Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 40:1-38

40  Ndiyeno Yehova analankhula ndi Mose, kuti:  “Mwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo,+ udzautse chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako.+  Mkati mwake, udzaikemo likasa la umboni+ ndi kutchinga kumene kuli Likasalo ndi nsalu.+  M’chihemacho udzaikemonso tebulo+ ndi kuikapo zinthu zake mwadongosolo. Kenako udzaikemonso choikapo nyale+ ndi kuyatsa nyale zake.+  Ndiyeno udzaike guwa lansembe lagolide la zofukiza,+ patsogolo pa likasa la umboni, ndi kuika nsalu yotchinga pakhomo la chihema chopatulika.+  “Udzaike guwa lansembe+ zopsereza patsogolo pa khomo la chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako.  Ndipo udzaike beseni pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe, ndi kuthiramo madzi.+  Kenako udzatchinge bwalo+ la chihema chopatulika ndi mpanda, ndipo pachipata cha bwalolo udzakolowekepo nsalu yake yotchinga.+  Ndiyeno udzatenge mafuta odzozera+ ndi kudzoza chihema chopatulika ndi zonse zimene zili mkati mwake.+ Motero udzachiyeretse pamodzi ndi ziwiya zake zonse kuti chikhale chopatulika. 10  Udzadzozenso guwa lansembe zopsereza ndi ziwiya zake zonse ndi kuliyeretsa.+ Pamenepo guwalo lidzakhala lopatulika kwambiri.+ 11  Ndiponso udzadzoze beseni ndi choikapo chake ndi kuliyeretsa. 12  “Kenako udzabweretse Aroni ndi ana ake pafupi ndi khomo la chihema chokumanako, ndi kuwalamula kuti asambe ndi madzi.+ 13  Ukatero, udzaveke Aroni zovala zopatulika,+ kenako um’dzoze+ ndi kumuyeretsa kuti atumikire monga wansembe wanga. 14  Ndiyeno udzatenge ana ake ndi kuwaveka mikanjo.+ 15  Ndipo udzawadzoze ngati mmene wadzozera abambo awo+ kuti atumikire monga ansembe anga. Iwo adzatumikirabe monga ansembe odzozedwa m’mibadwo yawo yonse mpaka kalekale.”+ 16  Pamenepo Mose anachita zonse monga mmene Yehova anamulamulira.+ Anachitadi momwemo. 17  Choncho m’mwezi woyamba wa chaka chachiwiri, pa tsiku loyamba la mweziwo, anautsa chihema chopatulika.+ 18  Pamene Mose anali kuutsa chihema chopatulikacho, anayala pansi zitsulo zake zamphako+ ndi kukhazikapo mafelemu.+ Ndiyeno analowetsa mitengo yake yonyamulira+ ndi kuimika mizati pamalo ake.+ 19  Atatero anayala nsalu yophimba pachihemacho+ ndi inanso yophimba+ pamwamba pake, monga mmene Yehova analamulira Mose. 20  Kenako anatenga Umboni+ ndi kuuika mu Likasa,+ ndipo analowetsa mitengo yonyamulira+ m’mbali mwa Likasalo ndi kuika chivundikiro+ pamwamba pa Likasa.+ 21  Pamenepo analowetsa Likasa m’chihema chopatulika ndi kuika nsalu yotchinga+ pamalo ake, kutchinga likasa la umboni,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 22  Ndiyeno analowetsa tebulo+ m’chihema chokumanako, n’kuliika kumbali yakumpoto ya chihemacho, kunja kwa nsalu yotchinga. 23  Kenako anasanja mkate woonetsa+ Yehova patebulopo, monga mmene Yehova analamulira Mose. 24  Atatero analowetsa choikapo nyale+ m’chihema chokumanako ndi kuchiika patsogolo pa tebulo, kumbali yakum’mwera ya chihemacho. 25  Ndipo anayatsa nyalezo+ pamaso pa Yehova, monga mmene Yehova analamulira Mose. 26  Kenako analowetsa guwa lansembe lagolide+ m’chihema chokumanako, ndi kuliika patsogolo pa nsalu yotchinga, 27  kuti azifukizirapo zofukiza zonunkhira,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 28  Atatero anakoloweka nsalu yotchinga+ pakhomo la chihema chopatulika. 29  Ndiyeno anaika guwa lansembe+ zopsereza pakhomo la chihema chopatulika, kapena kuti chihema chokumanako, kuti aziperekerapo nsembe yopsereza+ ndi nsembe yambewu, monga mmene Yehova analamulira Mose. 30  Kenako pakati pa chihema chokumanako ndi guwa lansembe anaikapo beseni n’kuthiramo madzi osamba.+ 31  Mose, Aroni ndi ana ake anali kusamba m’manja ndi m’mapazi awo pamenepo. 32  Akamalowa m’chihema chokumanako ndiponso akamapita kuguwa lansembe anali kusamba,+ monga mmene Yehova analamulira Mose. 33  Atatero anatchinga mpanda+ kuzungulira bwalo la chihema chopatulika ndi guwa lansembe, ndipo anakoloweka nsalu yotchinga pachipata cha bwalolo.+ Chotero Mose anamaliza ntchitoyo. 34  Pamenepo mtambo+ unayamba kuphimba chihema chokumanako, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza m’chihemacho. 35  Mose sanathenso kulowa m’chihema chokumanako, chifukwa mtambo+ unaphimba chihemacho ndipo munadzaza ulemerero wa Yehova.+ 36  M’zigawo zonse za ulendo wawo, mtambowo ukakwera pamwamba pa chihema chokumanako, ana a Isiraeli anali kunyamuka n’kuyamba ulendo.+ 37  Koma ukapanda kukwera, iwo sanali kunyamuka mpaka tsiku limene wakwera.+ 38  Mtambo wa Yehovawo unali kukhala pamwamba pa chihema chopatulika usana, ndipo usiku panali kukhala moto. Nyumba yonse ya Isiraeli inali kuona zimenezi m’zigawo zonse za ulendo wawo.+

Mawu a M'munsi