Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 22:1-31

22  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, kodi ndiwe wokonzeka kuweruza?+ Kodi uweruza mzinda umene uli ndi mlandu wa magaziwu+ ndi kuudziwitsa zonyansa zake zonse?+  Unene kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Iwe mzinda umene ukukhetsa magazi+ kufikira nthawi yako yoweruzidwa itakwana,+ iwe mzinda umene wapanga mafano onyansa kuti udzidetse nawo,+  uli ndi mlandu wa magazi amene wakhetsa+ ndipo wadzidetsa chifukwa cha mafano onyansa amene wapanga.+ Wafupikitsa masiku a moyo wako ndipo zaka zoti ulandire chilango zafika. Choncho ndidzakusandutsa chinthu chotonzedwa pakati pa mitundu ina ya anthu ndiponso ndidzakusandutsa chinthu chimene mayiko onse adzachiseka ndi kuchikuwiza.+  Mayiko amene uli nawo pafupi ndiponso amene ali kutali ndi iwe adzakukuwiza, iwe mzinda wa dzina lodetsedwa komanso wachisokonezo chachikulu.+  Mwa iwetu muli atsogoleri+ a Isiraeli. Aliyense wa iwo akugwiritsa ntchito dzanja lake modzipereka kuti akhetse magazi.+  Anthu anyoza abambo ndi amayi awo mwa iwe.+ Mlendo wokhala mwa iwe amuchitira zinthu mwachinyengo.+ Azunza mwana wamasiye* ndi mkazi wamasiye.”’”+  “‘Iwe wanyoza malo anga oyera, ndipo wadetsa sabata langa.+  Mwa iwe muli anthu amiseche amene akukhetsa magazi.+ Iwo amadya chakudya choperekedwa nsembe kwa mafano m’mapiri.+ Achita khalidwe lotayirira mwa iwe.+ 10  Anthu avula bambo awo.+ Iwo agona ndi mkazi wodetsedwa amene akusamba.+ 11  Munthu wachita zinthu zonyansa ndi mkazi wa mnzake,+ ndipo munthu wachita khalidwe lotayirira mwa kugona ndi mkazi wa mwana wake.+ Munthu wagona ndi mlongo wake, mwana wamkazi wa bambo ake.+ 12  Anthu alandira ziphuphu kuti akhetse magazi.+ Iwe walandira chiwongoladzanja+ ndi kuchita katapira.+ Ukupeza phindu losayenera mwa kubera anzako+ mwachinyengo+ ndipo ine wandiiwala,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 13  “‘Ine ndawomba m’manja*+ chifukwa cha phindu lachinyengo limene wapeza+ komanso chifukwa cha zochita zako zokhetsa magazi zimene zili pakati pako.+ 14  Kodi mtima wako udzapitiriza kupirira,+ kapena kodi manja ako adzakhala ndi mphamvu m’masiku amene ndidzakulange?+ Ine Yehova ndanena ndipo ndidzachitapo kanthu.+ 15  Anthu ako ndidzawabalalitsira ku mitundu ina ya anthu ndipo ndidzawamwaza m’mayiko osiyanasiyana.+ Komanso ndidzachotsa zodetsa zako mwa iwe.+ 16  Ndithudi udzaipitsidwa pamaso pa mitundu ina, ndipo udzadziwa kuti ine ndine Yehova.’”+ 17  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 18  “Iwe mwana wa munthu, kwa ine a nyumba ya Isiraeli akhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo.+ Onsewo ali ngati mkuwa, tini, chitsulo ndi mtovu m’ng’anjo. Iwo akhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga siliva.+ 19  “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chifukwa chakuti nonsenu mwakhala ngati zinthu zachabechabe zotsalira poyenga zitsulo,+ ine ndikusonkhanitsani pamodzi mu Yerusalemu.+ 20  Ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu amenewa ndili wokwiya ndiponso waukali. Ndidzawasonkhanitsa ngati mmene anthu amasonkhanitsira siliva, mkuwa, chitsulo,+ mtovu ndi tini m’ng’anjo kuti zinthu zimenezi azikolezere+ moto ndi kuzisungunula.+ Choncho anthu inu ndidzakukolezerani moto ndi kukusungunulani. 21  Ndidzakusonkhanitsani pamodzi ndi kukukolezerani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo mudzasungunuka mumzindawo.+ 22  Monga mmene anthu amasungunulira siliva m’ng’anjo, inenso ndidzakusungunulani mumzindawo. Chotero inu mudzadziwa kuti ine Yehova ndakutsanulirani mkwiyo wanga.’”+ 23  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 24  “Iwe mwana wa munthu, uza dzikoli kuti, ‘Iwe ndiwe dziko limene silikuyeretsedwa. Pa tsiku limene udzadzudzulidwe mwamphamvu, mwa iwe simudzagwa mvula.+ 25  Aneneri ako akukonza chiwembu mwa iwe.+ Iwo akukhadzula anthu+ ngati mkango wobangula umene wagwira nyama.+ Akulanda anthu chuma ndi zinthu zawo zamtengo wapatali.+ Achulukitsa akazi amasiye mmenemo.+ 26  Ansembe ako aphwanya chilamulo changa modzionetsera,+ ndipo akuipitsa malo anga oyera.+ Sakusiyanitsa+ zinthu zoyera ndi zinthu wamba.+ Sanauze anthu kusiyana kwa zinthu zodetsedwa ndi zinthu zoyera.+ Anyalanyaza sabata langa+ ndipo andichitira mwano pakati pawo.+ 27  Atsogoleri a mumzindawo ali ngati mimbulu yomwe ikukhadzula nyama. Iwo akukhetsa magazi+ ndiponso kuwononga miyoyo n’cholinga chopeza phindu mwachinyengo.+ 28  Aneneri a mumzindawo apaka laimu machimo a atsogoleriwo.+ Aona masomphenya onama+ ndipo akuloserera atsogoleriwo zinthu zabodza.+ Iwo akunena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse. 29  Anthu a m’dzikolo abera anthu pochita zachinyengo+ ndiponso zauchifwamba.+ Iwo akuzunza anthu osautsika ndi osauka.+ Abera mlendo pochita zachinyengo komanso zopanda chilungamo.’+ 30  “‘Ndinafunafuna munthu pakati pawo amene angathe kukonzanso mpanda wamiyala+ ndi kuima pamalo ogumuka a mpandawo+ kuti ateteze dzikolo n’cholinga choti ine ndisaliwononge,+ koma sindinapeze aliyense. 31  Choncho ndidzawadzudzula mwamphamvu.+ Ndidzawafafaniza ndi moto wa mkwiyo wanga.+ Ndidzawalanga malinga ndi zochita zawo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “mwana wamwamuna wopanda bambo.”
Kuwomba m’manja chinali chizindikiro chosonyeza kunyoza kapena kunyogodola.