Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 24:1-18

24  Choncho Mulungu anauza Mose kuti: “Kwera upite kwa Yehova, iweyo, Aroni, Nadabu, Abihu+ ndi akulu 70+ a Isiraeli, ndipo mugwade chapatali.  Mose yekha ayandikire kwa Yehova, koma enawo asayandikire. Anthu ena onse asakwere m’phiri.”+  Ndiyeno Mose anapita kwa anthu ndi kuwafotokozera mawu onse a Yehova ndi zigamulo zake zonse.+ Pamenepo anthu onse anayankhira pamodzi kuti: “Mawu onse amene Yehova wanena tidzachita.”+  Choncho Mose analemba mawu onse a Yehova.+ Ndiyeno anadzuka m’mawa kwambiri n’kumanga guwa lansembe ndi zipilala 12 zoimira mafuko 12 a Isiraeli, m’tsinde mwa phiri.+  Kenako anatuma anyamata a Isiraeli ndipo anyamatawo anapereka nsembe zopsereza komanso anapereka ng’ombe kuti zikhale nsembe zachiyanjano+ kwa Yehova.  Pamenepo Mose anatenga hafu ya magazi ndi kuwaika m’mbale zolowa,+ ndipo hafu inayo anawaza paguwa lansembe.+  Ndiyeno anatenga buku la pangano+ ndi kuwerengera anthuwo kuti amve.+ Zitatero anthuwo anati: “Zonse zimene Yehova wanena tidzachita zomwezo ndipo tidzamumvera.”+  Pamenepo Mose anatenga magaziwo ndi kuwaza anthuwo,+ ndipo anati: “Awa ndiwo magazi okhazikitsira pangano+ limene Yehova wapangana nanu mwa mawu onsewa.”  Choncho Mose, Aroni, Nadabu, Abihu ndi akulu 70 a Isiraeli anakwera m’phirimo, 10  ndipo anaona Mulungu wa Isiraeli.+ Pansi pa mapazi ake panali chinthu chooneka ngati miyala ya safiro yoyalidwa bwino, choyera ngati kumwamba.+ 11  Mulungu sanawononge atsogoleri amenewo a ana a Isiraeli,+ koma iwo anaona masomphenya a Mulungu woona+ ndipo anadya ndi kumwa.+ 12  Pamenepo Yehova anauza Mose kuti: “Kwera m’phiri muno ufike kwa ine ndi kukhala momwe muno, pakuti ndikufuna kukupatsa miyala yosema imene ndalembapo chilamulo kuti ndiphunzitse anthu.”+ 13  Choncho Mose ndi Yoswa mtumiki wake ananyamuka, ndipo Mose anakwera m’phiri la Mulungu woona.+ 14  Koma Mose anali atauza akuluwo kuti: “Tidikireni pompano mpaka titabwerako.+ Panotu muli ndi Aroni ndi Hura.+ Aliyense amene ali ndi mlandu wofuna kuweruzidwa afikire iwowa.”+ 15  Motero Mose anakwera m’phirimo, mtambo utakuta phirilo.+ 16  Ulemerero wa Yehova+ unakhalabe paphiri la Sinai,+ ndipo mtambowo unakutabe phirilo kwa masiku 6. Ndiyeno pa tsiku la 7, Mulungu anaitana Mose kuchokera mumtambowo.+ 17  Kwa ana a Isiraeli, ulemerero wa Yehova unali kuoneka ngati moto wolilima+ pamwamba pa phiri. 18  Kenako Mose analowa mumtambomo ndi kukwera m’phirimo.+ Mose anakhala mmenemo masiku 40, usana ndi usiku.+

Mawu a M'munsi