Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 26:1-21

26  M’chaka cha 11, pa tsiku loyamba la mwezi, Yehova analankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, Turo+ wanena Yerusalemu+ kuti, ‘Eyaa! Zakhala bwino! Mzindawo wathyoledwa.+ Mzinda umene unali kukopa anthu a mitundu ina+ wathyoledwa. Tsopano ine zinthu zindiyendera bwino. Ndilemera chifukwa mzindawo wawonongedwa.’+  Pa chifukwa chimenechi, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mitundu yambiri ya anthu+ kuti idzamenyane nawe. Anthuwo adzabwera ngati mafunde a m’nyanja.+  Mitunduyo idzagwetsa mpanda wa Turo+ ndi kugumula nsanja zake.+ Ine ndidzapala fumbi lake n’kumusandutsa malo osalala opanda kanthu kalikonse, apathanthwe.  Iye adzakhala malo oyanikapo makoka+ pakati pa nyanja.’+ “‘Ine ndanena, anthu a mitundu ina adzalanda zinthu zake,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.  ‘Anthu a m’midzi yake yozungulira imene ili kunja kwa mzindawo adzaphedwa ndi lupanga, ndipo anthu adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ine ndidzatumiza Nebukadirezara mfumu ya Babulo, mfumu ya mafumu,+ kuchokera kumpoto+ kuti akaukire Turo. Iye adzapita ndi mahatchi,+ magaleta ankhondo,+ asilikali a pamahatchi, khamu la anthu+ kapena kuti gulu lalikulu la anthu.  Anthu okhala m’midzi yozungulira imene ili kunja kwa mzindawu adzawapha ndi lupanga. Iwo adzakumangira mpanda womenyerapo nkhondo ndi chiunda chomenyerapo nkhondo,+ ndipo adzadziteteza ndi chishango chachikulu.  Mfumuyo idzagumula mpanda wako ndi chida chogumulira, ndipo idzagwetsa nsanja zako ndi zida zake. 10  Fumbi limene chikhamu cha mahatchi ake chidzachite lidzakufotsera.+ Mpanda wako udzagwedezeka chifukwa cha phokoso la asilikali a pamahatchi ndi mawilo a magaleta ankhondo. Izi zidzachitika iye akamadzalowa m’zipata zako ngati mmene zimakhalira polowa mumzinda umene mpanda wake augumula. 11  Ziboda za mahatchi ake zidzapondaponda m’misewu yako yonse.+ Iye adzapha anthu ako ndi lupanga ndipo zipilala zako zolimba zidzagwa. 12  Iwo adzakulanda chuma chako+ ndi malonda ako.+ Adzagwetsa mpanda wako ndi nyumba zako zosiririka. Miyala yako, zinthu zako zamatabwa ndi fumbi lako, adzaziponya m’madzi.’ 13  “‘Ndidzathetsa phokoso la kuimba kwako+ ndipo phokoso la azeze ako silidzamvekanso.+ 14  Ndidzakusandutsa malo osalala apathanthwe lopanda kanthu.+ Udzakhala malo oyanikapo makoka.+ Iwe sudzamangidwanso, pakuti ine Yehova ndanena,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.+ 15  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wauza mzinda wa Turo kuti, ‘Kodi zilumba sizidzagwedezeka chifukwa cha phokoso la kuwonongedwa kwako, kubuula kwa anthu ovulazidwa koopsa, ndi kuphedwa kwa anthu ako ambiri?+ 16  Atsogoleri onse a kunyanja adzatsika+ m’mipando yawo yachifumu+ ndi kuvula malaya awo akunja odula manja. Adzavula zovala zawo za nsalu yopeta. Iwo adzavala zovala zonjenjemeretsa. Adzakhala padothi+ ndipo nthawi zonse azidzanjenjemera+ ndi kukuyang’anitsitsa modabwa. 17  Iwo adzakuimbira nyimbo yoimba polira.+ Azidzati: “‘“Iwe mzinda wotamandika, zoona wawonongekadi! Mwa iwe munali kukhala anthu ochokera kunyanja.+ Unali wamphamvu panyanja.+ Iwe ndi anthu ako munali kuchititsa mantha anthu onse okhala padziko lapansi. 18  Pa tsiku la kuwonongedwa kwako, zilumba zidzanjenjemera. Zilumba za m’nyanja zidzasokonezeka chifukwa cha kuwonongedwa kwako.”’+ 19  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndikadzakusandutsa mzinda wabwinja ngati mizinda imene simukukhala anthu, ndikadzakubweretsera madzi ambiri, ndipo madzi ochulukawo akadzakumiza,+ 20  ndidzakutsitsira m’dzenje, ngati mmene ndinatsitsira ena onse m’manda momwe muli anthu amene anafa kalekale.+ Ine ndidzakuchititsa kukhala pansi, panthaka.+ Udzakhala kumeneko pamodzi ndi malo ena amene anawonongedwa kalekale ndiponso pamodzi ndi ena onse amene akutsikira kumanda.+ Ndidzachita zimenezi kuti anthu asadzakhalenso mwa iwe, koma m’dziko la anthu amoyo ndidzaikamo zokongoletsera.+ 21  “‘Ndidzakugwetsera zoopsa modzidzimutsa+ ndipo sudzakhalaponso. Anthu adzakufunafuna+ koma sudzapezeka mpaka kalekale,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi