Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 31:1-18

31  Ndiyeno Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose, kuti:  “Inetu ndikuitana ndi kutchula dzina Bezaleli+ mwana wamwamuna wa Uri, mwana wa Hura wa fuko la Yuda.+  Ndipo ndidzam’patsa mzimu wa Mulungu kuti akhale wanzeru, wozindikira, wodziwa zinthu, ndi kuti akhale mmisiri waluso pa ntchito ina iliyonse.+  Ndidzam’patsa mzimuwo kutinso akhale wotha kulinganiza kapangidwe ka zinthu, kupanga zinthu zagolide, zasiliva ndi zamkuwa,+  waluso lolemba pamiyala mochita kugoba+ ndi wodziwa kupanga zinthu zina zilizonse zamatabwa.+  Ndipo inetu ndaika Oholiabu mwana wamwamuna wa Ahisama wa fuko la Dani+ kuti athandize Bezaleli. Komanso ndaika nzeru mumtima wa munthu aliyense waluso, kuti apange zonse zimene ndakulamulazi:+  chihema chokumanako,+ likasa+ la umboni, chivundikiro chimene chili pamwamba pake,+ ndi zipangizo zonse za m’chihema.  Kutinso apange tebulo ndi zipangizo zake,+ choikapo nyale chagolide woyenga bwino ndi zipangizo zake zonse,+ guwa lansembe zofukiza,+  guwa lansembe yopsereza ndi zipangizo zake zonse,+ beseni ndi choikapo chake,+ 10  zovala zosokedwa bwino ndi zovala zopatulika za Aroni wansembe, zovala za ana ake zoti azivala potumikira monga ansembe,+ 11  mafuta odzozera, ndi zofukiza zonunkhira za pamalo opatulika.+ Iwo adzapanga zonse malinga ndi zimene ndakulamula.” 12  Kenako Yehova anauzanso Mose kuti: 13  “Koma iwe uuze ana a Isiraeli kuti, ‘Muonetsetse kuti muzisunga masiku anga a sabata,+ pakuti ndi chizindikiro pakati pa ine ndi inu m’mibadwo yanu yonse, kuti mudziwe kuti ine Yehova ndakusankhani kukhala opatulika.+ 14  Muzisunga sabata chifukwa ndi lopatulika kwa inu.+ Amene walinyoza ayenera kuphedwa ndithu.+ Aliyense wogwira ntchito pa tsikuli ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake.+ 15  Muzigwira ntchito masiku 6, koma tsiku la 7 likhale sabata lopuma pa ntchito zonse.+ Limeneli ndi tsiku lopatulika kwa Yehova. Aliyense wogwira ntchito pa tsiku la sabata adzaphedwa ndithu. 16  Ana a Isiraeli azisunga sabata, ndipo azichita zimenezi m’mibadwo yawo yonse. Limeneli ndi pangano mpaka kalekale.+ 17  Chimenechi n’chizindikiro pakati pa ine ndi ana a Isiraeli mpaka kalekale,+ chifukwa m’masiku 6, Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, ndipo pa tsiku la 7 anapuma pa ntchito yake.’”+ 18  Ndiyeno atamaliza kulankhula naye paphiri la Sinai, anapatsa Mose miyala iwiri yosema ya Umboni,+ miyala yolembedwapo mawu ndi chala cha Mulungu.+

Mawu a M'munsi