Zokhudza screen reader

Sankhani chinenero

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitani ku nkhani yake

Mboni za Yehova

Chichewa

Baibulo la pa Intaneti

BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA

Deuteronomo 34:1-12

34  Ndiyeno Mose anachoka m’chipululu cha Mowabu kupita m’phiri la Nebo,+ pamwamba pa Pisiga,+ moyang’anana ndi Yeriko.+ Pamenepo Yehova anayamba kumuonetsa dziko lonse, kuchokera ku Giliyadi mpaka ku Dani.+  Anamuonetsanso dziko lonse la Nafitali, dziko la Efuraimu ndi la Manase, dziko lonse la Yuda mpaka kunyanja ya kumadzulo.+  Anamuonetsa Negebu+ ndi Chigawo*+ cha Yorodano, chigwa cha ku Yeriko, mzinda wa mitengo ya kanjedza,+ mpaka ku Zowari.+  Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: “Dziko lija ndinalumbira kwa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo kuti, ‘Ndidzalipereka kwa mbewu yako’+ ndi limeneli. Ndakuonetsa kuti ulione ndi maso ako chifukwa sudzawoloka kukalowa m’dzikolo.”+  Kenako Mose mtumiki wa Yehova+ anafera pamenepo m’dziko la Mowabu, mogwirizana ndi zimene Yehova analamula.+  Iye anamuika m’manda m’chigwa, m’dziko la Mowabu moyang’anana ndi Beti-peori,+ ndipo palibe amene akudziwa manda ake kufikira lero.+  Mose anamwalira ali ndi zaka 120.+ Diso lake silinachite mdima+ ndipo anali adakali ndi mphamvu.+  Ana a Isiraeli analira Mose m’chipululu cha Mowabu masiku 30.+ Ndiyeno masiku onse olira maliro a Mose anatha.  Yoswa mwana wa Nuni anali wodzazidwa ndi mzimu wa nzeru,+ pakuti Mose anaika manja ake pa iye.+ Choncho ana a Isiraeli anayamba kumumvera ndipo iwo anayamba kuchita monga momwe Yehova analamulira Mose.+ 10  Koma mu Isiraeli simunakhalebe mneneri aliyense wofanana ndi Mose,+ amene Yehova anali kumudziwa pamasom’pamaso,+ 11  amene anachita zizindikiro ndi zozizwitsa zonse zimene Yehova anam’tuma kukachita m’dziko la Iguputo kwa Farao, kwa atumiki ake onse ndi m’dziko lake lonse.+ 12  Simunakhalebe mneneri amene anachita zinthu zazikulu ndi zoopsa ndi dzanja lake lamphamvu, ngati zimene Mose anachita pamaso pa Aisiraeli onse.+

Mawu a M'munsi

Onani mawu a m’munsi pa Ge 13:10.