Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 5:1-23

5  Kenako Mose ndi Aroni anapita kwa Farao ndi kumuuza kuti:+ “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lolani anthu anga apite m’chipululu kuti akachite chikondwerero.’”+  Koma Farao anati: “Yehova ndani+ kuti ndimvere mawu ake, ndi kulola Aisiraeli kuti apite?+ Ine sindikum’dziwa Yehova ngakhale pang’ono,+ komanso, sindilola kuti Aisiraeli apite.”+  Koma iwo anati: “Mulungu wa Aheberi walankhula nafe.+ Chotero mutilole chonde, tipite ulendo wamasiku atatu m’chipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.+ Ngati sititero, adzatipha ndi mliri kapena lupanga.”+  Pamenepo mfumu ya Iguputo inawauza kuti: “N’chifukwa chiyani iwe Mose ndi Aroni mukufuna kuti anthu asiye ntchito zawo?+ Bwererani ku ukapolo wanu!”+  Farao anapitiriza kuti: “Anthu amenewa ndi ambiri m’dziko lino,+ ndipo inu mukufuna kuwasiyitsa ntchito yawo ya ukapolo.”+  Tsiku lomwelo Farao analamula amene anali kugwiritsa ntchito anthuwo mwankhanza, ndi akapitawo a anthuwo+ kuti:  “Anthu amenewa musawapezerenso udzu woumbira njerwa+ ngati kale. Muwasiye azikafuna okha udzu umenewo.  Komanso, muwauze kuti chiwerengero cha njerwa zofunika chikhale chakale chomwe chija. Musawachepetsere chiwerengerocho, chifukwa ayamba ulesi.+ N’chifukwa chake akulira kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Mulungu wathu!’+  Agwiritseni ntchito yakalavulagaga anthu amenewa ndipo muonetsetse kuti sakuchita ulesi ndi kumvera zabodza.”+ 10  Choncho amene anali kugwiritsa ntchito anthuwo,+ pamodzi ndi akapitawo anapita kwa Aisiraeli n’kukawauza kuti: “Mverani zimene Farao wanena, ‘Sindikupatsaninso udzu woumbira njerwa. 11  Inuyo muzikafuna nokha udzu kulikonse kumene mungaupeze, koma ntchito yanu sichepetsedwa ngakhale pang’ono.’”+ 12  Chotero, anthu anali balalabalala m’dziko lonse la Iguputo kukafuna mapesi m’malo mwa udzu. 13  Motero amene anali kuwagwiritsa ntchito aja anali kuwakakamiza+ kugwira ntchito ponena kuti: “Muzimaliza ntchito yanu. Aliyense azimaliza ntchito yake tsiku lililonse, ngati mmene munali kuchitira pamene udzu unali kupezeka.”+ 14  Kenako oyang’anira ntchito+ a Farao anamenya+ akapitawo a ana a Isiraeli amene iwo anawaika, n’kumati: “N’chifukwa chiyani dzulo ndi lero simunamalize kuumba njerwa+ zimene munauzidwa ngati mmene munali kuchitira kale?”+ 15  Zitatero akapitawo+ a ana a Isiraeli anapita kwa Farao ndi kumudandaulira kuti: “N’chifukwa chiyani atumiki anu mukuwachitira zimenezi? 16  Ife atumiki anu sitikupatsidwa udzu, koma akutiuza kuti, ‘Umbani njerwa!’ ndipo tikumenyedwa ngakhale kuti olakwa ndi anthu anu.”+ 17  Koma iye anati: “Mukuchita ulesi, mukuchita ulesi!+ N’chifukwa chake mukunena kuti, ‘Tikufuna tipite kukapereka nsembe kwa Yehova.’+ 18  Choncho pitani, katumikireni! Ngakhale kuti sakupatsani udzu, komabe chiwerengero cha njerwa zimene muziumba sichisintha.”+ 19  Pamenepo akapitawo a ana a Isiraeli anaona kuti zinthu zawaipira atamva mawu akuti:+ “Musachepetse ngakhale pang’ono chiwerengero cha njerwa zimene aliyense amaumba tsiku ndi tsiku.”+ 20  Zitatero anakumana ndi Mose ndi Aroni,+ amene anali kudikira akapitawowa kuti aonane nawo pamene amachokera kwa Farao. 21  Nthawi yomweyo iwo anati: “Yehova aone zimene mwachitazi ndipo akuweruzeni,+ chifukwa mwatinunkhitsa+ pamaso pa Farao ndi atumiki ake, moti mwawapatsa lupanga m’manja mwawo kuti atiphe.”+ 22  Pamenepo Mose anatembenukira kwa Yehova+ n’kunena kuti: “Yehova, n’chifukwa chiyani mwadzetsa zoipa pa anthu awa?+ Mwanditumiranji ine?+ 23  Kuchokera pamene ndinapita kukalankhula ndi Farao m’dzina lanu,+ iye wachitira anthu awa zinthu zoipa,+ ndipo inu simunalanditse anthu anu.”+

Mawu a M'munsi