Esitere 3:1-15

3  Pambuyo pake, Mfumu Ahasiwero analemekeza Hamani+ mwana wa Hamedata Mwagagi,+ ndipo anam’kweza+ ndi kum’patsa mpando wapamwamba kuposa akalonga ena onse amene mfumuyo inali nawo.+  Choncho atumiki onse a mfumu amene anali kuchipata cha mfumu+ anali kuwerama ndi kugwadira Hamani, pakuti mfumu inali italamula kuti anthu azim’chitira zimenezi. Koma Moredekai sanali kumuweramira kapena kumugwadira.+  Ndiyeno atumiki a mfumu amene anali kuchipatako anayamba kufunsa Moredekai kuti: “N’chifukwa chiyani ukunyalanyaza lamulo la mfumu?”+  Popeza kuti anali kulankhula naye tsiku ndi tsiku koma sanali kuwamvera, anthuwo anakauza Hamani kuti aone ngati Moredekai angapitirize zimene anali kuchitazo,+ pakuti anawauza kuti anali Myuda.+  Hamani anakwiya kwambiri+ chifukwa anaona kuti Moredekai sanali kumuweramira ndi kumugwadira.+  Koma Hamani anaona kuti n’zosakwanira kupha Moredekai yekha pakuti anthu anamuuza za anthu a mtundu wa Moredekai. Choncho Hamani anayamba kufunafuna kufafaniza+ Ayuda onse, anthu a mtundu wa Moredekai amene anali mu ufumu wonse wa Ahasiwero.+  Ndiyeno m’mwezi woyamba,+ umene ndi mwezi wa Nisani,* m’chaka cha 12+ cha Mfumu Ahasiwero, munthu wina anachita Puri*+ kapena kuti Maere+ pamaso pa Hamani kuti adziwe tsiku ndi mwezi woyenerera. Choncho Maerewo anagwera mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara.*+  Kenako Hamani anauza Mfumu Ahasiwero kuti: “Pali mtundu wina wa anthu umene ukupezeka paliponse+ ndipo ukudzipatula pakati pa anthu m’zigawo zonse za ufumu wanu.+ Malamulo awo ndi osiyana ndi malamulo a anthu ena onse ndipo sakutsatira+ malamulo anu mfumu. Choncho si bwino kuti inu mfumu muwalekerere anthu amenewa.  Ngati zingakukomereni mfumu, palembedwe makalata kuti anthu amenewa awonongedwe. Ine ndidzapereka matalente 10,000+ asiliva kwa anthu amene adzagwira ntchito imeneyi+ kuti abweretse matalentewo mosungiramo chuma cha mfumu.” 10  Pamenepo mfumu inavula mphete yodindira+ kudzanja lake ndi kuipereka kwa Hamani+ mwana wa Hamedata Mwagagi,+ amene anali kudana kwambiri ndi Ayuda.+ 11  Ndiyeno mfumu inauza Hamani kuti: “Siliva+ akhale wako, pamodzinso ndi anthuwa ndipo uchite nawo zimene ukuona kuti n’zabwino.”+ 12  Kenako anaitana alembi a mfumu+ m’mwezi woyamba, pa tsiku la 13 la mweziwo. Ndipo alembiwo analemba+ zonse zimene Hamani analamula masatarapi* a mfumu, abwanamkubwa a m’zigawo zosiyanasiyana+ za ufumuwo ndi akalonga a anthu osiyanasiyana m’chigawo chilichonse. Makalata amenewa anawalemba malinga ndi mmene anthu a m’chigawo chilichonse anali kulembera+ ndiponso m’chinenero chawo. Makalatawa anawalemba m’dzina+ la Mfumu Ahasiwero ndipo anawadinda ndi mphete yake yodindira.+ 13  Ndiyeno anatumiza makalatawo kudzera mwa amtokoma+ kupita kuzigawo zonse za mfumu. Anachita izi kuti pa tsiku limodzi,+ pa tsiku la 13 la mwezi wa 12 umene ndi mwezi wa Adara,+ awononge, aphe ndi kufafaniza Ayuda onse, mnyamata komanso mwamuna wachikulire, ana ndi akazi ndi kufunkha zinthu zawo.+ 14  Zimene analemba m’makalatawo kuti zikhale lamulo+ kuzigawo zonse,+ anazifalitsa kwa anthu a mitundu yonse kuti akonzekere tsiku limeneli. 15  Amtokomawo anapita mofulumira+ chifukwa cha mawu a mfumu ndi lamulo limene linaperekedwa m’nyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.+ Ndipo mfumu ndi Hamani, anakhala pansi kuti amwe vinyo,+ koma mumzinda wa Susani+ munali chipwirikiti.+

Mawu a M'munsi

Onani Zakumapeto 13.
Mawu akuti “Puri” amatanthauza “Maere.” Apa ndi pamene panachokera dzina la mwambo wachiyuda wa “Purimu,” wochitika m’mwezi wa 12 pakalendala yopatulika. Onani Zakumapeto 13.
Onani Zakumapeto 13.
Onani mawu a m’munsi pa Eza 8:36.