Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 23:1-49

23  Yehova anapitiriza kulankhula nane+ kuti:  “Iwe mwana wa munthu, panali akazi awiri, ana aakazi obadwa kwa mayi mmodzi.+  Akazi amenewa anayamba kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ Anayamba uhule umenewu ali atsikana ang’onoang’ono.+ Kumeneko amuna anafinya mabere awo+ ndi kutsamira chifuwa chawo ali anamwali.  Wamkulu dzina lake anali Ohola, wamng’ono anali Oholiba. Akazi amenewa anakhala anga+ ndipo anabereka ana aamuna ndi aakazi.+ Ohola akuimira Samariya+ ndipo Oholiba akuimira Yerusalemu.+  “Ohola anayamba kuchita uhule+ ngakhale kuti anali mkazi wanga. Anali kulakalaka kwambiri amuna amene ankakhumba kugona naye.+ Anali kulakalaka Asuri+ amene anali kukhala moyandikana naye.  Anali kulakalaka abwanamkubwa ovala zovala zabuluu ndiponso ankalakalaka atsogoleri. Onsewa anali anyamata osiririka, asilikali okwera pamahatchi.  Iye anapitiriza kuchita zauhule zakezo ndi amuna onse osankhidwa a ku Asuri. Anadziipitsa ndi amuna onse amene anawakhumba ndiponso ndi mafano awo onyansa.+  Iye sanasiye zauhule zake zimene anachokera nazo ku Iguputo. Aiguputowo anagona naye kuyambira ali kamtsikana. Iwo ndiwo anatsamira chifuwa chake ali namwali ndipo anali kuchita naye zachiwerewere.+  Choncho ndinam’pereka m’manja mwa amuna amene anali kukhumba kugona naye.+ Ndinam’pereka m’manja mwa ana aamuna a ku Asuri amene iye anali kuwakhumba.+ 10  Amuna amenewa ndiwo amene anamuvula.+ Iwo anatenga ana ake aamuna ndi aakazi+ ndipo iyeyo anamupha ndi lupanga. Iye anatchuka ndi khalidwe loipa pakati pa akazi ena ndipo iwo anamuweruza. 11  “Mng’ono wake Oholiba ataona zimenezi,+ anayamba kukonda chiwerewere chodziwononga nacho kuposa mkulu wake. Anayamba kuchita uhule kuposa dama la mkulu wake.+ 12  Iye anali kulakalaka kwambiri ana aamuna a ku Asuri.+ Anali kulakalaka abwanamkubwa ndi atsogoleri amene anali kukhala moyandikana naye. Amuna onsewa anali ovala mwaulemerero, asilikali okwera pamahatchi komanso anyamata osiririka.+ 13  Oholiba atadziipitsa, ine ndinaona kuti akazi onsewa anali ndi khalidwe lofanana.+ 14  Iye anawonjezera zochita zake zauhule ataona zithunzi za amuna zogoba pakhoma,+ zithunzi+ za Akasidi zopaka utoto wofiira,+ 15  zithunzi za amuna ovala malamba m’chiuno,+ ndiponso ovala nduwira zazitali zolendewera kumutu kwawo. Amuna onsewo anali kuoneka ngati ankhondo, komanso ngati ana aamuna a ku Babulo, obadwira m’dziko la Kasidi. 16  Ataona zithunzizo, anayamba kukhumba kwambiri amunawo+ ndipo anatumiza anthu ku Kasidi kuti akawaitane.+ 17  Ana aamuna a ku Babulowo anali kubwera kwa iye. Anali kupita kubedi lake lochitirapo zachikondi ndi kumuipitsa ndi chiwerewere chawo.+ Iye anapitiriza kuipitsidwa ndi amunawo kenako ananyansidwa nawo n’kuwasiya. 18  “Oholiba anayamba kuchita uhule modzionetsera ndipo anali kudzivula,+ moti ine ndinasiya kukhala naye chifukwa chonyansidwa naye, monga mmene ndinasiyira mkulu wake chifukwa chonyansidwa naye.+ 19  Oholiba anapitiriza kuwonjezera zochita zake zauhule+ mpaka kufika pokumbukira masiku amene anali kamtsikana,+ pamene anali kuchita uhule m’dziko la Iguputo.+ 20  Iye anali ndi chilakolako champhamvu ngati cha adzakazi* amene amuna awo ali ndi ziwalo ngati za abulu amphongo, amuna amene mpheto zawo zili ngati mpheto za mahatchi amphongo.+ 21  Iwe Oholiba, unapitiriza kulakalaka khalidwe lotayirira la pa utsikana wako mwa kufunafuna njira zoti amuna atsamire pachifuwa chako, kuyambira pamene unali ku Iguputo+ mpaka m’tsogolo. Unachita izi kuti ukhutiritse chilakolako cha mabere a utsikana wako.+ 22  “Choncho iwe Oholiba, Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Ndichititsa kuti amuna amene anali zibwenzi zako akuukire.+ Amenewa ndi amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo. Ine ndidzawabweretsa kuti akuukire kuchokera kumbali zonse.+ 23  Ndidzabweretsa ana aamuna a ku Babulo,+ Akasidi onse,+ amuna a ku Pekodi,+ a ku Sowa, a ku Kowa, pamodzi ndi ana aamuna a ku Asuri. Onsewa ndiwo anyamata osiririka, abwanamkubwa, atsogoleri, amuna ankhondo, amuna ochita kusankhidwa ndi okwera pamahatchi. 24  Onsewa adzabwera kudzakuukira. Anthuwo pofika, padzamveka phokoso la magaleta* ankhondo ndi la mawilo.+ Iwo adzabwera ndi khamu la anthu, atatenga zishango zazikulu, zishango zazing’ono ndi zisoti. Iwo adzakuzungulira kuti akuukire. Ndidzawapatsa mphamvu zoweruza, ndipo adzakuweruza motsatira malamulo awo.+ 25  Ndidzasonyeza ukali wanga pa iwe+ ndipo iwo adzakulanga mwaukali.+ Adzakuchotsa mphuno ndi makutu ndipo ziwalo zako zotsala adzazidula ndi lupanga. Iwo adzatenga+ ana ako aamuna ndi aakazi+ ndipo zinthu zako zotsala adzazitentha ndi moto.+ 26  Adzakuvula zovala zako+ ndi kutenga zinthu zako zokongola.+ 27  Ndithu, ine ndidzathetsa khalidwe lotayirira mwa iwe+ ndiponso uhule wako umene unachoka nawo kudziko la Iguputo.+ Sudzakwezanso maso ako kuyang’ana amuna a ku Iguputo ndipo dziko la Iguputo sudzalikumbukiranso.’ 28  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Iwe ndikupereka m’manja mwa amuna amene wadana nawo, amuna amene unawasiya chifukwa chonyansidwa nawo.+ 29  Iwo adzakulanga mwaukali ndi kukutengera zinthu zonse zimene unazipeza movutikira ndipo adzakusiya wosavala ndi wamaliseche.+ Umaliseche umene unauonetsa pochita dama, khalidwe lako lotayirira, ndi zochita zako zauhule zidzaonekera poyera.+ 30  Adzakuchitira zimenezi chifukwa chakuti wachita uhule ndi mitundu ina ya anthu+ komanso chifukwa chakuti wadziipitsa ndi mafano awo onyansa.+ 31  Iwe wayenda m’njira ya mkulu wako+ ndipo ndidzakupatsa kapu yake.’+ 32  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Udzamwa za m’kapu ya mkulu wako, kapu yaitali ndi yaikulu.+ Udzakhala chinthu choseketsa ndi chotonzedwa chifukwa m’kapumo muli zambiri.+ 33  Udzaledzera kwambiri ndi kudzazidwa ndi chisoni. Udzaledzera ndi zinthu za m’kapu ya mkulu wako Samariya, zinthu zodabwitsa kwambiri ndi zowononga. 34  Iwe udzamwa ndi kugugudiza za m’kapuyo,+ ndipo udzatafuna zidutswa za kapuyo ndi kukhadzula mabere ako.+ “Ine ndanena,” watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’ 35  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Popeza kuti wandiiwala+ ndi kundiponya kumbuyo,+ udzalangidwa chifukwa cha khalidwe lako lotayirira ndi zochita zako zauhule.’” 36  Yehova anandiuzanso kuti: “Iwe mwana wa munthu, kodi uweruza+ Ohola ndi Oholiba+ ndi kuwauza zinthu zonyansa zimene achita?+ 37  Iwo achita chigololo+ ndipo m’manja mwawo muli magazi.+ Achita chigololo ndi mafano awo onyansa.+ Kuwonjezera apo, ana anga aamuna amene anandiberekera anawaponya pamoto kuti akhale chakudya cha mafanowo.+ 38  Komanso anandichitira zinthu izi: Pa tsikulo anaipitsa+ malo anga opatulika+ ndiponso sabata langa.+ 39  Atapha ana awo aamuna ndi kuwapereka kwa mafano onyansa,+ pa tsiku lomwelo anabwera kumalo anga opatulika ndi kuwadetsa.+ Izi ndi zimene achita m’nyumba yanga.+ 40  Kuwonjezera apo, akaziwo atatumiza uthenga kwa amuna ochokera kutali, amuna amene anawatumizira uthengawo+ anabweradi.+ Iwe unasamba,+ n’kupaka zodzikongoletsera m’maso,+ ndi kuvala zodzikongoletsera kuti amuna amenewa akuone.+ 41  Kenako unakhala pabedi pako,+ patsogolo pa tebulo loyalidwa bwino.+ Patebulopo unaikapo zofukiza zanga zonunkhira+ ndi mafuta anga.+ 42  Kumeneko kunamveka phokoso la anthu amene akucheza mosaopa kanthu.+ Kuwonjezera pa amuna ambiri amene anali kubwera, panalinso zidakwa+ zochokera m’chipululu. Amuna amenewa anaveka akaziwo zibangili ndi zisoti zokongola zachifumu kumutu kwawo.+ 43  “Kenako ndinalankhula zokhudza mkazi amene anatopa chifukwa cha chigololo+ kuti, ‘Komatu apitiriza kuchita uhulewo.’+ 44  Amuna aja anapitiriza kubwera kwa iye monga mmene amuna amapitira kwa hule. Anapita kwa Ohola ndi Oholiba monga akazi akhalidwe lotayirira.+ 45  Koma amuna olungama+ ndi amene adzam’patse chiweruzo chimene amapereka kwa akazi achigololo+ komanso chimene amapereka kwa akazi okhetsa magazi.+ Pakuti iwowa ndi akazi achigololo ndipo m’manja mwawo muli magazi.+ 46  “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Kudzabwera khamu la anthu kudzawaukira+ ndi kuwasandutsa chinthu chochititsa mantha komanso chinthu choyenera kutengedwa ndi adani.+ 47  Khamu la anthulo lidzawaponya miyala+ ndi kuwapha ndi malupanga. Adzaphanso ana awo aamuna ndi aakazi+ ndi kutentha nyumba zawo.+ 48  Ndithu ine ndidzathetsa khalidwe lotayirira+ m’dzikoli+ ndipo akazi onse adzatengerapo phunziro, moti sadzachita khalidwe lotayirira ngati lanu.+ 49  Anthu amenewo adzakulangani chifukwa cha khalidwe lanu lotayirira+ komanso mudzalangidwa chifukwa cha machimo amene munachita ndi mafano anu onyansa. Anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.’”+

Mawu a M'munsi

Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.