pa mfumu ya Babulo monga wovulazidwa koopsa.+ 25  Ndidzalimbitsa manja a mfumu ya Babulo ndipo Farao adzagwetsa manja ake. Ndikadzapereka lupanga langa m’manja mwa mfumu ya Babulo, iye n’kuligwiritsa ntchito pomenyana ndi dziko la Iguputo, iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova. 26  Ine ndidzabalalitsira Aiguputo ku mitundu ina ya anthu+ ndi kuwamwazira kumayiko ena, ndipo iwo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”

Mawu a M'munsi