Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 7:1-26

7  “Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene ukupita kukalitenga kukhala lako,+ adzakuchotsera mitundu ikuluikulu.+ Adzakuchotsera Ahiti,+ Agirigasi,+ Aamori,+ Akanani,+ Aperezi,+ Ahivi+ ndi Ayebusi,+ mitundu 7 ikuluikulu ndi yamphamvu kuposa iwe.+  Yehova Mulungu wako adzawapereka ndithu kwa iwe ndipo udzawagonjetse.+ Udzawawononge ndithu+ ndipo usadzachite nawo pangano kapena kuwakomera mtima.+  Usadzachite nawo mgwirizano wa ukwati. Usadzapereke ana ako aakazi kwa ana awo aamuna ndipo usadzatenge ana awo aakazi ndi kuwapereka kwa ana ako aamuna.+  Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatire ndipo adzatumikira ndithu milungu ina.+ Pamenepo mkwiyo wa Yehova udzakuyakirani ndipo adzakuwonongani ndithu mofulumira.+  “Koma inu mudzawachitire zotsatirazi: Mudzagwetse maguwa awo ansembe+ ndi kuphwanya zipilala zawo zopatulika.+ Mudzadule+ mizati yawo yopatulika+ ndi kutentha zifaniziro zawo zogoba.+  Pakuti ndinu anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.+ Yehova Mulungu wanu anakusankhani kuti mukhale anthu ake, chuma chake chapadera, mwa anthu onse okhala padziko lapansi.+  “Sikuti Yehova anakusonyezani chikondi ndi kukusankhani chifukwa chakuti munali ochuluka kuposa mitundu yonse,+ chifukwatu mtundu wanu unali waung’ono mwa mitundu yonse.+  Koma Yehova anakutulutsani ndi dzanja lamphamvu+ kuti akulanditseni m’nyumba yaukapolo,+ m’manja mwa Farao mfumu ya Iguputo, chifukwa chakuti Yehova anakukondani,+ komanso chifukwa chosunga lumbiro lake limene analumbirira makolo anu.+  Ndipo iwe ukudziwa bwino kuti Yehova Mulungu wako ndi Mulungu woona,+ Mulungu wokhulupirika,+ wosunga pangano+ ndiponso wosonyeza kukoma mtima kosatha kwa anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake ku mibadwo masauzande,+ 10  koma wobwezera munthu wodana ndi Mulunguyo mwa kumuwononga+ pamasom’pamaso. Sadzazengereza kuwononga munthu amene amadana ndi Mulungu. Adzam’bwezera pamasom’pamaso. 11  Uzisunga malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene ndikukupatsa lero, mwa kuzitsatira.+ 12  “Ndiyeno mukapitiriza kumvera zigamulo zimenezi ndi kuzisunga,+ Yehova Mulungu wanu adzasunga pangano+ ndi kukusonyezani kukoma mtima kosatha, zimene analumbirira makolo anu.+ 13  Ndipo adzakukondani ndithu, kukudalitsani,+ kukuchulukitsani+ ndi kudalitsa zipatso za mimba yanu+ ndi zipatso za nthaka yanu.+ Adzadalitsa mbewu zanu, vinyo wanu watsopano ndi mafuta anu, ana a ng’ombe zanu ndi ana a nkhosa zanu,+ m’dziko limene analumbirira makolo anu kuti adzakupatsani.+ 14  Inu mudzakhala odalitsika mwa anthu onse.+ Pakati panu sipadzapezeka mwamuna, mkazi kapena chiweto chosabereka.+ 15  Yehova adzakuchotserani matenda onse. Ndipo sadzakugwetserani matenda onse oipa a ku Iguputo amene inu mukuwadziwa,+ koma adzawagwetsera pa onse odana nanu. 16  Muwononge anthu a mitundu yonse amene Yehova Mulungu wanu akuwapereka kwa inu.+ Musawamvere chisoni+ ndipo musatumikire milungu yawo+ chifukwa kuchita zimenezo kudzakutcherani msampha.+ 17  “Ukaganiza mumtima mwako kuti, ‘Mitundu iyi yandikulira kwambiri. Ndingathe bwanji kuipitikitsa?’+ 18  Usaiope.+ Nthawi zonse uzikumbukira zimene Yehova Mulungu wako anachitira Farao ndi Iguputo yense.+ 19  Uzikumbukira mayesero aakulu amene maso ako anaona,+ zizindikiro, zozizwitsa+ ndiponso dzanja lamphamvu+ ndi mkono wotambasula+ umene Yehova Mulungu wako anakutulutsa nawo m’dzikolo.+ Umu ndi mmene Yehova Mulungu wako adzachitira ndi anthu a mitundu yonse amene ukuwaopa.+ 20  Yehova Mulungu wako adzachititsanso mantha mitima yawo+ kufikira onse otsala+ ndiponso amene anali kubisala pamaso pako atawonongedwa. 21  Usachite nawo mantha pakuti Yehova Mulungu wako, Mulungu wamphamvu ndi wochititsa mantha,+ ali pakati panu.+ 22  “Yehova Mulungu wako adzakankhira mitundu imeneyi kutali ndi iwe, kuichotsa pamaso pako pang’onopang’ono.+ Sadzakulola kuifafaniza mofulumira, kuopera kuti zilombo zakutchire zingakuchulukire ndi kukuwononga. 23  Yehova Mulungu wako adzawaperekadi kwa iwe ndi kuwabalalitsa atasokonezeka kwambiri, kufikira atawonongedwa.+ 24  Adzapereka mafumu awo m’manja mwako,+ ndipo iwe udzafafanize mayina awo padziko lapansi.+ Palibe munthu amene adzaima kutsutsana ndi iwe+ kufikira utawafafaniza.+ 25  Mudzatenthe zifaniziro zogoba za milungu yawo.+ Usadzalakelake siliva ndi golide wawo+ kapena kudzitengera zinthu zimenezi,+ kuopera kuti zingakutchere msampha,+ chifukwa zimenezi ndi zonyansa+ kwa Yehova Mulungu wako. 26  Usabweretse m’nyumba mwako zinthu zonyansa kuti iwenso ungawonongedwe mofanana ndi zinthuzo. Uzinyansidwa nazo kwambiri ndi kuipidwa nazo+ chifukwa zinthu zimenezi ndi zoyenera kuwonongedwa.+

Mawu a M'munsi