Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 6:1-25

6  “Tsopano amenewa ndiwo malamulo, malangizo ndi zigamulo zimene Yehova Mulungu wanu walamula kuti ndikuphunzitseni,+ kuti muzikazitsatira m’dziko limene mukuwolokerako kukalitenga kukhala lanu.  Muyenera kuphunzira zimenezi kuti muziopa+ Yehova Mulungu wanu, n’cholinga choti masiku onse a moyo wanu muzisunga mfundo zake ndi malamulo ake amene ndikukuuzani, inuyo, ana anu ndi zidzukulu zanu,+ ndiponso kuti masiku anu atalike.+  Ndipo inu Aisiraeli, muzimvetsera ndi kutsatira mfundo ndi malamulo ake mosamala,+ kuti zinthu zikuyendereni bwino,+ ndi kuti muchuluke kwambiri m’dziko loyenda mkaka ndi uchi, monga mmene Yehova Mulungu wa makolo anu anakulonjezerani.+  “Tamverani, Aisiraeli inu: Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.*+  Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse,+ moyo wako wonse,+ ndi mphamvu zako zonse.+  Ndipo mawu awa amene ndikukulamula lero azikhala pamtima pako,+  ndi kuwakhomereza mwa ana ako.+ Uzilankhula nawo za mawuwo ukakhala pansi m’nyumba mwako, poyenda pamsewu, pogona+ ndi podzuka.  Uziwamanga padzanja lako+ monga chizindikiro, ndipo azikhala ngati chomanga pamphumi pako,*+  ndiponso uziwalemba pafelemu la khomo la nyumba yako ndi pazipata za mzinda wanu.+ 10  “Ndiyeno Yehova Mulungu wako akadzakulowetsa m’dziko limene analumbirira makolo ako Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti adzakupatsa,+ dziko lokhala ndi mizinda ikuluikulu yooneka bwino imene sunamange ndiwe,+ 11  yokhalanso ndi nyumba zodzaza ndi zinthu zonse zabwino zimene sunaikemo ndiwe, ndi zitsime* zimene sunakumbe ndiwe, minda ya mpesa ndi mitengo ya maolivi imene sunabzale ndiwe, n’kudya ndi kukhuta,+ 12  samala kuti usaiwale+ Yehova amene anakutulutsa m’dziko la Iguputo, m’nyumba yaukapolo. 13  Uziopa Yehova Mulungu wako+ ndi kum’tumikira,+ ndipo uzilumbira pa dzina lake.+ 14  Musatsatire milungu ina, milungu iliyonse ya anthu okuzungulirani,+ 15  (pakuti Yehova Mulungu wanu amene ali pakati panu ndi Mulungu wofuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha basi).+ Musatsatire milungu ina kuopera kuti mkwiyo wa Yehova Mulungu wanu ungakuyakireni,+ ndipo angakufafanizeni padziko lapansi.+ 16  “Musamuyese, Yehova Mulungu wanu,+ mmene munamuyesera pa Masa.*+ 17  Muzionetsetsa kuti mukusunga malamulo a Yehova Mulungu wanu,+ maumboni ake+ ndi zigamulo+ zake zimene wakupatsani.+ 18  Ndipo muzichita zoyenera ndi zabwino pamaso pa Yehova kuti zikuyendereni bwino,+ ndi kuti mukalowedi m’dziko labwino limene Yehova analumbirira makolo anu,+ ndi kulitenga kukhala lanu, 19  mwa kukankhira adani anu kutali monga mmene Yehova analonjezera.+ 20  “Mwana wako akadzakufunsa tsiku lina m’tsogolo+ kuti, ‘Kodi zikumbutso, malangizo ndi zigamulo izi zimene Yehova Mulungu wathu anakupatsani, zimatanthauza chiyani?’ 21  Pamenepo mwana wakoyo udzamuyankhe kuti, ‘Tinakhala akapolo a Farao ku Iguputo, koma Yehova anatitulutsa ku Iguputoko ndi dzanja lamphamvu.+ 22  Motero Yehova anali kuchita zizindikiro ndi zozizwitsa+ zazikulu ndiponso zodzetsa masoka, mu Iguputo yense, kwa Farao ndi kwa onse a m’nyumba mwake ife tikuona.+ 23  Ndipo anatitulutsa kumeneko kuti atibweretse kuno kudzatipatsa dziko limene analumbirira makolo athu.+ 24  Choncho Yehova anatilamula kuti tizitsatira malangizo onsewa,+ tiziopa Yehova Mulungu wathu ndi kupindula nthawi zonse,+ kuti tikhale ndi moyo monga mmene zilili lero.+ 25  Ndipo tikatsatira malamulo onsewa monga mmene Yehova Mulungu wathu watilamulira,+ ndiye kuti tikuchita chilungamo+ pamaso pake.’

Mawu a M'munsi

Kapena kuti “Yehova ndi Mulungu wathu, Yehova ndi mmodzi [kapena, pali Yehova mmodzi].”  
Mawu ake enieni, “pakati pa maso ako.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Dzina lakuti “Masa” limatanthauza “Kuyesa; Mayesero.”