Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 37:1-29

37  Tsopano Bezaleli+ anapanga Likasa+ la mtengo wa mthethe, mikono iwiri ndi hafu m’litali, mkono umodzi ndi hafu m’lifupi, ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.+  Kenako analikuta ndi golide woyenga bwino mkati ndi kunja komwe, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira Likasalo.+  Ndiyeno analipangira mphete zinayi zagolide zoika pamwamba pa miyendo yake inayi. Mphete ziwiri zinali mbali imodzi, ndipo mphete zina ziwiri zinali mbali inayo.+  Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo anaikuta ndi golide.+  Mitengo yonyamulirayo anailowetsa m’mphete zam’mbali mwa Likasa zija kuti azinyamulira Likasalo.+  Kenako anapanga chivundikiro+ chagolide woyenga bwino, mikono iwiri ndi hafu m’litali, ndi mkono umodzi ndi hafu m’lifupi.+  Anapanganso akerubi awiri agolide. Anali osula ndipo anawapanga kumapeto onse awiri a chivundikirocho.+  Kerubi mmodzi anali kumbali imodzi ya chivundikirocho ndipo kerubi wina kumbali inayo. Akerubiwo anawapanga kumbali zonse ziwiri za chivundikirocho.+  Mapiko a akerubiwo anali okweza m’mwamba ndi otambasula.+ Iwo anaphimba chivundikirocho ndi mapiko awo, ndipo anakhala moyang’anizana, koma nkhope zawo zinayang’ana pachivundikirocho.+ 10  Ndiyeno anapanga tebulo la mtengo wa mthethe,+ mikono iwiri m’litali, mkono umodzi m’lifupi ndi mkono umodzi ndi hafu msinkhu wake.+ 11  Analikuta ndi golide woyenga bwino, ndipo anapanga mkombero wagolide kuzungulira tebulo lonselo.+ 12  Analipangiranso felemu, muyezo wake chikhatho* chimodzi m’lifupi mwake. Felemuli linazungulira tebulo lonse ndipo anapanga mkombero wagolide pafelemulo.+ 13  Kuwonjezera pamenepo, analipangira mphete zinayi zagolide ndi kuziika m’makona ake anayi, mmene munali miyendo yake inayi.+ 14  Mphetezo zinali pafupi ndi felemu lija kuti muzilowa mitengo yonyamulira tebulolo.+ 15  Ndiyeno anapanga mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndi kuikuta ndi golide. Mitengo imeneyi inali yonyamulira tebulolo.+ 16  Atatero anapanga ziwiya za patebulolo, mbale zake, zikho zake, mitsuko yake ndi mbale zake zolowa zoti azithirira nsembe zachakumwa. Anazipanga ndi golide woyenga bwino.+ 17  Kenako anapanga choikapo nyale+ chagolide woyenga bwino. Chimenechi chinali chosula. Choikapo nyalechi chinali ndi nthambi m’mbali mwake, ndiponso chinali ndi masamba ofunga duwa, mfundo ndi maluwa.+ 18  Choikapo nyalechi chinali ndi nthambi 6. Kumbali ina kunatuluka nthambi zitatu, ndipo kumbali inayo kunatulukanso nthambi zitatu.+ 19  Pamalo atatu a nthambi za mbali imodzi, panali masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa. Pamalo atatu a nthambi za mbali inayo, panalinso masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa. Nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyalecho zinali zotero.+ 20  Ndipo pamalo anayi a choikapo nyalecho panali masamba ofunga duwa opangidwa ngati maluwa a mtengo wa amondi, ndipo masambawo anatsatizana ndi mfundo ndi maluwa.+ 21  Mfundo imodzi inali pansi pa nthambi zake ziwiri, mfundo ina inalinso pansi pa nthambi zake ziwiri, ndipo mfundo inanso inali pansi pa nthambi zinanso ziwiri. Zinali choncho ndi nthambi 6 zotuluka m’choikapo nyale.+ 22  Choikapo nyalecho chinali ndi mfundo ndi nthambi. Chonsechi chinali chiwiya chimodzi chosula, chagolide woyenga bwino.+ 23  Ndiyeno anachipangira nyale 7, zopanira zake zozimitsira nyale ndi mbale zake zoikamo phulusa la zingwe za nyale. Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino.+ 24  Choikapo nyalecho pamodzi ndi ziwiya zake zonsezi anazipanga pogwiritsa ntchito golide woyenga bwino wolemera talente limodzi.* 25  Kenako anapanga guwa lansembe zofukiza+ la matabwa a mthethe.+ M’litali mwake linali mkono umodzi, m’lifupi mwake mkono umodzi. Mbali zake zonse zinayi zinali zofanana, ndipo msinkhu wake unali mikono iwiri. Guwalo linali ndi nyanga pamwamba pake.+ 26  Ndiyeno analikuta ndi golide woyenga bwino pamwamba pake ndi m’mbali mwake kuzungulira guwalo, komanso nyanga zake. Analipangira mkombero wagolide wozungulira guwa lonselo.+ 27  Kumbali ziwiri za guwalo anapangako mphete zagolide, ziwiri kumbali iyi ndi zinanso ziwiri kumbali inayo. Anazipanga m’munsi mwa mkombero kuti muzilowa mitengo yonyamulira guwalo.+ 28  Anapanganso mitengo yonyamulira ya mtengo wa mthethe ndipo anaikuta ndi golide.+ 29  Kuwonjezera pamenepo, anapanganso mafuta ogwiritsa ntchito pa kudzoza kopatulika,+ ndi mafuta onunkhira+ osakaniza mwaluso.

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Eks 25:25.
“Talente limodzi” linali kulemera makilogalamu pafupifupi 34.2.