Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 18:1-27

18  Tsopano Yetero, wansembe wa ku Midiyani, apongozi ake a Mose,+ anamva zonse zimene Mulungu anachitira Mose ndi Aisiraeli, anthu a Mulungu, ndi mmene Yehova anawatulutsira ku Iguputo.+  Pamenepo Yetero, apongozi ake a Mose, anatenga Zipora, mkazi wa Mose, amene Mose anali atamutumiza kwawo,  ndipo anatenganso ana aamuna awiri+ a Zipora. Mwana wina, Mose anamutcha dzina lakuti Gerisomu,*+ ndipo anati: “Chifukwa ndine mlendo m’dziko lino.”  Ndipo mwana winayo anamutcha Eliezere,*+ ndipo anati: “Mulungu wa atate anga ndiye mthandizi wanga, pakuti anandipulumutsa kulupanga la Farao.”+  Choncho Yetero, apongozi ake a Mose, pamodzi ndi ana a Mose awiri aamuna ndi mkazi wake, anapita kwa Mose kuchipululu, kuphiri la Mulungu woona, kumene anamanga msasa.+  Ndiyeno anatumiza mawu kwa Mose, kuti: “Ine Yetero, mpongozi wako,+ ndafika pamodzi ndi mkazi wako ndi ana ako awiri.”  Nthawi yomweyo Mose anatuluka kukachingamira apongozi ake, ndipo anagwada n’kuwaweramira, kenako n’kuwapsompsona.+ Pamenepo anayamba kulonjerana ndi kufunsana za moyo. Kenako anapita kukalowa m’hema.  Motero Mose anawafotokozera apongozi akewo zonse zimene Yehova anachitira Farao ndi Iguputo chifukwa cha Isiraeli.+ Anawafotokozeranso mavuto onse amene anakumana nawo m’njira,+ ndi mmene Yehova anali kuwalanditsira.+  Yetero anasangalala kwambiri atamva zabwino zonse zimene Yehova anachitira Aisiraeli powalanditsa m’manja mwa Aiguputo.+ 10  Choncho Yetero anati: “Yehova adalitsike, iye amene anakulanditsani m’manja mwa Aiguputo ndiponso m’dzanja la Farao, amenenso analanditsa anthuwa m’manja mwa Aiguputo.+ 11  Tsopano ndadziwa kuti Yehova ndiye wamkulu kuposa milungu ina yonse.+ Zimenezi zinaoneka Aiguputo atasonyeza kudzikuza pamaso pa Aisiraeli.” 12  Pamenepo Yetero, apongozi ake a Mose, anabweretsa* nsembe yopsereza ndi nsembe zina kwa Mulungu.+ Ndipo Aroni ndi akulu onse a Isiraeli anabwera n’kudyera limodzi mkate ndi apongozi ake a Mose, pamaso pa Mulungu woona.+ 13  Pa tsiku lotsatira, Mose anakhala pansi monga mwa masiku onse kuti atumikire anthu monga woweruza,+ ndipo anthu anali kubwera ndi kuimirira pamaso pa Mose kuyambira m’mawa mpaka madzulo. 14  Pamenepo apongozi a Mose anaona zonse zimene iye anali kuchitira anthuwo. Ndiyeno anati: “Kodi anthuwa ukuchita nawo chiyani? N’chifukwa chiyani wangokhala wekha kupereka ziweruzo ndipo anthu onse ali chiimire pamaso pako kuyambira m’mawa mpaka madzulo?” 15  Mose anayankha apongozi akewo kuti: “Chifukwa anthuwa amabwera kwa ine kuti adzamve ziweruzo za Mulungu.+ 16  Akakhala ndi mlandu pakati pawo+ ayenera kubwera nawo kwa ine, ndipo ndiyenera kuwaweruza ndi kuwauza chigamulo cha Mulungu woona ndi malamulo ake.”+ 17  Pamenepo apongozi a Mose anamuuza kuti: “Imene ukutsatirayi si njira yabwino. 18  Ndithu mutopa nazo zimenezi, iwe ndi anthu amene uli nawowa, chifukwa ntchito imeneyi yakukulira kwambiri.+ Sungathe kuichita wekha.+ 19  Tsopano mvera zimene ndikufuna kukuuza.+ Ndikulangiza ndipo Mulungu adzakhala nawe.+ Iwe ukhale woimira anthuwa kwa Mulungu woona,+ ndipo ndiwe amene uzipititsa milandu kwa Mulungu woona.+ 20  Ndipo uziwaphunzitsa za malangizo ndi malamulo,+ ndi kuwauza njira imene ayenera kuyendamo, ndi ntchito imene ayenera kuchita.+ 21  Koma mwa anthu onsewa, usankhe amuna oyenerera,+ oopa Mulungu,+ okhulupirika,+ odana ndi kupeza phindu mwachinyengo.+ Amenewa uwaike kukhala otsogolera anthuwa, ndipo pakhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000,+ atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10.+ 22  Amenewa ndiwo aziweruza anthu pa nkhani iliyonse yoyenera. Ndiyeno pakakhala nkhani iliyonse yaikulu azibwera nayo kwa iwe,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza aziisamalira. Choncho amunawo athandizane nawe kunyamula mtolowu, kuti udzipeputsire ntchito.+ 23  Ukachita zimenezi, ndipo izi n’zimene Mulungu wakulamula kuchita, pamenepo udzaikwanitsa ntchitoyi komanso anthuwa adzabwerera kumahema awo mu mtendere.”+ 24  Nthawi yomweyo Mose anamvera zimene apongozi ake anamuuza ndipo anachita zonse zimene ananena.+ 25  Ndipo Mose anasankha amuna oyenerera mu Isiraeli yense ndi kuwapatsa udindo wokhala atsogoleri a anthu,+ kuti akhale atsogoleri a magulu a anthu 1,000, atsogoleri a magulu a anthu 100, atsogoleri a magulu a anthu 50 ndi atsogoleri a magulu a anthu 10. 26  Motero iwo anali kuweruza anthuwo pa nkhani iliyonse yoyenera. Nkhani yovuta anali kupita nayo kwa Mose,+ koma nkhani iliyonse yaing’ono, iwo monga oweruza anali kuisamalira. 27  Kenako Mose anaperekeza apongozi ake+ ndi kutsanzikana nawo, ndipo iwo anabwerera kwawo.

Mawu a M'munsi

Kutanthauza kuti “Ndi Mlendo Kumeneko.”
Kutanthauza kuti “Mulungu Wanga Ndi Mthandizi.”
Kapena kuti “anapereka.”