Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 3:1-27

3  Iye anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya chimene chili pamaso pakochi. Idya mpukutuwu,+ kenako upite kukalankhula ndi nyumba ya Isiraeli.”  Pamenepo ndinatsegula pakamwa panga, ndipo iye anandipatsa mpukutuwo kuti ndidye.+  Kenako anandiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, idya mpukutu umene ndikukupatsawu, kuti mimba yako ikhute ndiponso kuti mpukutuwo udzaze m’matumbo mwako.” Choncho ndinayamba kudya mpukutuwo, ndipo unali wotsekemera* ngati uchi m’kamwa mwanga.+  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, pita pakati pa nyumba+ ya Isiraeli ndipo ukawauze mawu anga.  Pakuti sindikukutuma kwa anthu olankhula chinenero chovuta kumva+ ndiponso a lilime lolemera.+ Koma ndikukutuma kunyumba ya Isiraeli,  osati kwa mitundu yambiri ya anthu olankhula chinenero chovuta kumva kapena a lilime lolemera, amene sungathe kumvetsetsa mawu awo.+ Ndikanakhala kuti ndinakutuma kwa anthu amenewo, akanakumvera.+  Koma a nyumba ya Isiraeli sakafuna kukumvera, chifukwa iwo safuna kundimvera.+ Pakuti anthu onse a nyumba ya Isiraeli ndi amakani ndi osamva.+  Koma ndachititsa nkhope yako kuti ikhale yolimba mofanana ndi nkhope zawo,+ ndiponso chipumi chako kuti chikhale cholimba mofanana ndi zipumi zawo.+  Ndachititsa chipumi chako kukhala ngati mwala wa dayamondi, cholimba kuposa mwala wa nsangalabwi.+ Usawaope,+ ndipo usachite mantha ndi nkhope zawo,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.”+ 10  Iye anapitiriza kundiuza kuti: “Iwe mwana wa munthu, usunge mumtima mwako mawu anga onse amene ndikukuuza,+ ndipo umve ndi makutu ako. 11  Pita pakati pa anthu otengedwa ukapolo,+ pakati pa ana a anthu a mtundu wako, ndipo ukawauze kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena,’ kaya akamve kapena ayi.”+ 12  Kenako mzimu unanditenga+ ndipo kumbuyo kwanga ndinayamba kumva mawu amphamvu ngati chimkokomo chachikulu,+ akuti: “Utamandike ulemerero wa Yehova kumalo ake.”+ 13  Kenako ndinamva phokoso la mapiko a zamoyo amene anali kukhulana pafupipafupi.+ Ndinamvanso phokoso la mawilo amene anali pambali pawo,+ ndi chimkokomo chachikulu. 14  Mzimu unandinyamula+ moti ndinapita ndili wachisoni ndi wokwiya kwambiri mumtima mwanga, ndipo dzanja la Yehova linandigwira mwamphamvu.+ 15  Chotero ndinapita kwa anthu otengedwa ukapolo amene anali ku Tele-abibu, amene anali kukhala+ pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Ndinayamba kukhala pamalo pamene anthuwo anali kukhala ndipo ndinakhala pamenepo masiku 7. Ndinangokhala phee pakati pawo, ndili m’maganizo.+ 16  Pamapeto pa masiku 7, Yehova analankhula nane, kuti: 17  “Iwe mwana wa munthu, ine ndakuika kuti ukhale mlonda wa nyumba ya Isiraeli.+ Umve mawu ochokera pakamwa panga ndipo undichenjezere anthuwo.+ 18  Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Udzafa ndithu,’+ iwe osamulankhula munthu woipayo ndi kumuchenjeza kuti asiye njira yake yoipa n’cholinga choti akhalebe ndi moyo,+ iyeyo poti ndi woipa adzafa chifukwa cha zolakwa zake,+ koma magazi ake ndidzawafuna kuchokera m’manja mwako.+ 19  Koma iweyo ukachenjeza munthu woipa,+ koma iye osasiya zoipa zakezo ndi njira zake zoipa, munthuyo adzafa chifukwa cha zoipa zake.+ Koma iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.+ 20  Munthu wolungama akasiya chilungamo chake+ n’kumachita zinthu zopanda chilungamo, ine n’kumuikira chopunthwitsa pamaso pake,+ iyeyo adzafa chifukwa chakuti sunamuchenjeze. Adzafa chifukwa cha tchimo lake+ ndipo zinthu zolungama zimene anachita sizidzakumbukiridwa,+ koma magazi ake ndidzawafuna kwa iweyo.+ 21  Koma ngati iweyo unachenjeza munthu wolungama kuti asachimwe,+ iye osachimwadi, munthuyo adzakhalabe ndi moyo chifukwa anachenjezedwa,+ ndipo iweyo udzakhala utapulumutsa moyo wako.”+ 22  Kenako dzanja la Yehova linafika pa ine kumeneko ndipo iye anandiuza kuti: “Nyamuka, pita kuchigwa+ ndipo ndikalankhula nawe kumeneko.” 23  Chotero ndinanyamuka n’kupita kuchigwako. Kumeneko ndinangoona kuti ulemerero wa Yehova waimirira,+ ngati ulemerero umene ndinauona pafupi ndi mtsinje wa Kebara.+ Nditaona zimenezo, ndinagwada n’kuwerama mpaka nkhope yanga pansi.+ 24  Kenako mzimu unalowa mwa ine+ n’kundiimiritsa,+ ndipo Mulungu anayamba kulankhula nane, kuti: “Pita ukadzitsekere m’nyumba mwako. 25  Tsopano iwe mwana wa munthu, dziwa kuti adzakumanga ndi zingwe kuti usapite pakati pawo.+ 26  Ndidzachititsa lilime lako kumatirira kumwamba m’kamwa mwako,+ ndipo sudzathanso kulankhula.+ Sudzakhalanso munthu wowadzudzula,+ pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+ 27  Ndikamalankhula nawe ndizikutsegula pakamwa. Ndiyeno iweyo uzikawauza kuti,+ ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena.’ Wakumva amve,+ ndipo wosamva asamve, pakuti iwo ndi nyumba yopanduka.+

Mawu a M'munsi

Ena amati “wonzuna.”