Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 34:1-35

34  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo ine ndidzalemba pamiyala yosemayo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija,+ imene iwe unaswa.+  Ndipo ukonzeke kuti mawa m’mawa ukakwere m’phiri la Sinai ndi kukakhala pafupi ndi ine kumeneko, pamwamba pa phirilo.+  Koma usakwere m’phirimo ndi wina aliyense, ndipo musapezeke wina aliyense mmenemo.+ Kuwonjezera apo, nkhosa kapena ng’ombe zisadye m’tsinde mwa phirilo.”+  Chotero Mose anasemadi miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo anadzuka m’mamawa ndi kukwera m’phiri la Sinai, atanyamula miyala iwiriyo m’manja mwake, monga momwe Yehova anam’lamulira.  Pamenepo Yehova anatsika+ mumtambo ndi kuimirira pafupi ndi Mose, n’kulengeza dzina lake lakuti Yehova.+  Ndipo Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wachisomo,+ wosakwiya msanga+ ndiponso wodzaza ndi kukoma mtima kosatha+ ndi choonadi.+  Wosungira mibadwo masauzande kukoma mtima kosatha,+ wokhululukira zolakwa ndi machimo,+ koma wosalekerera konse wolakwa osam’langa.+ Wolanga ana, zidzukulu, ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+  Nthawi yomweyo, Mose anagwada n’kuweramira pansi.+  Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde, Yehova ayende nafe pakati pathu,+ chifukwa anthuwa ndi ouma khosi,+ ndipo mutikhululukire zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndi kutitenga kukhala chuma chanu.”+ 10  Poyankha Mulungu anati: “Tsopano ndichita nanu pangano ili: Ndidzachita zinthu zodabwitsa pamaso pa anthu ako onse, zinthu zimene sizinachitikepo padziko lonse lapansi kapena m’mitundu yonse.+ Ndipo anthu onse okuzungulirani adzaonadi ntchito za Yehova, chifukwa ndidzachita nanu chinthu chochititsa mantha.+ 11  “Koma inu sungani zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 12  Samalani kuti musachite pangano ndi anthu a m’dziko limene mukupitako+ kuopera kuti ungakhale msampha pakati panu.+ 13  Koma maguwa awo ansembe mukawagwetse, zipilala zawo zopatulika mukaziphwanye ndipo mizati yawo yopatulika mukaidule.+ 14  Pakuti simuyenera kugwadira mulungu wina,+ chifukwa Yehova, amene dzina lake ndi Nsanje, alidi Mulungu wansanje.*+ 15  Samalani, kuopera kuti mungachite pangano ndi anthu okhala m’dzikomo, pakuti iwo adzachita chiwerewere ndi milungu yawo+ ndi kupereka nsembe kwa milungu yawo.+ Chifukwa mukachita nawo pangano, mosakayikira wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+ 16  Kenako mudzatenga ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna,+ ndipo ana awo aakazi adzachita chiwerewere ndi milungu yawo, n’kuchititsa ana anu aamuna kuchita chiwerewere ndi milungu yawo.+ 17  “Musadzipangire milungu ya mafano opangidwa ndi chitsulo chosungunula.+ 18  “Muzisunga chikondwerero cha mkate wosafufumitsa.+ Monga momwe ndinakulamulirani, muzidya mkate wosafufumitsa masiku 7 m’mwezi wa Abibu*+ pa nthawi yoikidwiratu, chifukwa munatuluka mu Iguputo m’mwezi wa Abibu. 19  “Mwana aliyense woyamba kubadwa ndi wanga,+ ngakhalenso mwana woyamba kubadwa wa ziweto zanu zonse, ng’ombe ndi nkhosa.+ 20  Mwana woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa.+ Koma ngati simungamuwombole, muzimupha mwa kum’thyola khosi. Ndipo aliyense woyamba kubadwa mwa ana anu aamuna muzimuwombola.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa ine ali chimanjamanja.+ 21  “Muzigwira ntchito zanu kwa masiku 6, koma pa tsiku la 7 muzisunga sabata.+ M’nyengo yolima ndi m’nyengo yokolola muzisunga sabata.+ 22  “Muzichita chikondwerero cha masabata ndi tirigu woyamba kucha pa nyengo yokolola tiriguyo.+ Muzichitanso chikondwerero cha zokolola kumapeto kwa chaka.+ 23  “Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azionekera+ kwa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli. 24  Pakuti ndidzathamangitsira mitunduyo kutali ndi inu,+ ndipo ndidzakuza dera lanu.+ Palibe aliyense adzasirira dziko lanu pamene mwachoka kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka.+ 25  “Popereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chofufumitsa.+ Ndipo nsembe ya chikondwerero cha pasika isamagone mpaka m’mawa.+ 26  “Zipatso zoyamba kucha zabwino koposa+ za m’munda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+ “Musawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi wake.”+ 27  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Dzilembere mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe ndi Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+ 28  Choncho Mose anakhalabe m’phirimo ndi Yehova masiku 40, usana ndi usiku. Iye sanadye mkate kapena kumwa madzi.+ Ndipo Mulungu analemba mawu a pangano, Mawu Khumi,* pamiyala yosemayo.+ 29  Ndiyeno Mose anatsika m’phiri la Sinai atanyamula miyala iwiri ija ya Umboni m’manja mwake,+ koma iye sanadziwe kuti nkhope yake inali kuwala chifukwa anali atalankhula ndi Mulungu.+ 30  Aroni ndi ana onse a Isiraeli ataona Mose, anaona kuti nkhope yake ikuwala, ndipo anaopa kumuyandikira.+ 31  Pamenepo Mose anawaitana. Chotero Aroni ndi atsogoleri onse a khamu la Isiraeli anabwerera kwa iye, ndipo Mose anayamba kulankhula nawo. 32  Kenako ana onse a Isiraeli anamuyandikira, ndipo iye anayamba kuwauza malamulo onse amene Yehova anam’patsa paphiri la Sinai.+ 33  Mose akatha kulankhula nawo anali kuika chophimba pankhope yake.+ 34  Koma Mose akamalowa kukaonekera kwa Yehova kuti akalankhule naye, anali kuchotsa chophimbacho mpaka atatulukamo.+ Kenako anali kupita kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza zimene walamulidwa.+ 35  Ndipo ana a Isiraeli anali kuona kuti nkhope ya Mose ikuwala.+ Choncho Mose anali kuphimbanso nkhope yake mpaka atabwerera kukalankhula ndi Mulungu.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”
Onani Zakumapeto 13.
Mawu akuti “Mawu Khumi” akutanthauza mawu khumi olamula, zinthu khumi zoyenera kuchita, kapena Malamulo Khumi.