Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Ekisodo 13:1-22

13  Yehova analankhulanso ndi Mose kuti:  “Ndipatulireni mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa,* wa munthu ndi wa chiweto, pakati pa ana a Isiraeli. Ameneyu ndi wanga.”+  Chotero Mose anauza anthuwo kuti: “Muzikumbukira tsiku lino limene munatuluka mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo, chifukwa Yehova anakutulutsani mmenemo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ Choncho musadye chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+  Mukutuluka lero m’mwezi wa Abibu.*+  Ndipo Yehova akadzakulowetsani m’dziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi,+ limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani,+ pamenepo muzidzachita mwambo uwu m’mwezi uno.  Muzidzadya mikate yosafufumitsa masiku 7,+ ndipo pa tsiku la 7 limenelo muzidzachita chikondwerero kwa Yehova.+  Muzidzadya mikate yopanda chofufumitsa kwa masiku 7.+ Musamadzapezeke ndi chilichonse chokhala ndi chofufumitsa.+ Mtanda wa ufa wokanda wokhala ndi chofufumitsa usamadzapezeke pena paliponse m’dziko lanu.+  Ndiyeno pa tsiku limenelo udzauze mwana wako kuti, ‘Ndikuchita izi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira potuluka mu Iguputo.’+  Chotero mwambo umenewu uzikukumbutsani zimene zinachitikazi ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi pamphumi panu,+ kuti chilamulo cha Yehova chikhale pakamwa panu.+ Zizikhala choncho chifukwa Yehova anakutulutsani mu Iguputo ndi mphamvu ya dzanja lake.+ 10  Ndipo muzisunga lamulo ili pa nthawi yake yoikidwiratu chaka ndi chaka.+ 11  “Yehova akadzakulowetsani m’dziko la Akanani,+ monga momwe analumbirira kwa inu ndi kwa makolo anu,+ akadzakupatsani dzikolo, 12  pamenepo muzidzapereka kwa Yehova mwana aliyense woyamba kubadwa,+ ndi mwana aliyense wa ziweto zanu woyamba kubadwa.+ Chachimuna chilichonse n’cha Yehova.+ 13  Mwana aliyense woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa, koma ngati simungamuwombole, muzimupha mwa kum’thyola khosi.+ Ndipo aliyense woyamba kubadwa mwa ana anu aamuna muzimuwombola.+ 14  “Ndiyeno m’tsogolo, mwana wanu akadzakufunsani+ kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mudzamuyankhe kuti, ‘Yehova anatitulutsa ndi mphamvu ya dzanja lake mu Iguputo,+ m’nyumba ya ukapolo.+ 15  Koma Farao anaumitsa mtima wake posalola kuti ife tichoke,+ motero Yehova anapha mwana woyamba kubadwa aliyense m’dziko la Iguputo,+ kuyambira mwana woyamba kubadwa wa munthu mpaka mwana woyamba kubadwa wa nyama.+ N’chifukwa chake tikupereka nsembe kwa Yehova ana onse a nyama oyamba kubadwa,+ ndipo tikuwombola mwana woyamba kubadwa aliyense mwa ana athu.’+ 16  Mwambo umenewu ukhale ngati chizindikiro cholembedwa padzanja lanu ndi chomanga pamphumi panu,*+ chifukwa Yehova anatitulutsa mu Iguputo ndi mphamvu ya dzanja lake.”+ 17  Farao atalola kuti ana a Isiraeli apite, Mulungu sanawadutsitse m’dziko la Afilisiti ngakhale kuti kunali kufupi, pakuti Mulungu anati: “Anthu angataye mtima atakumana ndi nkhondo ndipo angabwerere ku Iguputo.”+ 18  Chotero Mulungu anachititsa ana a Isiraeli kuyenda njira yaitali yodutsa m’chipululu chapafupi ndi Nyanja Yofiira.+ Koma iwo potuluka m’dziko la Iguputo, anayenda mwa dongosolo lomenyera nkhondo.+ 19  Choncho Mose anatenga mafupa a Yosefe chifukwa Yosefe analumbiritsa ana a Isiraeli, kuti: “Ndithudi, Mulungu adzakukumbukirani,+ ndipo pochoka kuno mudzatenge mafupa anga.”+ 20  Motero ananyamuka ku Sukoti n’kukamanga msasa ku Etamu m’malire a chipululu.+ 21  Yehova anali kuyenda patsogolo pawo mumtambo woima njo ngati chipilala powatsogolera usana,+ ndipo usiku anali kuwatsogolera m’moto woima njo ngati chipilala kuti uziwaunikira, kuti apitirizebe ulendo usana ndi usiku.+ 22  Choncho mtambowo sunachoke patsogolo pa anthuwo usana, ngakhalenso motowo sunachoke usiku.+

Mawu a M'munsi

Mawu ake enieni, “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa, wotsegula mimba ya mayi aliyense.”
Onani Zakumapeto 13.
Mawu ake enieni, “pakati pa maso anu.”