Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 21:1-32

21  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana ku Yerusalemu ndipo ulankhule+ kwa malo oyera.+ Ulosere zoipa zimene zidzachitikire dziko la Isiraeli.+  Uuze dziko la Isiraeli kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Ine ndidzakulanga.+ Ndidzasolola lupanga langa m’chimake+ ndi kupha anthu ako olungama ndiponso anthu ako oipa.+  Ndidzatulutsa lupanga langa m’chimake ndi kupha anthu onse kuchokera kum’mwera mpaka kumpoto. Ndidzachita izi kuti ndiphe anthu ako olungama ndiponso anthu ako oipa.+  Anthu onse adzadziwa kuti ine Yehova ndasolola lupanga langa m’chimake,+ ndipo sindidzalibwezeramonso.”’+  “Koma iwe mwana wa munthu, buula mwamantha.+ Ubuule pamaso pawo mowawidwa mtima.+  Ndiyeno akakufunsa kuti, ‘N’chifukwa chiyani ukubuula?’+ Uwayankhe kuti, ‘N’chifukwa cha uthenga umene ndamva.’+ Pakuti uthengawo udzafika ndithu+ ndipo mtima wa munthu aliyense udzasungunuka ndi mantha.+ Anthu onse adzazizira nkhongono. Aliyense adzataya mtima ndipo mawondo onse adzachucha madzi.*+ ‘Uthengawo ufika ndithu+ ndipo zimene ukunena zidzachitikadi,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Yehova wanena kuti: “Nena mofuula kuti, ‘Lupanga! Lupanga!+ Lupanga lanoledwa+ ndi kupukutidwa. 10  Lupanga lanoledwa pokonzekera kupha anthu. Lapukutidwa kuti linyezimire.’”’”+ “Koma kodi tilibe chifukwa chosangalalira?”+ “‘Kodi lupangalo likukana ndodo yachifumu+ ya mwana wanga,+ ngati mmene likukanira mtengo uliwonse?+ 11  “‘Wina wapereka lupangalo kuti lipukutidwe n’cholinga choti alinyamule ndi kuligwiritsa ntchito. Lupangalo lanoledwa ndi kupukutidwa kuti alipereke m’dzanja la munthu wakupha.+ 12  “‘Lira ndi kufuula+ iwe mwana wa munthu, chifukwa lupangalo laukira anthu anga.+ Laukira atsogoleri onse a Isiraeli.+ Atsogoleriwo aperekedwa kuti aphedwe ndi lupanga pamodzi ndi anthu anga.+ Chotero menya pantchafu yako chifukwa cha chisoni.+ 13  Lupangalo layesedwa kuti aone ngati lili lakuthwa.+ Kodi chidzachitike n’chiyani ngati lupangalo likukana ndodo yachifumu?+ Ndodoyo sidzapitiriza kukhalapo,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 14  “Iwe mwana wa munthu, losera ndipo uwombe m’manja.+ Unene katatu mawu akuti ‘Lupanga!’+ Limeneli ndi lupanga lopha anthu. Lupanga limeneli ndi limene lapha munthu wotchuka, ndipo lazungulira anthu.+ 15  Ndidzapha anthu ndi lupanga kuti mitima ya anthu isungunuke ndi mantha,+ komanso kuti ndidzachulukitse anthu ogonjetsedwa m’zipata zawo zonse.+ Kalanga ine! Lupangalo likunyezimira. Alipukuta kuti liphe anthu.+ 16  Iwe lupanga, sonyeza kuti ndiwe wakuthwa.+ Pita mbali ya kudzanja lamanja. Sankha malo ako. Pita mbali ya kudzanja lamanzere. Pita kulikonse kumene nkhope yako yaloza. 17  Ine ndidzawomba m’manja+ chifukwa cha ukali ndipo ndidzathetsa mkwiyo wanga.+ Ine Yehova ndanena.” 18  Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 19  “Koma iwe mwana wa munthu, konza misewu iwiri yoti lupanga la mfumu ya Babulo lidzadutsemo.+ Misewu yonseyo ichokere m’dziko limodzi. Pamsewu wopita mumzindawo, uikepo chikwangwani cholozera kumeneko.+ 20  Ukonze msewu woti lupanga lidzadutsemo pokaukira mzinda wa Raba+ wa ana a Amoni, ndi msewu wina woti lidzadutsemo pokaukira Yuda, inde pokaukira mzinda wa Yerusalemu wokhala ndi mpanda wolimba kwambiri.+ 21  Mfumu ya Babulo yaima chilili pamene panakumana misewu iwiri kuti iwombeze maula.+ Mfumuyo yagwedeza mivi, yafunsira kwa aterafi*+ ndi kuyang’ana pachiwindi cha nyama. 22  M’dzanja lake lamanja, maulawo asonyeza kuti iye apite ku Yerusalemu, kuti akaike zida zogumulira mzindawo,+ akalamule asilikali ake kuti aphe anthu, akalize chizindikiro chochenjeza,+ akaike zida zogumulira zipata za mzindawo, ndiponso kuti akamange chiunda chomenyerapo nkhondo, ndi mpanda womenyerapo nkhondo.+ 23  Kwa anthu amene anachita nawo malumbiro,+ maulawo aoneka ngati abodza.+ Mfumu ya Babuloyo yakumbukira zolakwa zawo+ kuti iwagwire ukapolo.+ 24  “Choncho Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: ‘Anthu inu, adani anu adzakugwirani chifukwa chakuti zolakwa zanu zinaululidwa ndipo munachititsa kuti zikumbukiridwe.+ Ndithu adzakugwirani chifukwa machimo anu, kapena kuti zochita zanu zauchimo zinaonekera ndipo simunaiwalidwe.’+ 25  “Koma iwe mtsogoleri+ wa Isiraeli, woipa ndi wovulazidwa koopsa,+ nthawi yafika yoti ulangidwe. Mapeto a zolakwa zako afika.+ 26  Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Chotsa nduwira* ndipo vula chisoti chachifumu.+ Zinthu zasintha tsopano.+ Kweza munthu wotsika+ ndipo tsitsa munthu wokwezeka.+ 27  Ine ndidzawononga, ndidzawononga, ndidzawononga ufumu.*+ Ufumu umenewu sudzaperekedwa kwa wina aliyense kufikira atabwera amene ali woyenerera mwalamulo kuutenga,+ ndipo ndidzaupereka kwa iye.’+ 28  “Iwe mwana wa munthu, losera kuti, ‘Izi n’zimene Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena zokhudza ana a Amoni ndi chitonzo chochokera kwa iwo.’ Unene kuti, ‘Lupanga lasololedwa kuti liphe anthu. Lapukutidwa kuti liwononge komanso kuti linyezimire,+ 29  chifukwa chakuti olosera anu anakuuzani masomphenya abodza,+ chifukwa chakuti anakulosererani zabodza, kuti mukhale pagulu la anthu ophedwa, anthu oipa amene tsiku lawo loti alangidwe lafika. Mapeto a zolakwa zawo zonse afika.+ 30  Bwezerani lupanga m’chimake. Ndidzakuweruzirani kwanu, m’dziko limene munachokera.+ 31  Ndidzakudzudzulani mwamphamvu. Ndidzakupemererani moto wa mkwiyo wanga,+ ndipo ndidzakuperekani m’manja mwa anthu osaganiza bwino, akatswiri odziwa kuwononga.+ 32  Mudzakhala ngati nkhuni pamoto.+ Magazi anu adzayenderera m’dzikolo. Inu simudzakumbukiridwanso, pakuti ine Yehova ndanena.’”+

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti adzakodzedwa chifukwa cha mantha.
Onani mawu a m’munsi pa Ge 31:19.
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “chisoti chachifumu.”