Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 6:1-30

6  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Tsopano uona zimene ndichite kwa Farao.+ Chifukwa cha dzanja lamphamvu, iye awalola kuchoka, ndipo chifukwa cha dzanja lamphamvu awatulutsa m’dziko lake.”+  Mulungu ananenanso kwa Mose kuti: “Ine ndine Yehova.+  Ndinali kuonekera kwa Abulahamu,+ Isaki+ ndi Yakobo+ monga Mulungu Wamphamvuyonse.+ Koma za dzina langa lakuti Yehova,+ ine sindinadzidziwikitse+ kwa iwo.  Ndinakhazikitsa pangano langa ndi iwo kuti ndidzawapatsa dziko la Kanani, dziko limene anali kukhalamo monga alendo.+  Motero ineyo ndamva kubuula kwa ana a Isiraeli,+ amene Aiguputo akuwagwiritsa ntchito yaukapolo, ndipo ndikukumbukira pangano langa.+  “Choncho uwauze ana a Isiraeli kuti, ‘Ine ndine Yehova. Ndithu, ndidzakutulutsani mu Iguputo ndi kukuchotserani goli lawo, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wawo.+ Ndidzakuwombolani ndi dzanja langa lotambasula komanso ndi ziweruzo zamphamvu.+  Chotero ndidzakutengani kukhala anthu anga,+ ndi kukusonyezani kuti ndine Mulungu.+ Inuyo mudzadziwadi kuti ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndidzakutulutsani mu Iguputo, ndi kukuchotserani goli lawo.+  Ine ndidzakulowetsani m’dziko limene ndinalumbirira+ Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, nditakweza dzanja langa. Ndidzakupatsani dzikolo kukhala lanu.+ Ine ndine Yehova.’”+  Kenako Mose analankhula mawu amenewa kwa ana a Isiraeli, koma iwo sanamvere Mose chifukwa chokhumudwa ndiponso chifukwa cha ntchito yowawa ya ukapolo.+ 10  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: 11  “Pita kwa Farao, mfumu ya Iguputo,+ ukamuuze kuti alole ana a Isiraeli kutuluka m’dziko lake.”+ 12  Koma Mose anayankha Yehova kuti: “Komatu ana a Isiraeli sanandimvere,+ nanga Farao akandimvera bwanji?+ Pakuti ndimalankhula movutikira.”*+ 13  Koma Yehova anapitirizabe kuuza Mose ndi Aroni, kuti apereke lamulo kwa ana a Isiraeli ndi kwa Farao, mfumu ya Iguputo, kuti atulutse ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo.+ 14  Tsopano awa ndiwo atsogoleri a nyumba ya makolo a Aisiraeli. Ana aamuna a Rubeni, yemwe anali mwana woyamba kubadwa wa Isiraeli,+ anali Hanoki, Palu, Hezironi ndi Karami.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Rubeni.+ 15  Ndipo ana aamuna a Simiyoni anali Yemueli, Yamini, Ohadi, Yakini, Zohari ndi Shauli, mwana amene anabereka ndi mkazi wachikanani.+ Amenewa ndiwo mabanja a fuko la Simiyoni.+ 16  Awa ndi mayina a ana aamuna a Levi,+ malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo:+ Gerisoni, Kohati ndi Merari.+ Ndipo Levi anakhala ndi moyo zaka 137. 17  Ana a Gerisoni anali Libini ndi Simeyi,+ malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+ 18  Ndipo ana a Kohati anali Amuramu, Izara, Heburoni ndi Uziyeli.+ Kohati anakhala ndi moyo zaka 133. 19  Ndipo ana aamuna a Merari anali Mali ndi Musi.+ Amenewa ndiwo anali mabanja a Alevi malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+ 20  Tsopano Amuramu anatenga Yokebedi, mlongo wa bambo ake, kukhala mkazi wake.+ Ndipo Yokebedi anam’berekera Amuramu, Aroni ndi Mose.+ Amuramu anakhala ndi moyo zaka 137. 21  Ndipo ana aamuna a Izara anali Kora,+ Nefegi ndi Zikiri. 22  Ndipo ana aamuna a Uziyeli anali Misayeli, Elizafana ndi Sitiri.+ 23  Aroni anatenga Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wake wa Naasoni,+ kukhala mkazi wake. Ndipo Eliseba anam’berekera Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.+ 24  Ndipo ana aamuna a Kora anali Asiri, Elikana ndi Abiasafu.+ Amenewa ndiwo anali mabanja a Kora.+ 25  Ndipo Eleazara mwana wa Aroni,+ anatenga mwana wamkazi wa Putieli kukhala mkazi wake. Ndipo iye anam’berekera Pinihasi.+ Amenewa ndiwo atsogoleri a mabanja a m’fuko la Levi, malinga ndi mzere wobadwira wa makolo awo.+ 26  Umenewu ndiwo mzere wa Aroni ndi Mose, amene Yehova anawauza kuti:+ “Tulutsani ana a Isiraeli m’dziko la Iguputo malinga ndi makamu awo.”+ 27  Mose ndi Aroni amenewa ndi amene analankhula kwa Farao mfumu ya Iguputo, kuti atulutse ana a Isiraeli mu Iguputo.+ 28  Choncho pa tsiku limene Yehova analankhula ndi Mose m’dziko la Iguputo,+ 29  Yehova anamuuza kuti: “Ine ndine Yehova.+ Zonse zimene ndikukuuza, ukauze Farao mfumu ya Iguputo.” 30  Pamenepo Mose anauza Yehova kuti: “Komatu ndimalankhula movutikira, ndiye Farao akandimvera bwanji?”+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Ndine wosadulidwa milomo,” ngati kuti milomo yake inali ndi khungu lolendewera, moti inali yaitali kwambiri ndi yochindikala, yomulepheretsa kulankhula bwinobwino.