Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti | BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ezekieli 20:1-49

20  M’chaka cha 7, m’mwezi wachisanu, pa tsiku la 10 la mweziwo, akuluakulu a Isiraeli anabwera kwa ine kudzafunsira kwa Yehova,+ ndipo anakhala pamaso panga.+  Ndiyeno Yehova analankhula nane kuti:  “Iwe mwana wa munthu, lankhula ndi akuluakulu a Isiraeliwo ndipo uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi amuna inu mwabweradi kudzafunsira kwa ine?+ ‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti inu mufunsire kwa ine,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.”’  “Kodi ndiwe wokonzeka kuwaweruza? Kodi uwaweruza, iwe mwana wa munthu?+ Auze zinthu zonyansa zimene makolo awo anachita.+  Uwauze kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Pa tsiku limene ndinasankha Isiraeli, ndinakweza mkono wanga+ polumbirira mbewu ya nyumba ya Yakobo ndi kuwachititsa kuti andidziwe m’dziko la Iguputo. Inde, ndinakweza mkono wanga ndi kuwalumbirira kuti, ‘Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’  Pa tsiku limenelo ndinakweza dzanja langa+ powalumbirira kuti ndidzawatulutsa m’dziko la Iguputo kupita nawo kudziko limene ndinaliyendera kuti iwo akakhalemo, dziko loyenda mkaka ndi uchi. Linali dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse.+  Ine ndinawauza kuti, ‘Aliyense wa inu ataye zinthu zake zonyansa zimene amaziyang’anitsitsa pozilambira ndipo musadziipitse ndi mafano onyansa a ku Iguputo. Ine ndine Yehova Mulungu wanu.’  “‘“Koma iwo anayamba kundipandukira ndipo sanafune kundimvera. Aliyense wa iwo sanataye zinthu zonyansa zimene anali kuziyang’anitsitsa pozilambira ndipo sanasiye mafano onyansa a ku Iguputo. Choncho ine ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga kuti ukali wanga uthere pa iwo m’dziko la Iguputo.+  Koma ine ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina amene iwo anali kukhala pakati pawo, pakuti ndinawachititsa kuti andidziwe pamaso pa anthu a mitundu inawo powatulutsa m’dziko la Iguputo. 10  Chotero ndinawatulutsa m’dziko la Iguputo ndi kuwalowetsa m’chipululu. 11  “‘“Kumeneko ndinawapatsa malamulo ndi kuwadziwitsa zigamulo zanga, kuti munthu amene akuzitsatira akhalebe ndi moyo. 12  Ndinawapatsanso sabata langa kuti likhale chizindikiro pakati pa ine ndi iwowo. Ndinachita zimenezi n’cholinga choti adziwe kuti ine Yehova, ndiye amene ndikuwapatula. 13  “‘“Koma iwowo, a nyumba ya Isiraeli, anandipandukira m’chipululu. Iwo sanayende motsatira malamulo anga ndipo anakana zigamulo zanga zimene munthu akamazitsatira, amakhala ndi moyo.+ Sabata langa analidetsa kwambiri,+ moti ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga m’chipululu kuti ndiwafafanize. 14  Koma ndinachita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa mitundu ya anthu amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo. 15  Ine ndinakweza dzanja langa powalumbirira m’chipululu kuti sindidzawalowetsa m’dziko limene ndinawapatsa, dziko loyenda mkaka ndi uchi, (dziko lokongola kwambiri kuposa mayiko onse)+ 16  chifukwa anakana zigamulo zanga, sanayende motsatira malamulo anga, anadetsa sabata langa komanso mtima wawo unali pa mafano awo onyansa. 17  “‘“Maso anga anayamba kuwamvera chisoni kuti ndisawawononge, chotero sindinawafafanize m’chipululu. 18  Choncho ndinauza ana awo m’chipululu kuti, ‘Musayende motsatira malamulo a makolo anu,+ ndipo musasunge zigamulo zawo.+ Musadziipitse ndi mafano awo onyansa.+ 19  Ine ndine Yehova Mulungu wanu. Yendani motsatira malamulo anga ndipo musunge zigamulo zanga ndi kuzitsatira. 20  Muzisunga sabata langa kuti likhale lopatulika+ ndipo likhale chizindikiro pakati pa ine ndi inu, kuti mudziwe kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu.’ 21  “‘“Koma anawo anayamba kundipandukira. Sanayende motsatira malamulo anga ndipo sanasunge ndi kutsatira zigamulo zanga, zimene ngati munthu atazitsatira angakhale ndi moyo.+ Iwo anadetsa sabata langa,+ choncho ndinatsimikiza mtima kuwatsanulira mkwiyo wanga, kuti ukali wanga uthere pa iwo m’chipululu. 22  Ine ndinabweza dzanja langa+ ndi kuchita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa mitundu ya anthu amene anaona ndikutulutsa anthu anga pakati pawo.+ 23  Komanso ndinakweza dzanja langa powalumbirira m’chipululu, kuti ndidzawabalalitsira ku mitundu ya anthu ndi kuwamwazira m’mayiko osiyanasiyana, 24  chifukwa chakuti sanatsatire zigamulo zanga, anakana malamulo anga, anadetsa sabata langa+ komanso maso awo anali pa mafano onyansa a makolo awo.+ 25  Chifukwa cha zimenezi ine ndinawalola kutsatira malamulo oipa ndi zigamulo zimene sizikanawathandiza kukhala ndi moyo.+ 26  Ndinawalola kudziipitsa ndi mphatso zawo pamene anali kuponya pamoto* mwana aliyense woyamba kubadwa. Ndinachita zimenezi kuti ndiwasautse n’cholinga choti adziwe kuti ine ndine Yehova.”’+ 27  “Choncho iwe mwana wa munthu, lankhula ndi nyumba ya Isiraeli ndipo uwauze kuti,+ ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Makolo anu anandilankhulira mawu onyoza pamene anali kundichitira zinthu mosakhulupirika.+ 28  Komabe ine ndinawalowetsa m’dziko limene ndinawalumbirira nditakweza dzanja langa kuti ndidzawapatsa.+ Koma ataona phiri lililonse lalitali ndi mtengo uliwonse wanthambi zambiri, anayamba kupereka nsembe zawo pamenepo+ ndi zopereka zawo zochititsa mseru. Analinso kufukiza nsembe zafungo lokhazika mtima pansi+ ndi kuthira nsembe zawo zachakumwa pamalo amenewo.+ 29  Choncho ndinawafunsa kuti, ‘Kodi malo okwezekawa ndi a chiyani? Kodi mumachitako chiyani kumeneko kuti malowo azitchedwa kuti Malo Okwezeka mpaka lero?’”’+ 30  “Tsopano uza nyumba ya Isiraeli kuti, ‘Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Kodi anthu inu mukudziipitsa potsatira njira za makolo anu? Kodi mukutsatira zinthu zawo zonyansa ndi kuchita zachiwerewere ndi mafano amenewo? 31  Kodi mukudziipitsa polemekeza mafano anu onse onyansa mpaka lero, popereka mphatso zanu mwa kuponya pamoto ana anu aamuna? Kodi pa nthawi imodzimodziyo ndilole kuti mufunsire kwa ine, inu anthu a nyumba ya Isiraeli?”’ “‘Pali ine Mulungu wamoyo, sindilola kuti mufunsire kwa ine,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 32  ‘Ndithu zimene mukuganiza+ sizichitika.+ Inu mukunena kuti: “Tiyeni tikhale ngati anthu a mitundu ina. Tikhale ngati mabanja a m’mayiko ena+ potumikira mitengo ndi miyala.”’” 33  “‘Pali ine Mulungu wamoyo,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, ‘ndidzakhala mfumu yanu ndipo ndidzakulamulirani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula+ ndi mkwiyo wosefukira.+ 34  Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ya anthu ndipo ndidzakusonkhanitsani pamodzi kuchokera kumayiko amene munabalalikirako. Ndidzakusonkhanitsani ndi dzanja lamphamvu, mkono wotambasula ndi mkwiyo wosefukira.+ 35  Ndidzakulowetsani m’chipululu cha mitundu ya anthu+ ndipo kumeneko ndidzatsutsana nanu pamasom’pamaso.+ 36  “‘Monga mmene ndinatsutsirana ndi makolo anu m’chipululu cha dziko la Iguputo,+ ndidzatsutsananso ndi inu,’ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. 37  ‘Ndidzakudutsitsani pansi pa ndodo ya m’busa ndi kuchita nanu pangano lolimba.+ 38  Ndidzachotsa pakati panu anthu ondipandukira ndi ondichimwira. Pakuti ndidzawatulutsa m’dziko limene akukhalamo monga alendo, koma sadzalowa m’dziko la Isiraeli,+ ndipo anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.’+ 39  “Inu a nyumba ya Isiraeli, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti, ‘Pitani, aliyense wa inu akatumikire mafano ake onyansawo. Pambuyo pake, ngati simundimvera ndidzakusiyani ndipo simudzadetsanso dzina langa loyera ndi mphatso zanu ndiponso mafano anu onyansa.’+ 40  “‘Nyumba yonse ya Isiraeli idzanditumikira m’phiri langa loyera,+ phiri lalitali la m’dziko la Isiraeli,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa. ‘Kumeneko ndidzasangalala nawo ndipo ndidzafuna zopereka zanu ndi nsembe zanu za zinthu zoyambirira kucha pa zinthu zanu zonse zopatulika.+ 41  Ndikadzakutulutsani pakati pa anthu a mitundu ina ndi kukusonkhanitsani pamodzi kuchokera m’mayiko osiyanasiyana kumene munabalalikira,+ ndidzasangalala nanu chifukwa cha nsembe zanu zafungo lokhazika mtima pansi, ndipo ndidzakhala woyera chifukwa cha inu pamaso pa anthu a mitundu ina.’+ 42  “‘Ndikadzakulowetsani m’dziko la Isiraeli,+ dziko limene ndinalumbira nditakweza dzanja kuti ndidzalipereka kwa makolo anu, anthu inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ 43  Ndithu kumeneko mudzakumbukira njira zanu ndi zochita zanu zonse zimene munali kudziipitsa nazo.+ Mukadzakumbukira zimenezi, mudzachita manyazi ochita kuonekera pankhope zanu chifukwa cha zoipa zonse zimene munachita.+ 44  Ndikadzachitapo kanthu chifukwa cha dzina langa,+ inu mudzadziwa kuti ine ndine Yehova.+ Inu a nyumba ya Isiraeli, ine sindidzachitapo kanthu mogwirizana ndi njira zanu zoipa kapena zochita zanu zosayenera,’+ watero Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa.” 45  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula nane kuti: 46  “Iwe mwana wa munthu, yang’ana+ ku mbali ya kum’mwera ndipo ulankhule+ mawu onena za kumeneko. Ulosere kunkhalango ya dziko la kum’mwera. 47  Uuze nkhalango ya kum’mwerayo kuti, ‘Imva mawu a Yehova. Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti: “Ine ndikukuyatsa moto. Motowo unyeketsa mtengo uliwonse wauwisi ndi mtengo uliwonse wouma.+ Malawi a motowo sadzatheka kuwazimitsa,+ ndipo nkhope zonse,* kuchokera kum’mwera mpaka kumpoto zidzapsa ndi moto.+ 48  Anthu onse adzaona kuti ine Yehova ndaiyatsa moto nkhalangoyo ndipo sudzatheka kuuzimitsa.”’” 49  Ine ndinanena kuti: “Kalanga ine, Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa! Iwo akundinena kuti, ‘Kodi si miyambi imene akunenayi?’”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “anadutsitsa pamoto.”
Kapena kuti “nthaka yonse ya dziko lapansi.”