Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 25:1-17

25  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana kwa ana a Amoni ndipo ulosere zoipa zimene zidzawachitikire.+  Uuze ana a Amoniwo kuti, ‘Imvani mawu a Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Chifukwa chakuti malo anga opatulika adetsedwa, inu mwanena kuti: Eyaa! Zakhala bwino! Mwaneneranso zimenezi dziko la Isiraeli chifukwa chakuti lakhala bwinja, komanso nyumba ya Yuda chifukwa chakuti anthu ake atengedwa ukapolo.+  Pa chifukwa chimenechi, ndikuperekani kwa anthu a Kum’mawa kuti mukhale chuma chawo.+ Iwo adzamanga misasa yokhala ndi mipanda ndiponso mahema awo m’dziko lanu. Adzadya zokolola zanu ndi kumwa mkaka wanu.+  Mzinda wa Raba+ ndidzausandutsa malo odyetserako ngamila, ndipo dziko la ana a Amoni ndidzalisandutsa malo opumulirako gulu la nkhosa.+ Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti munawomba m’manja+ ndi kuponda pansi mwamphamvu, komanso munasangalala ndi mtima wonyoza poona zimene zinachitikira dziko la Isiraeli,+  ine ndakutambasulirani dzanja langa,+ ndipo ndidzakuperekani kwa mitundu ina ya anthu monga zofunkha. Ndidzakuphani ndi kukuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu ndi kukuwonongani kuti musapezekenso m’dziko.+ Ndidzakufafanizani,+ ndipo mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza kuti Mowabu+ ndi Seiri+ anena kuti: “Taonani! Nyumba ya Yuda ili ngati mitundu ina yonse ya anthu,”+  ine ndidzaonetsa adani awo malo otsetsereka a ku Mowabu. Kumalo amenewa ndi kumene kuli mizinda ya m’malire a dzikolo. Mizinda yake ndi Beti-yesimoti,+ Baala-meoni+ ndi Kiriyataimu.+ Mizinda imeneyi imakongoletsa dzikolo. 10  Ndidzapereka Mowabu limodzi ndi ana a Amoni+ kwa anthu a Kum’mawa+ kuti akhale chuma chawo. Ndidzachita izi kuti ana a Amoni asadzakumbukiridwenso+ pakati pa mitundu ya anthu. 11  Ndidzapereka chiweruzo m’dziko la Mowabu,+ ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+ 12  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti Edomu walanga nyumba ya Yuda ndipo akupitiriza kuilanga ndi kuichitira zinthu zoipa kwambiri,+ 13  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndidzatambasulira Edomu+ dzanja langa ndi kupha anthu ndi ziweto m’dzikolo.+ Ndidzalisandutsa bwinja kuyambira ku Temani+ mpaka ku Dedani.+ Iwo adzaphedwa ndi lupanga. 14  ‘Ine ndidzalanga Edomu kudzera mwa anthu anga Aisiraeli.+ Aisiraeliwo adzachitira Edomu mogwirizana ndi mkwiyo komanso ukali wanga, ndipo Aedomuwo adzadziwa mmene ndimalangira,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’ 15  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Afilisiti achitira zoipa+ Aisiraeli ndipo akupitiriza kuwachitira zoipazo. Mumtima mwawo akusangalala ndiponso kuwanyoza. Akuchita zimenezi kuti awawononge+ chifukwa cha chidani chawo chomwe chidzakhalepo mpaka kalekale.+ 16  Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikutambasula dzanja langa kuti ndilange Afilisiti,+ ndipo ndidzapha Akereti+ ndi kuwononga anthu onse okhala m’mbali mwa nyanja.+ 17  Anthu amenewa ndidzawalanga kwambiri ndi kuwadzudzula mwaukali,+ ndipo ndikadzawalanga adzadziwa kuti ine ndine Yehova.”’”+

Mawu a M'munsi